Kodi Ndizimwa Asipilini Tsiku N’tsiku?
Kodi Ndizimwa Asipilini Tsiku N’tsiku?
Nkhani ino n’njonena za zinthu zimene zimachitikadi m’moyo zolongosoledwa ndi dokotala. Ikusonyeza vuto lofala kwambiri.
BANJA lonse linada nkhaŵa. Tsopano ngakhale dokotala nayenso anada nkhaŵa. Dokotalayo anati, “Ngati saleka kutuluka magazi mwamsanga tingaganize zomuika magazi.”
Munthuyo anali kutuluka magazi m’mimba pang’onopang’ono kwa masabata angapo, ndipo atamuyeza anapeza kuti vuto linali kutupa kwa chifu. Dokotalayo anafunsa mothedwa nzeru kuti, “Ukunenetsa kuti sukumwa mankhwala alionse?”
Munthuyo anati, “Inde. Ndikungomwa mankhwala aŵa amene ndinagula kusitolo chifukwa cha matenda anga amafupa otchedwa athritis.”
Dokotalayo atadzidzimuka anatchera khutu. “N’tawaona.” Anaŵerenga mosamala mawu apachikuto onena za mankhwala ena omwe anasakaniza ndi mankhwalawo, ndipo anapeza chimene anali kufuna. Mankhwala otchedwa Acetylsalicylic acid! Basi vuto linali limenelo. Pamene wodwalayo anasiya kumwa mankhwala okhala ndi asipiliniwo ndi kupatsidwa mankhwala owonjezera magazi ndi enanso a m’mimba, anasiya kutuluka magazi ndipo pang’onopang’ono magazi ake anakhala okwanira.
Kutuluka Magazi Chifukwa cha Mankhwala
Kutuluka magazi m’mimba ndi m’matumbo chifukwa cha mankhwala ndi matenda aakulu lerolino. Ngakhale kuti pali mankhwala ambiri amene angayambitse zimenezi, mavuto ambiri otereŵa amabwera chifukwa cha mankhwala a matenda amafupa otchedwa athritis ndiponso mankhwala oletsa kuwawa. Ena mwa mankhwalaŵa ndi monga gulu la mankhwala osatupitsa lotchedwa nonsteroidal anti-inflammatory drugs, kapena NSAIDS. Mayina angasiyane m’mayiko osiyanasiyana.
Asipilini ali m’mankhwala ambiri ogula kusitolo, ndipo m’mayiko ambiri anthu omwa asipilini tsiku n’tsiku achuluka m’zaka zaposachedwapa. N’chifukwa chiyani achuluka?
Kukondetsa Asipilini
Mu 1995 magazini ya za thanzi yotchedwa Harvard Health Letter inati “kugwiritsa ntchito asipilini kaŵirikaŵiri kumapulumutsa miyoyo.” Ponenapo za kufufuza kosiyanasiyana kumene kwachitika m’mayiko angapo, ndipo kwabwerezedwa kambirimbiri kuyambira pamenepo, ofufuza anapeza kuti: “Pafupifupi munthu aliyense amene anadwalako matenda a mtima kapena a sitiroko, kapena amene amadwala matenda a angina, kapena amene wachitidwako opaleshoni yosintha mitsempha ya mtima ayenera kumwa theka kapena mbulu wathunthu wa asipilini tsiku n’tsiku pokhapokha ngati mankhwalaŵa samuyanja.” *
Ofufuza ena anena kuti kumwa asipilini tsiku n’tsiku n’kwabwino kwa amuna kapenanso akazi a zaka zopitirira 50 amene angathe kudwala matenda a mtima mosavuta. Kuphatikizanso apo, pali kufufuza kosonyeza kuti kumwa asipilini tsiku n’tsiku kungachepetse tsoka la kudwala matenda a kansa ya m’matumbo akuluakulu ndiponso kumwa mlingo waukulu wa mankhwalaŵa kwa nyengo yaitali kungathandize anthu odwala matenda a shuga kuchepetsa shuga opezeka m’magazi mwawo.
Kodi asipilini amagwira bwanji ntchito kuti azitha kuthandiza m’njira imeneyi? Ngakhale kuti si zonse zimene zili zodziŵika, umboni ukusonyeza kuti asipilini amagwira ntchito yochititsa kuti zidutswa za m’magazi zikhale zosamatana kwambiri, ndipo potero amachititsa kuti magazi asaundane. Mwina izi zimapangitsa kuti mitsempha ing’onoing’ono yopita ku mtima ndi ku ubongo isatsekeke, ndipo potero ziwalo zofunika kwambirizi siziwonongedwa.
Ngati akunena kuti asipilini amathandiza m’njira zambiri chonchi, n’chifukwa chiyani si aliyense
amene amamwa? Chifukwa chimodzi n’chakuti, pali zinthu zambiri zimene sizinadziŵikebe bwinobwino. Ngakhale mlingo woyenera sukudziŵika bwino. Ena amati ndi bwino kumwa mbulu umodzi kaŵiri patsiku ndiponso ena amati koma mbulu wa ana umodzi wokha basi patsiku. Kodi mlingo wa akazi uyenera kusiyana ndi wa amuna? Madokotala sali otsimikiza. Ngakhale kuti asipilini wongomeza angakhale ngati wothandiza, nkhani yakuti asipilini wopanda asidi ameneyu n’ngwabwino idakali yovutabe.Zifukwa Zokhalira Osamala
Ngakhale kuti kunena mwatchutchutchu mankhwala a asipilini n’ngachilengedwe, moti Amwenye a ku America ankapeza mankhwala opezeka mu asipilini kuchokera m’makungwa a mtengo wamsondodzi, mankhwalaŵa amayambitsanso matenda ena ochuluka. Anthu ena amawapatsa vuto la kutuluka magazi ndipo kuphatikizanso apo asipilini angayambitsenso matenda ena ambiri, komanso matenda amene anthu ena amadwala chifukwa chosayanjana nawo. Zakuti si anthu onse amene ayenera kumwa asipilini tsiku n’tsiku n’zosachita kufunsa.
Komabe, munthu amene ali pangozi yakuti angadwale matenda a mtima kapena sitiroko kapena amene ali ndi zinthu zina zodzetsa matendaŵa angafune kufunsa dokotala wake kuti amuuze kuopsa ndiponso ubwino wa kumwa asipilini tsiku n’tsiku. Mwachidziŵikire wodwalayo angafune kutsimikiza kuti alibe vuto lililonse la kutuluka magazi, kusayanjana ndi asipilini ndiponso vuto lililonse la m’mimba ndi m’matumbo. Musanayambe kumwa mankhwalawo kambiranani ndi dokotalayo za mavuto ena amene angakhalepo kapena chithandizo china chamankhwala chimene chingalimbane ndi mankhwalaŵa.
Monga taonera kale, mankhwala a asipilini ndiponso mankhwala ena ofanana nawo angathe kubweretsa vuto la kutuluka magazi. Ndipo kutuluka magazi kumeneku kungakhale kobisika, kosaonekera msanga, ndipo kungakule pang’onopang’ono. Mankhwala enanso ayenera kugwiritsidwa ntchito mosamala, makamaka mankhwala ena oletsa kutupa. Ngati mukugwiritsa ntchito mankhwala alionse otere onetsetsani kuti dokotala wanu mwamuuza. Nthaŵi zambiri kungakhale kwanzeru kusiya kugwiritsa ntchito mankhwalawo musanakachitidwe opaleshoni. Mwinanso kuyezetsa kuchuluka kwa magazi anu pafupipafupi kungakhale kothandiza.
Ngati tikufuna kudzipulumutsa ku mavuto am’tsogolo, tiyenera kumvera mwambi wa m’Baibulo wakuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; Koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” (Miyambo 22:3) Pankhani ya mankhwalayi, tiyeni tikhale m’gulu la anthu ochenjera kuti tisalipitsidwe thanzi lathu.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Galamukani! silangiza kuti mtundu wachithandizo cha mankhwala akutiakuti ndiwo wabwino.
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 20, 21]
Kodi Ndani Angakhale Woyenera Kumamwa Asipilini Tsiku N’tsiku?
● Anthu amene ali ndi matenda a mitsempha ya mtima kapena amene mitsempha yawo yaikulu yodutsa pakhosi ili yochepa.
● Anthu amene adwalako matenda a sitiroko (odza chifukwa cha kuundana kwa magazi) kapena amene anaumako ziwalo kwakanthaŵi chifukwa choti magazi sakufika kuziwalozo.
● Amuna opitirira zaka 50 amene ali ndi chimodzi kapena zingapo mwa zinthu zotsatirazi zimene zingayambitse matenda a mtima: kusuta fodya, kuthamanga kwa mtima, matenda a shuga, kuchuluka kwa mankhwala a m’thupi otchedwa cholesterol, kuchepa kwa mankhwalaŵa mu puloteni yam’thupi yotchedwa HDL, kunenepa kwadzaoneni, uchidakwa, kapena ngati pamtundu wanu pali wina amene anadwalapo matenda a mitsempha ya mtima pamsinkhu wochepa (kapena matenda a mtima asanafike zaka 55) kapena matenda a sitiroko, ndiponso moyo wosagwira ntchito zolimba.
● Amayi a zaka zopitirira 50 okhala ndi zinthu ziŵiri kapena zingapo zatchulidwazo zimene zingayambitse matenda.
Mungafune kukambirana kaye ndi dokotala wanu musanasankhe kuchita chilichonse pankhaniyi.
[Mawu a Chithunzi]
Gwero: Consumer Reports on Health