Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuthandiza Achinyamata Kusiya Kupulupudza

Kuthandiza Achinyamata Kusiya Kupulupudza

Kuthandiza Achinyamata Kusiya Kupulupudza

YOLEMBEDWA NDI MTOLANKHANI WA GALAMUKANI! KU FRANCE

ZOCHITIKA zaposachedwapa zaonetsa poyera kuti bata ndi mtendere zawonongekeratu m’madera ambiri otsalira a m’mizinda ya ku France. Malingana n’zimene inanena magazini yachifalansa yotchedwa L’Express, “chiwawa cha m’mizinda chakwera moŵirikiza nthaŵi zisanu m’zaka zisanu ndi chimodzi.” Ndiponso, chiŵerengero cha achinyamata amene akukhudzidwa m’milandu yachiwawa chakwera kwambiri.

Kuphatikiza pa kuwononga zinthu, kugulitsa mankhwala osokoneza bongo, kulanda zinthu, kutentha zinthu, ndiponso umbava, achinyamata opulupudza akufuna makamaka anthu oimira Boma. Enanso amene amachitidwa chiwawa ndi anthu monga apolisi, ozimitsa moto, ndiponso ogwira ntchito m’magalimoto olipiritsa monga mabasi.

N’chifukwa chiyani pali chiwawa chachikulu chonchi? “N’chifukwa chakuti makhalidwe abwino amabanja awonongeka, motero kuchita chiwawa kuli kuukira dongosolo lililonse limene limakhala ndi malamulo monga opezeka m’mabanja,” analongosola motero akatswiri aŵiri asayansi ya khalidwe la anthu. Iwo ananenanso kuti “achinyamata amadziona kuti anyanyalidwa ndi opereka malamulo ameneŵa” ndi kuti alibe “chiyembekezo chilichonse cha tsogolo labwino.”

Mboni za Yehova zimalalikira mokhazikika uthenga wa m’Baibulo wopatsa chiyembekezo, m’madera amene kupulupudza kuli kofala. Posachedwapa, m’pulogalamu ina ya pawailesi yakanema ya chifalansa mtolankhani wina anati: “Mboni za Yehova zimafika ngakhale kumadera osauka kwenikweniko kumene nthaŵi zina kumaoneka ngati kunanyanyalidwa ndi mabungwe othandiza anthu, apolisi, ndi boma. Zimakalalikira ku nyumba ndiponso m’misewu ya m’maderawa, mmene zimayankhulitsa anthu ndiponso zimawamvetsera.” Ntchito yawo imathandiza anthu kwambiri, monga mmene kalata yotsatirayi yochokera kwa wachinyamata wina amene amaŵerenga Galamukani! ikunenera.

“Ndikufuna kukuthokozani ndi mtima wanga wonse chifukwa cha mabuku anu. Mwandithandiza ineyo pandekha komanso mwandithandiza kuti ndigwirizane kwambiri ndi makolo anga. Ndili ndi zaka 16 zokha ndipo ndimachokera m’banja lachisilamu.

“Chimene ndikufuna kunena n’chakuti mwandisiyitsa kupulupudza. Chifukwa cha zimenezo, ndikuchitsatira bwinopo chipembedzo changa komanso ndimaŵerenga Baibulo. Ndikupitirizabe sukulu chifukwa cha inu. Kuphatikizanso apo, kudzera m’magazini anu, mwathandiza anthu angapo m’dera limene ndikukhala amene ndimawabwereka magaziniwa mwezi uliwonse ndipo asiya kupulupudza. Ndikukuthokozani kwambiri ndipo ndikuona kuti sindikanafika apa chipanda inu.”