Kodi Yehova Anali Mulungu wa Fuko la Ayuda?
Lingaliro la Baibulo
Kodi Yehova Anali Mulungu wa Fuko la Ayuda?
M’MAYIKO ambiri lerolino, dzina lakuti Yehova limadziŵika kwambiri ndi gulu la Mboni za Yehova. Komabe, dzina limeneli limapezekanso m’mabaibulo ena amene zipembedzo zinanso zimagwiritsa ntchito. Inde, dzina lakuti Yehova m’zilembo zinayi zotchedwa Tetiragalamatoni lagwiritsidwa ntchito kwa zaka zikwi zambiri.
Nthaŵi zina Yehova amatchedwa “Mulungu wa Israyeli.” (1 Mbiri 17:24) Mawu ameneŵa apangitsa anthu kukhulupirira kuti anali mulungu wa fuko limenelo lokha basi, kuti Ahebri anachita kubwerekera kwa mitundu ina kapena kudzipangira okha. “[Yehova] anayamba monga mulungu wankhanza kwambiri wa fuko la Aisrayeli,” akutero Karen Armstrong, amene analemba buku lakuti, A History of God (Mbiri ya Mulungu). “Kenako, aneneri a Israyeli . . . , m’zaka za ma 600 ndi 500 B.C., anasadutsa Mulungu wa fuko ameneyu kukhala wamkulukulu wosatheka kum’fotokoza.”
Anthu olemba mbiri yachipembedzo ochuluka ayesa kufotokoza kuti dzinalo Yehova linachokera kwa Akanani ndi Aigupto. Ena amanena kuti “ndi dzina lomwe fuko lakalelo linayambitsa” ndipo si dzina la Mulungu amene amatchulidwa mu “Chipangano cha Tsopano.” Kodi zimenezi n’zoona? Kodi kuŵerenga Baibulo mosamala kumasonyeza chiyani?
Yehova—Mulungu wa Anthu Onse
Baibulo limasonyezadi kuti Yehova anali paubale wolimba ndi mtundu wa Israyeli. Aroma 3:29) Kodi Paulo amanena Mulungu wake uti? Chabwino, m’kalata yopita kwa Aroma yomweyi, dzina lakuti Yehova lilimo maulendo 19. Pogwira mawu a Yoweli amene anali mneneri wachihebri wakale, mtumwiyu ananena kuti si Ayuda okha koma ‘aliyense adzaitana pa dzina la Ambuye [“Yehova,” NW] adzapulumuka.’—Aroma 10:13; Yoweli 2:32.
Koma chimenechi si chifukwa chonenera kuti iye anali wa fuko limeneli lokha basi. Paulo mtumwi wachikristu anafunsa kuti: “Mulungu ndiye wa Ayuda okhaokha kodi? Si wawo wa amitundunso kodi?” Kodi yankho lomveka la Paulo linali lotani? “Eya, wa amitundunso.” (Aisrayeli sanachite kusankha kuti Yehova akhale Mulungu wawo, koma Yehova ndi amene anawasankha kuti akwaniritse cholinga chake chokonza njira ya Mesiya. Ndiponso, tsogolo la mulungu wa fuko limadalira anthu ake. Fukolo akaligonjetsa, mulungu wawonso amagonja. Umu si mmene zakhalira ndi Yehova.
Pangano la Yehova ndi Abrahamu, limene linayamba kugwira ntchito zaka mazana ambiri Chikristu chisanayambe, linalonjeza kuti adzadalitsa anthu amitundu yonse, kusonyeza kuti Mulungu amasamala anthu onse. (Genesis 12:1-3; Machitidwe 10:34, 35; 11:18) Davide, mfumu ya Israyeli, anasonyeza kuti si dziko la Aisrayeli lokha limene linali la Yehova koma kuti: “Dziko lapansi n’la Yehova ndi zodzala zake zomwe, dziko lokhalamo anthu ndi iwo okhala m’mwemo.”—Salmo 24:1.
Ndiyeno Solomo mwana wa Davide atapatulira kachisi wolambiriramo kwa Yehova, anasonyeza kuti anthu odzichepetsa a mtundu uliwonse angam’fikire Yehova. M’pemphero lake lopatulira, Solomo anati: “Ndiponso kunena za mlendo, wosati wa anthu anu Aisrayeli, koma wakufumira m’dziko lakutali . . . nadzapemphera molunjika ku nyumba ino; mverani Inu m’Mwamba mokhala Inu, ndipo chitani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziŵe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisrayeli.”—1 Mafumu 8:41-43.
Aisrayeli Akanidwa
Pankhani ya ubale wa Aisrayeli ndi Yehova, Pulofesa C. J. Labuschagne analemba kuti: “Mu mbiri yonse ya Aisrayeli zinkachitika n’zoti nthaŵi zina Mulungu ‘wa fukolo’ sankawayanja ndipo nthaŵi zina ankawayesa mdani.” M’zaka za zana loyamba Aisrayeli atakana Mesiya, Yehova anakana mtundu umenewo.
Komabe, Akristu anapitiriza kugwiritsa ntchito dzina lakuti Yehova. Pamene mpingo wachikristu umakula, unali ndi anthu ochokera m’mitundu yonse. Wophunzira wachiyuda Yakobo, amene anatsogolera msonkhano wachikristu ku Yerusalemu ananena kuti Mulungu, ‘anayang’anira amitundu [amene si Ayuda], kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.’ Ndiyeno Yakobo posonyeza kuti zimenezi zinali zitanenedwa kale, anagwira mawu aulosi amene ali ndi dzina la Mulungu mu buku la Amosi.—Machitidwe 15:2, 12-18; Amosi 9:11, 12.
Amasamala ndi Kudalitsa Anthu Onse
Popitiriza kugogomeza mfundo yakuti Yehova ndi Mulungu wa anthu onse, Paulo analemba kuti: ‘Kulibe kusiyana Myuda ndi Mhelene; pakuti Yemweyo ali Ambuye wa onse, nawachitira zolemera onse amene aitana pa Iye.’ (Aroma 10:12) Inde, Yehova amadalitsa anthu onse omvera.
Yehova walonjeza anthu ake onse okhulupirika ndi omvera tsogolo laulemerero mosayang’ana mtundu kapena fuko lawo. M’Mawu ake anthu otereŵa amawatcha ‘zofunika za amitundu onse.’ (Hagai 2:7) Anthu ameneŵa amaphunzira za Yehova ndipo amam’konda. Za anthu ameneŵa, buku lomalizira m’Baibulo limati: “Mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu [Yehova], popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.”—Chivumbulutso 15:4.
[Chithunzi patsamba 28]
Mose atagwira Malamulo Khumi