Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chivomezi!

Chivomezi!

Chivomezi!

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU TAIWAN

“Ndinkaŵerenga ndili chogona m’chipinda changa cha pansanjika ya chisanu ndi chinayi ya nyumba ina ku Taipei pamene magetsi anayamba kuzima pang’onopang’ono. Kenako chipindacho chinayamba kunjenjemera modetsa nkhaŵa. Zinali ngati kuti chilombo chinachake chinali chitagwira nyumbayo ndi kuyamba kuigwedeza. Ndinajoŵera kunsi kwa tebulo pamene chiphokoso cha zinthu zogwera pansi m’nyumba ya padenga chinandipangitsa mantha kuti denga likugwa. Zinkaoneka kuti zizingopitirizabe.”—Mtolankhani wokhala ku Taiwan.

CHIVOMEZI. Kungotchula mawu ameneŵa kumachititsa mantha, ndipo posachedwapa mwina munachimva chikugwedeza moŵirikiza. Malinga ndi kunena kwa U.S. Geological Survey, zivomezi zikuluzikulu zambiri zoposa zina zonse zinachitika m’chaka cha 1999, ndipo chiŵerengero cha imfa zochitika chinaŵirikiza kaŵiri avareji yapachaka.

Chivomezi chachikulu chinachitika ku Taiwan m’chaka cha 1999, kumene zigawo zikuluzikulu ziŵiri za dziko zimakumana pansi pa nthaka. Kwenikweni, pansi pa nthaka pali malo anthenya okwana 51 ku dziko la Taiwan. Ndiyetu, m’posadabwitsa kuti zivomezi zokwana 15,000 zimachitika kumeneku chaka chilichonse. Ngakhale kuti zambiri ndi zazing’ono kwambiri zoti sizidziŵika.

Koma sizinali choncho pa September 21, 1999. Pa nthaŵi ya 1:47 a.m., dziko la Taiwan linagwedezeka ndi chivomezi champhamvu moti Pulezidenti Lee Teng-hui anachitchula kukhala “choopsa kwambiri m’dzikoli kwa zaka 100.” Chinatenga masekondi 30 okha koma chinali chachikulu moti chinafika 7.6 pa sikelo ya Richter. * Kuchokera pa gwero lake pansi kufika pamwamba pa nthaka, chivomezicho chinagwedeza nthaka kupitirira pang’ono kilomita imodzi. Ndiye popeza chinachitikira pafupi m’nthaka, mphamvu yake inamveka konsekonse. “Ndinadzidzimutsidwa ndi kunjenjemera kodetsa nkhawa,” anatero Liu Xiu-Xia, amene amakhala kufupi ndi kumene kunayambira chivomezicho. Katundu wa m’nyumba anagwa, ngakhale magetsi akudenga anagwera pansi. Ndinalephera kutuluka chifukwa cha zinthu ndi magalasi zimene zinali zitagwera pa chitseko.” Huang Shu-Hong amene anadzidzimutsidwa pa bedi ndi chivomezicho, anakumananso ndi vuto lina losiyana. Iye anati: “Magetsi anazima nthaŵi yomweyo, moti kunali mdima woopsa. Ndinatuluka kunja movutika ndipo ndinakhala kunja ndi anansi mphepete mwa msewu. Sikunaoneke kuti nthaka ingasiye kunjenjemera.”

Zoyesayesa Zopulumutsa

Mbandakucha kusakaza kwa chivomezicho kunaonekera. Nyumba zokwana 12,000, kuyambira nyumba wamba mpaka zam’mwamba zosanjikizana zinali zitagwa. Pamene uthenga wangoziwo unamveka, akatswiri opulumutsa ochokera ku mayiko 23 anabwera ku Taiwan kuti adzathandize antchito odzipereka akumeneko. Anthu ambiri anali opsinjidwabe m’nyumba zakugwazo.

Maola 72 oyambirira ngozi ikachitika ndiwo amakhala opulumuka anthu, koma panthaŵiyi ogwira ntchito yopulumutsawo anaona zodabwitsa. Mwachitsanzo, mnyamata wazaka zisanu ndi chimodzi anapulumutsidwa atapsinjidwa kwa maola 87. Ndipo ku Taipei, pamene ogwira ntchitowo anali kuchotsa zowonongeka za nyumba 12 zakugwazo ndi makako, mosayembekezeka mnyamata anapezeka. Pamodzi ndi mkulu wake anali atapanikizika masiku opitirira asanu, koma onse anapulumuka ngoziyo!

Komabe, chomvetsa chisoni n’chakuti, si onse amene anapezedwa, ndipo ogwira ntchito yopulumutsayo anaona zoopsa. Mwachitsanzo, woyang’anira gulu lina anadandaula kuti: “Tinamva kulira kwa mwana kwa maola asanu ndi atatu. Koma kenaka analeka kulirako.” Pomalizira pake, chiŵerengero cha omwalira chinakwera kupitirira 2,300, ndipo anthu opitirira 8,500 anavulala.

Kulimbana ndi Mavuto Ake

Kuyesetsa kwa mphamvu kunachitidwa kuti apereke malo okhala kwa anthu miyandamiyanda amene analibe pokhala chifukwa cha chivomezicho. Poyamba, ena mwa okhudzidwa ndi ngoziwo ankachita mantha kuti akhalenso m’nyumba. Zimenezi n’zomveka, chifukwa m’kati mwa masiku khumi chitangochitika chivomezi choyambacho, kunjenjemera kwa dziko kotsatira chivomezicho kokwana 10,000 kunachitika! Chimodzi cha zimenezizo chitayesedwa pa sikelo ya Richter chinali 6.8, ndipo chinatsirizitsa nyumba zomwe zinali zitagwedera kale.

Komabe, ntchito yothandizayo inapitirira. Mabungwe angapo amene si a boma kuphatikizapo magulu ena ochokera kunja, gulu la Abuda la Tzu Chi, ndi ozimitsa moto anathera nthaŵi ndi luso kutchito yofunika imeneyi. Enanso amene anagwira nawo ntchito imeneyi yothandiza anali a Mboni za Yehova. Mwa mzimu wa Baibulo wopezeka pa Agalatiya 6:10, iwo anali ndi zolinga ziŵiri. Anafuna kuti (1) akathandize awo amene anali abale awo m’chikhulupiriro, ndiponso (2) kuti akachitire onse zabwino, kuphatikizapo anthu osiyana nawo zikhulupiriro.

Pamene tsiku loyamba limatha, Mboni za Yehova zinali kubweretsa chakudya, madzi, matenti, ndi ziŵiya zophikira panja. Ndiye popeza njira zonse zolankhulirana zinali zitawonongeka, akulu ochokera ku mipingo isanu ndi umodzi kudera langozilo anayesetsa kufufuza Mboni zinzawo ndi abale awo komanso amene amaphunzira nawo Baibulo ndi ena okondwerera. Mboni zimene zinalibe malo okhala zinalimbikitsidwa kuti zikhale malo amodzi kuti onse asamalidwe ndi kufikiridwa mosavuta. Oyang’anira oyendayenda ndi a Komiti ya Nthambi ya Taiwan anakaona gulu lililonse ndi mipingo kuti akawalimbikitse.

Ntchito yotsatira inali kukonzanso nyumba zawo ndi Nyumba za Ufumu zimene zinali zitawonongeka. Mpingo uliwonse unalemba ndandanda ya anthu ofunika thandizo. Kenako, mwa malangizo a Komiti Yomanga Yachigawo, magulu a antchito odzifunira anatumizidwa kuti akakonze mmene munali mofunikira. Patangopita mwezi chivomezicho chitachitika ntchitoyo inamalizidwa.

Mboni za Yehova zinathandizanso anansi awo omwe si a Mboni. Mwachitsanzo, Mboni zinakayendera zipatala ndi malo a misasa kuti akapereke chitonthozo. Zinagaŵiranso mafotokope a Galamuka! a nkhani yakuti “Masoka Achilengedwe—Kuthandiza Mwana Wanu Kulimbana Nawo,” yotuluka m’kope ya Galamukani! wa July 8, 1996. Anthu ambiri anayamikira kulandira uthengawo ndipo anayamba kuŵerenga mofulumira. Pamene misewu inatsekulidwa, Mboni za Yehova zinatumiza katundu wodzaza galimoto zikuluzikulu kumadera akutali amapiri amene anawonongedwa kwambiri ndi chivomezicho.

Awo amene amaphunzira Baibulo amazindikira kuti linalosera kale kuti masiku otsiriza a dongosolo ili la zinthu adzadziŵika ndi “zivomezi m’malo akuti akuti.” (Mateyu 24:7) Komanso Baibulo limatitsimikizira kuti posachedwapa, pansi pa ulamuliro wamtendere wa Ufumu wa Mulungu, mtundu wa anthu sudzakhalanso ndi mantha ndi masoka achilengedwe. Panthaŵiyo dziko lapansili lidzakhaladi paradaiso weniweni.—Yesaya 65:17, 21, 23; Luka 23:43.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Poyerekeza, chivomezi choopsa chimene chinachitika ku dziko la Turkey mu August 1999 atachiyesa chinali 7.4, pa sikelo ya Rechter, komabe chinali chitapha anthu moŵirikiza kasanu ndi kaŵiri kuposa chimene chinachitika ku Taiwan.

[Chithunzi patsamba 27]

Mboni za Yehova zinachitabe misonkhano yawo pamene zimakhala m’makampu

[Chithunzi patsamba 28]

Chivomezi chinawononga misewu yambiri

[Mawu a Chithunzi]

San Hong R-C Picture Company

[Mawu a Chithunzi patsamba 28]

San Hong R-C Picture Company

[Mawu a Chithunzi patsamba 28]

Kuyeza chivomezi pa tsamba 26-8: Chithunzi mwachilolezo cha Berkeley Seismological Laboratory