Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulimbana ndi Matenda Ofoola Thupi

Kulimbana ndi Matenda Ofoola Thupi

Kulimbana ndi Matenda Ofoola Thupi

YOSIMBIDWA NDI TANYA SALAY

Zaka zingapo zapitazo, ndinali mayi wamphamvu ndiponso mtumiki wanthaŵi zonse m’tauni yaing’ono ya Luverne, ku Alabama. Kuno moyo ndi wamtendere ndi waphee. Ine, mwamuna wanga, Duke, ndi mwana wanga wamng’ono Daniel, zinthu zinali kutiyendera bwino. Koma opaleshoni yochepa inasintha kwambiri moyo wathu.

MAVUTO athu anayamba mu 1992 n’tachotsetsa chibelekero. Zitangochitika izi, ndinayamba kumva ululu waukulu nthaŵi zonse ndipo ndinkakodza pafupipafupi (maulendo 50 kapena 60 patsiku). Mapeto ake dokotala wanga wa matenda a akazi anagwirizana ndi dokotala wa matenda a m’chikhodzodzo kuti ayese kupeza vutolo.

Ndinapita ku chipatala kukapimitsa. Paulendo wanga woyamba, dokotalayo anapeza kuti ndili ndi interstitial cystitis (IC), kapena chotupa chofoola cha m’chikhodzodzo. Zinali zovuta kupeza matendawo chifukwa zizindikiro za IC n’zofanana ndi za matenda ena onse a m’chikhodzodzo. Komanso, palibe njira yodziŵika yopimira matenda a IC. Choncho, madokotala asanagamule kuti uli ndi matenda a IC, amayamba athana ndi zizindikiro zina.

Dokotala wathu sanabise, anati poti mankhwala sakuthandiza, mapeto ake n’kungochotsa chikhodzodzo! Anati pali mankhwala ena koma onse sathandiza. Zimenezitu zinatiziziritsa nkhongono. Ndinali bwinobwino mpaka nthaŵi imeneyi. Monga Mboni za Yehova, ine ndi Duke takhala mu utumiki wanthaŵi zonse kwa zaka zambiri, ndipo tsopano anandiuza kuti chikhodzodzo changa n’chofunika kuchotsa. Ndikusangalala kuti mwamuna wanga anandichirikiza kwambiri.

Tinaganiza zofuna dokotala wina wa matenda a m’chikhodzodzo. Tinayesa madokotala osiyanasiyana. Tsoka lake n’kuti madokotala ambiri anali asanawadziŵe kwenikweni matenda a IC. Komanso, madokotala ambiri a matendawa anali ndi maganizo osiyanasiyana aliyense, choncho amapereka mankhwala osiyana. Buku lina la za mankhwala limati: “Nthendayi siitherapo.” Lina limati: “Asayansi sanapezebe mankhwala a IC, komanso sangadziŵe mtundu wa mankhwala amene munthu angagwirizane nawo. . . . Chifukwa madokotala sadziŵa chimene chimayambitsa IC, amapereka mankhwala kuthetsa zizindikiro zake zokha.”

Ndinali pamoto kwabasi chifukwa cha ululu waukulu wa m’mimba ndiponso kukodzakodza kwakuti ndinali wokonzeka kuchita chilichonse chimene madokotala anena. Ndayesa mankhwala amitundumitundu oposa 40 komanso azitsamba, oboola ndi timasingano pathupi, ochititsa dzanzi mitsempha, kubayidwa jekeseni m’fupa la msana, ndi transcutaneous electrical nerver stimulation (TENS), njira imene amaloŵetsa moto wamagetsi wochepa m’nthupi kwa mphindi kapena maola angapo. Ndinafufuza zimene ndinatha, zomwe zinandithandiza kudziŵako pang’ono zimene zinali kuchitika.

Pakalipano, ndikumwa methadone, wopha ululu, komanso mankhwala ena sikisi. Ndimapitanso kaŵirikaŵiri ku chipatala cha zaululu, kumene ndimakabayitsa jekeseni wochititsa dzanzi ndi mankhwala ena opatsa nyonga. Za vuto la kukodzakodza, ndimapita ku chipatala pakatha miyezi itatu kapena inayi iliyonse kukapangitsa zimene amati hydrodistension, njira imene amagwiritsa ntchito zinthu zamadzimadzi kukuza chikhodzodzo mwa kuchipopa monga chibaluni. Andipanga zimenezi maulendo ambiri. Zimandipatsadi mpumulo kwa miyezo ingapo. Ndakhala m’chipatala maulendo 30 m’zaka zingapo zapitazo.

Bwanji njira yomaliza, yongochotseratu chikhodzodzo? Buku lina likuti: “Madokotala ambiri amachita mphwayi kuchita opaleshoni chifukwa sadziŵa zimene zingachitike kwa wodwala aliyense—ena amachitidwa opaleshoni koma zizindikiro sizitha.” Chotero pakalipano ndilibe maganizo ameneŵa.

Nthaŵi zina ululu umakhala wopitirira muyeso ndiponso susiya msanga moti ndimataya mtima. Nthaŵi ina ndinafika poganiza zodzipha. Koma n’taganiza za chitonzo chimene zimenezi zingabweretse pa dzina la Yehova, ndinaopa kuchita zimenezo. Ndaona kufunika kwa pemphero ndi phunziro laumwini komanso kukhala pa ubale wolimba ndi Yehova, chifukwa sudziŵa zimene zingachitike kusintha moyo wako. Ndithudi ubale umenewu wapulumutsa moyo wanga panthaŵi yanga yodwala, popeza ndikudziŵa kuti chipanda zimenezi bwenzi n’tadzipha.

Ndikaganiza zaka naini zapitazo, ndaona mmene moyo ungasinthire mofulumira. Ndakhulupirira mawu a pa Mlaliki 12:1, amene amati: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako, asanadze masiku oipa, ngakhale zisanayandikire zakazo zakuti udzati, Sindikondwera nazo.” Ndimayamikira kwambiri kuti ndinayamba utumiki wa nthaŵi zonse ndili ndi zaka 15 ndipo ndinauchita kwa zaka pafupifupi 20. Nthaŵi yonseyo ubale wanga ndi Yehova unalimba kwambiri.

Ndikuyamika Yehova kuti mwamuna wanga ndi mwana wanga Daniel amandichirikiza kwambiri. Komanso, zimandilimbikitsa anthu a kumpingo akandiimbira foni kapena kubwera kudzandiona. Nthaŵi yozizira zimandivuta kutuluka panja chifukwa nthaŵi imeneyi ululu umachuluka zedi. Choncho ndimalalikira patelefoni, zimene zandithandiza kukhalabe ndi chiyembekezo cholimba cha Paradaiso. Ndikuyembekezera mwachidwi nthaŵi imene matenda ndi kuvutika zidzakhala zinthu zakale ndipo sitidzazikumbukira.—Yesaya 33:24.