Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndende Zili Pamavuto Oopsa

Ndende Zili Pamavuto Oopsa

Ndende Zili Pamavuto Oopsa

“Kumanga ndende zina pofuna kuchepetsa umbanda kuli ngati kutsegula manda ena pofuna kuchepetsa matenda oopsa,” anatero ROBERT GANGI, KATSWIRI WA ZANDENDE.

NTHAŴI zambiri m’madera mmene zinthu zina zosasangalatsa amazitchula mozungulira, anthu amatchula mawu ena omveka bwinopo akamatchula mawu osautsa akuti “ndende.” Anthu a m’madera ena akamatchula ndende amati “n’kumaphunziro” kumene anthu amaphunzirako “luso lantchito zosiyanasiyana” ndiponso kumene “amathandizidwa.” Anthu ena amakondanso kutchula mawu ena m’malo mwa mawu ochotsa ulemu akuti “mkaidi.” Komatu mukaonetsetsa mupeza kuti ndende zili ndi mavuto oopsa masiku ano. Pakufunika ndalama zambiri zosungira omangidwa ndiponso vuto lokwaniritsa cholinga chomanga anthu oswa lamulo likukulirakulira.

Anthu ena akukayikira ngati ndende zilidi zothandiza. Amati ngakhale kuti akaidi padziko lonse achuluka mpaka kuposa mamiliyoni asanu ndi atatu, upandu sunachepe n’komwe m’mayiko ambiri. Komanso, ngakhale kuti anthu ambiri amene ali m’ndende anamangidwira mankhwala osokoneza bongo, mankhwalawo akupezekabe modetsa nkhaŵa m’madera ena.

Komabe, anthu osiyanasiyana amaona kuti kumangidwa ndi chibalo chochita kuchifuna. Munthu wolakwa akamangidwa, iwo amaona kuti pachitika chilungamo. Mtolankhani wina anafotokoza khalidwe lokonda kumangomangamanga anthu olakwa kuti lakhala ngati “matenda.”

Pali zifukwa zikuluzikulu zinayi zimene ophwanya malamulo amawaikira m’ndende: (1) Kuwalanga, (2) kuteteza anthu, (3) kuletsa umbanda winanso, ndiponso (4) kusintha khalidwe la olakwawo, powaphunzitsa kuti akadzawamasula adzakhale osunga malamulo ndiponso othandiza ena. Tiyeni tione ngati ndende zikukwaniritsadi zolinga zimenezi.