Thandizo kwa Anthu Ozunzidwa
Thandizo kwa Anthu Ozunzidwa
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU DENMARK
“N’KWAPAFUPI KULUNZANITSA MAFUPA OSWEKA KUSIYANA NDI KULUNZANITSA MTIMA WOSWEKA.”—Dr. Inge Genefke.
MNYAMATA wina akuyenda mumsewu wabata mumzinda wina wa ku Ulaya ndipo akuima pa sitolo ina kuti aone katundu oonetsedwa pa zenera la sitoloyo. Mwadzidzidzi, manja ake akunjenjemera. Mawondo ake akugwedezeka. Akudzigwira pakhosi ngati kuti akufuna kutsamwa. Pazeneralo, anali ataona chithunzithunzi cha apolisi aŵiri atavala yunifolomu. Mnyamatayo sanalakwe chilichonse, ndipo panalibe chifukwa choti achitire mantha. Komabe, kungoona anthu atavala yunifolomu kunam’kumbutsa malo ena akutali makilomita zikwizikwi ndiponso zaka za m’mbuyomo pamene anali kuzunzidwa.
Zimenezi zingakhale zitachitikira ena mwa abambo, amayi, komanso ana miyandamiyanda. Mwinanso zinachitikira winawake amene mumam’dziŵa. Ozunzidwa mwankhanza ameneyu mwina ndi munthu wothaŵa kwawo kapena mlendo amene wabwera kudzakhala kwanuko. Ana ake mwina akuphunzira sukulu pamodzi ndi anu. Mwina mumamuona monga mnansi wofatsa, wochita zinthu mosamala, waulemu amene nthaŵi zambiri sakonda kucheza ndi anthu ena. Komatu maonekedwe amapusitsa; angakulepheretseni kuona kuti wovutikayo amadandaula kwambiri mumtima poyesa kuiŵala mavuto amene anavulaza thupi ndi maganizo ake. Akaona chinachake kapena kumva mawu enaake, angathe kukumbukira zoopsa zomwe anakumana nazo. Mmodzi wa anthu ozunzidwa ameneŵa ananena kuti: “Ndikangomva kulira kwa mwana, ndimaganizira za anthu omwe ndinali kuwamva akulira m’ndende. Ndikangomva mkokomo wa mphepo mlengalenga, ndimakumbukira kulira kwa chikwapu chomwe ankandimenya nacho.”
Kuzunza anthu sikuchitidwa ndi atsogoleri andale opondereza okha kapena magulu azigaŵenga okha. M’mayiko ambiri, asilikali ndi apolisi nawonso amazunza anthu. Koma kodi n’chifukwa chiyani? Kuzunza ndi njira yachidule ndiponso yothandiza yopezera chidziŵitso, kuulula zinthu, kupeza umboni wa milandu kapena kubwezera. Malinga ndi zomwe ananena Dr. Inge Genefke wa ku Denmark, amene ali katswiri wotsogola kwambiri pa nkhani za kuzunza, m’zochitika zina maboma “ayamba kulamulira ndi kukhalabe pa ulamulirowo chifukwa cha mchitidwe wa kuzunza anthu.” Munthu wina wozunzidwa anati: “Ankafuna kundipha ine kuti
anthu ena aonerepo zomwe zimakuchitikira ukadzudzula boma.”Anthu ambiri amalingalira kuti kuzunza anthu anzawo ndi chinthu chachikale choyenera nthaŵi yotchedwa Nyengo Zamdima. Ndiponsotu, mu 1948 bungwe la United Nations linavomereza Chikalata cha Mfundo Zazikulu za Ufulu Wachibadwidwe, chimene chimanena kuti: “Palibe munthu amene adzazunzidwa, kuchitidwa nkhanza, chipongwe, kunyozedwa, kapena kulangidwa mwankhanza.” (Nkhani yachisanu) Komabe, akatswiri ena akukhulupirira kuti, 35 peresenti ya anthu othaŵa kwawo azunzidwapo. Kodi n’chifukwa chiyani kuzunza anthu kwafala motere? Kodi anthu ozunzidwa amakhudzidwa motani? Nanga kodi chingachitike n’chiyani kuti athandizidwe?
Zotsatira Zake
N’zosadabwitsa kuti anthu ambiri amene amazunzidwa amathaŵa m’dziko lawo kupita kwina kukayamba moyo wina. Koma ngakhale kuti malo angasinthe, mavuto akuthupi ndiponso amaganizo amapitirizabe. Mwachitsanzo, munthuyo angamadzione ngati wolakwa chifukwa analephera kuteteza anzake kapena abale ake ku nkhanza. Komanso angasiyiretu kukhulupirira anthu ena, poopa kuti munthu aliyense amene wakumana naye angakhale ali mdani. “Munthu amene anazunzidwa amasanduka mlendo mpaka kalekale,” anatero wolemba wina dzina lake Carsten Jensen. “Iye samakhulupiriranso dziko mpaka kalekale.”
Zotsatira zake ndizo kuphatikizana kwa mavuto ovulaza thupi ndi osautsa mtima amene angasokoneze munthuyo komanso aliyense ofuna kuyesa kumuthandiza. Mavuto akuthupi nthaŵi zina angathetsedwe mwachangu, koma osati mavuto a maganizo. Dr. Genefke anavomereza kuti: “Poyamba tinkaganiza kuti ‘tidzathetsa kuvulazidwa thupi kwawo ndipo atha kubwereranso ku moyo wawo wa nthaŵi zonse,’ koma posachedwapa tatulukira kuti n’kuŵaŵidwa mtima kumene kumaŵasautsa.” Komabe, Dr. Genefke ananenanso kuti: “Zakhala zodabwitsa kudziŵa kuti n’zotheka kutonthoza ndiponso kuthandiza munthu yemwe anazunzidwa, ngakhale patapita zaka zambiri.”
Mu 1982, pa chipatala chotchedwa Copenhagen National Hospital, Dr. Genefke pamodzi ndi madokotala ena a ku Denmark anakhazikitsa chipinda chothandiziramo anthu othaŵa kwawo amene anazunzidwa. Kuyamba kwakung’ono kumeneku kunakula kufikira kukhala bungwe lapadziko lonse lodziŵika ndi dzina lakuti International Rehabilitation Council for Torture Victims (IRCT). Kuchokera ku likulu lake ku Copenhagen, bungweli likutsogolera ntchito yothandiza anthu ovutika m’madera 100 padziko lonse. M’zaka zonsezi, bungweli laphunzira zambiri pa ntchito yothandiza anthu ozunzidwa.
Mmene Mungathandizire
Kaŵirikaŵiri kumakhala kothandiza kuti wozunzidwayo alongosole zomwe zinam’chitikira. Kalata ya chidziŵitso ya bungwe la IRCT inati, “M’zaka 20 zapitazi, anthu omwe ankazunzidwa anali kuzunzika m’njira ziŵiri. Yoyamba inali kuzunzidwa mwakuthupi komanso mwamaganizo, ndipo yachiŵiri mwa kusalankhula za mavuto awo.”
N’zoona kuti sikukhala kosangalatsa kulankhula nkhani zomvetsa chisoni monga ya kuzunza anthu. Koma ngati wozunzidwayo akufuna kuuza mnzake nkhani zoterezi ndipo mnzakeyo sakufuna kumvetsera, wozunzidwayo atha kutaya chiyembekezo. Choncho, n’kofunika kuti wozunzidwa aziona zoti pali amene amasamala. Inde, si kuti munthu azifufuza nkhani zaumwini za munthu wina ayi. Motero, zili kwa wozunzidwayo kusankha ngati akufuna kuuza wina, nthaŵi yodzamuuzira, ndiponso munthu yemwe akufuna kudzamuuza.—Miyambo 17:17; 1 Atesalonika 5:14.
* Kuchita manyazi nthaŵi zambiri n’chimodzi mwa zinthu zoyamba zofunika kuzithetsa. Katswiri wina wokhazikitsa maganizo pansi anauza mayi wina yemwe anali kugwiriridwa ndi kumenyedwa kaŵirikaŵiri kuti: “Sizachilendo ndipo n’zomveka kuti umachita manyanzi. Koma zindikira kuti ukuyenera kuchita manyazi si iwe ayi. Anthu omwe anakuchita izi ndiwo ayenera kuchita manyazi.”
Akatswiri ambiri amavomereza kuganizira mbali zonse ziŵiri kuzunzika kwathupi ndi kwamaganizo. Kwa anthu ena ozunzidwa, kukhazikitsa pansi maganizo awo kumafunikira chithandizo cha akatswiri. Njira zina zachithandizo ndi monga kupuma kokoka mpweya wambiri komanso kulankhulana ndi ena.Opulumuka Kumisasa Yachibalo
M’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, anthu miyandamiyanda anazunzidwa mwankhanza yadzaoneni m’misasa yachibalo ya Hitler. Ena mwa anthu ameneŵa anali Mboni za Yehova zikwizikwi omwe ankazunzidwa chifukwa chokana kusiya zikhulupiriro zawo za chipembedzo. Mosakayikira chikhulupiriro chawo chinawathandiza kupirira m’mikhalidwe yovutayo. Kodi chinawathandiza bwanji?
Akristu ameneŵa anali ataphunzira mozama Mawu a Mulungu kalekale asanaponyedwe m’misasa ya chibaloyo. N’chifukwa chake sanali wodabwa pamene ziyeso zinabuka, ndiponso sanaimbe mlandu Mulungu ataona kuti mavuto awo sanathe msanga. Mwakuphunzira Baibulo, Mbonizo zinadziŵa chifukwa chimene Mulungu amalolera kuipa komanso mmene adzathetsere kuipaku m’nthaŵi yake yoikika. Phunziro la Baibulo lawaphunzitsa kuti Yehova “amakonda chiweruzo” [“chilungamo,” NW] ndipo kuti amakwiya pamene munthu akuzunza munthu mnzake.—Salmo 37:28; Zekariya 2:8, 9.
Ndithudi, ambiri a opulumuka kumisasa yachibalo ameneŵa anapirira zoŵaŵa zambiri zimene zinatsatirapo. Potero, iwo analimbikitsidwa kwambiri mwa kutsatira uphungu wa mtumwi Paulo. Ali mkati mwa mavuto ku ndende ya Aroma, mkhalidwe umene uyenera kuti unkam’detsa nkhaŵa kwambiri, Paulo analembera okhulupirira anzake kuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 1:13; 4:6, 7.
Pochita phunziro la Baibulo, osunga umphumphu ameneŵa adziŵa kuti Mulungu walonjeza kuti apanga dziko lapansi kukhala paradaiso, mmene zoŵaŵa za mavuto onga kuzunzidwa zidzakhala zitachotsedwa.
Mboni za Yehova zikugawana chiyembekezo chozikidwa m’Baibulo chimenechi ndi anansi awo m’mayiko oposa 230. Chifukwa cha mkhalidwe wachiwawa wadziko, iwo akumana ndi anthu amene avutika chifukwa cha nkhanza za anthu anzawo. Pamene zikumana ndi anthu omwe anazunzidwa, Mboni zimayesetsa kugaŵana ndi anthu otere lonjezo la m’Baibulo la tsogolo laulemerero. Zilidi zokondwa zedi kuti zikufalitsa uthenga watsogolo labwino pamene kuzunzidwa kudzakhala mbiri yakale!—Yesaya 65:17; Chivumbulutso 21:4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 15 Galamukani! sikulimbikitsa kutsatira njira iliyonse. Akristu ayenera kuonetsetsa kuti njira yomwe akutsatira sikutsutsana ndi malamulo a Baibulo.
[Mawu Otsindika patsamba 17]
“PALIBE MUNTHU AMENE ADZAZUNZIDWA, KUCHITIDWA NKHANZA, CHIPONGWE, KUNYOZEDWA, KAPENA KULANGIDWA MWANKHANZA.”—Nkhani yachisanu, ya m’Chikalata cha Mfundo Zazikulu za Ufulu Wachibadwidwe
[Bokosi patsamba 18]
MMENE MUNGATHANDIZIRE
NGATI MUKUDZIŴANA NDI WINAWAKE AMENE WANGOYAMBA KUIŴALA MAVUTO A KUZUNZIDWA, MALINGALIRO OTSATIRAWA ANGAKHALE OTHANDIZA:
● Sonyezani chifundo. Mwina munganene kuti: “Ndikudziŵa kuti m’dziko lomwe mukuchokera muli mavuto ambiri. Kodi mukukhala nawo bwanji?”—Mateyu 7:12; Aroma 15:1.
● Musaloŵerere kapena kukakamira kupereka thandizo. M’malo mwake, khalani wachifundo ndi woganizira ena. Lolani kuti wovutikayo adziŵe kuti muli wofunitsitsa kumvetsera.—Yakobo 1:19.
● Peŵani kukhala wothandiza monkitsa. Musanyalanyaze ulemu wa wovutikayo kapena kuloŵerera pa nkhani zaumwini. Cholinga chathu ndicho kugaŵana naye mtolo wamavuto akewo, osati kum’senzera mtolo wonsewo.