Anthu Amakono Okhala M’mapanga
Anthu Amakono Okhala M’mapanga
YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU LESOTHO
LERONSO kuli anthu okhala m’mapanga? Inde tinawapeza ena ku Lesotho, lomwe lili dziko lamapiri lolamulidwa ndi mfumu lopezeka kumwera kwa Africa. Mudzi wawo wotchedwa Ha Kome, uli pamtunda wa makilomita 60 kuchokera mumzinda wa Maseru, womwe ndi likulu la dziko la Lesotho. Mzindawu uli m’tsinde mwa mapiri aakulu zedi ndiponso ochititsa kaso otchedwa Maluti. M’miyezi ya chilimwe, zigwa za mapiri ameneŵa nthaŵi zambiri zimakhala ndi maluŵa owala, ofiira. Maluŵa okongolaŵa amadziŵika mofala ndi dzina lachingelezi lakuti red-hot pokers ndipo amachita kuti psuu pakati pa zomera zobiriŵira zomwe n’zambiri m’derali.
Kuno kuli mabanja ochulukirapo ndithu amene amakhala moyo wachikale. Iwo amamanga nyumba zawo m’kati mwa mapanga a m’zigwa za phiri. Nsichi zamitengo ndiponso zinthu zina monga tsekera n’zimene zili m’mphepete mwa khoma lolimba lakumaso kwa phanga. Khomali amalimata ndi dothi losakaniza ndi ndoŵe zang’ombe. Kumata kumeneku kumawateteza ku chisanu panyengo yozizira ya ku Lesotho imene kumazizira mpaka madzi kuundana. M’kati, muli malo ena oloŵa otchedwa ifo, kutanthauza kuti “malo osonkhapo moto,” amene amagwiranso ntchito yotenthetsa m’phangamo kukazizira.
Denga, khoma lakumbuyo, ndiponso zipupa zam’mbali nthaŵi zambiri zimakhala mwala wa phanga lomwelo. Mwala umenewu amaumata ndi dothi losakaniza ndi ndoŵe zang’ombe, ndipo amaumata chaka ndi chaka. Zimenezi zimawonjezera kukongola ndi kusalala kwa mwalawo. M’kati amakongoletsamo ndi zikopa zang’ombe, ndiponso amazigwiritsanso ntchito monga mphasa zogonapo.
Mlendo wochokera kumayiko aazungu angaone kuti moyo wachikale umenewu uli m’pena posangalatsa. Zovala zotchuka kwambiri ndizo mabulangete okongola kwabasi ndiponso zisoti zozungulira zamlaza. Nthaŵi zambiri mungaone anyamata obusa nkhosa akuyenda osavala nsapato uku akuyang’anira nkhosa zawo. Amuna a m’mudzi umenewu mungawaone akulima m’minda yawo yachimanga kapenanso ali pakati kucheza ndi amuna anzawo.
Zizindikiro za kupita patsogolo kwa sayansi yamakono zimaoneka mwa apo ndi apo. Mwakamodzikamodzi mungaone ndege yaing’ono ikuuluka mlengalenga ndiponso magalimoto otha kuyenda m’misewu yamatope akubweretsa alendo odzaona mapangawo ndipo zimenezi zimachititsa chidwi ana ndi achikulire omwe m’mudzimo. Zinthu zambiri zofunika kuphika amaphikira panja m’miphika yakuda yachitsulo ya miyendo itatu ndipo amaitereka pamoto. Chifukwa chosoŵa nkhuni, ndoŵe zang’ombe zouma, bango, ndi tisanthi pang’ono n’zimene amagwiritsa ntchito pophika. Ziŵiya zapakhomo zomwe zimapezeka kwambiri m’mapangamo ndi monga mphero yopelera chimanga ndi mthiko wotakasira phala.
Lesotho ndi dziko limene limadziŵika kwambiri chifukwa cha zojambula za anthu otchedwa ma Bushmen, zimene zimapezeka m’mapanga ambiri ndi m’miyala ya m’dziko lonselo. Ma Bushmen ndi anthu oyamba kukhala m’mapanga a Ha Kome. Zojambula zawo zimaonetsa ntchito zosiyanasiyana, monga kugwira nsomba pogwiritsa ntchito mabwato ndi maukonde, ndiponso magule adzaoneni amene ovina ake mwachionekere ankavala zikopa zanyama. Zojambulazo zimaonetsanso nyama monga anyani, mikango, mvuu ndiponso ntchefu. Panopa zojambula zambiri ku mapanga a Ha Kome zinafufutika. N’zochepa chabe zimene zatsala monga zokumbutsa luso la ma Bushmen.
Kagulu ka Mboni za Yehova kamachita ntchito yolalikira m’dera limene silili kutali kwenikweni ndi ku Ha Kome. Nthaŵi ndi nthaŵi, iwo amakacheza ndi anthu okhala m’mapangawo, amene amadziŵika kwambiri chifukwa chochereza alendo. Nthaŵi zambiri a Mboniwo amawaphikira phala lakumeneko lotchedwa motoho. Anthu ambiri a ku Ha Kome n’ngwofunitsitsa kulandira mabuku ofotokoza Baibulo. Nthaŵi zambiri amasonyeza kuyamikira mabukuwo mwa kupereka ndiwo zamasamba, mazira, kapenanso zinthu zina monga zopereka za ntchito yophunzitsa ya a Mboniwo.
Anthu okhala m’mapanga lerolinoŵa amalemekeza kwambiri Baibulo ndipo amakonda kufunsa mafunso okhudza moyo, imfa, ndiponso zikhulupiriro zawo za miyambo yakale. Ntchito ya Mboni zokangalika m’deralo yachititsa kuti mukhale maphunziro a Baibulo ambiri. Motero, mbewu za choonadi zapeza nthaka yachonde m’mitima mwa anthu odzichepetsawo.—Mateyu 13:8.
[Mapu/Chithunzi patsamba 26]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
HA KOME