Mtundu Wodabwitsa wa Mbalame
Mtundu Wodabwitsa wa Mbalame
PA MTUNDU wa mbalame zonse zotchedwa ma penguin, pali mtundu waukulu wotchedwa emperor womwe mbalame zake n’zazikulu kwambiri, n’zazitali kupitirira mita imodzi ndipo zingathe kulemera makilogalamu okwana 40. Mbalame zina zonse za mu mtunduwu zikamaloŵera kumpoto pothaŵa nyengo yachisanu choopsa ndiponso ya mdima ya kudera lotchedwa Antarctica, mbalame zikuluzikulu zimenezi zimaloŵera kumwera komweko—ku Antarctica! N’chifukwa chiyani zimatero? N’zodabwitsa zedi kuti zimapita kukaswa ana.
Thadzi la mbalamezi likaikira dzira, mwamsanga tambala wake amalinyamula kulichotsa pamadzi oundana n’kuliika pamapazi ake. Kenaka amaliloŵetsa m’kathumba komwe kali pamimba pake. Ndiye thadzi lija limayamba ulendo wa kunyanja kukafuna malo abwino ndi chakudya. Tambalayo amafungatira dziralo kwa masiku 65, m’nyengo yoipitsitsa, ndipo pakuti sadya chilichonse amakhala ndi moyo chifukwa cha mafuta a m’thupi mwake. Kuti zizimvabe kutentha uku zikuwombedwa ndi chimphepo chokuntha paliŵiro la makilomita 200 pa ola, mbalame zanzeru zimenezi zimaunjikana pamodzi m’magulu aakulu. Zimasinthanasinthana kukhala mumzere wakunja umene umatchinga mphepo, zitalozetsa msana kumene kukuchokera mphepo.
N’zodabwitsa kwambiri kuti dziralo limaswa mwanapiye nthaŵi imene thadzi lija likubwerera komwe linapita kuja. Koma kodi thadzilo limam’peza bwanji tambala wake pagulu la atambala zikwizikwi ofanafana? Pogwiritsa ntchito nyimbo inayake. Panthaŵi yomwe zinkatomerana, mbalame ziŵirizi zinkaimbirana kanyimbo ndipo iliyonse inaloŵeza kuimba kwa inzake. Mathadziwo akabwerako, iwo pamodzi ndi atambala aja amaimba ndi mtima wawo wonse. Anthu angasokonezeke zedi ndi phokosolo, koma mbalame zikuluzikuluzi m’pamene zimatha kupeza mabanja awo mwamsanga. Kenaka, akapereka monyinyirika mwanapiye watsopanoyo, tambala amene panthaŵiyi amakhala atafooka zedi ndi njala amayenda mwapendapenda kapenanso modzikhwekhwereza chafufumimba pamadzi oundana mtunda wamakilomita 72 pofuna madzi ndi chakudya.
[Mawu a Chithunzi patsamba 31]
Mwachilolezo cha John R. Peiniger