Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ulendo Wokaona Malo ku Ghana

Ulendo Wokaona Malo ku Ghana

Ulendo Wokaona Malo ku Ghana

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU GHANA

MDIMA ndi nkhungu zitayamba kuchoka, kunja kunayamba kucha ndipo tinayamba kuyenda pang’onopang’ono mtunda wamakilomita 80 mumsewu wafumbi wopita kunkhalango yosungirako nyama zam’tchire ya Mole National Park, kumpoto kwa Ghana. Malo omwe tinali kuona m’njira, tchire lake makamaka linali la udzu, zitsamba, ndi mitengo yaifupi. Tikayenda kwakanthaŵi ndithu, tinkadutsa midzi yaing’ono yokhala ndi nyumba zaudzu zachipupa chomata.

Zinthu zinasinthiratu kwambiri titafika ku Damongo, tauni yochuluka zochitika yakumidzi komwe kuli masitolo, misewu yatala, ndiponso magalimoto ambirimbiri! Ana ovala yunifolomu zodera anali paulendo wawo wopita kusukulu. Akazi ovala malaya amitundu yokongola anali atasenza zinthu zosiyanasiyana pamitu yawo. Zinthuzo zinali nkhuni, zakudya, ndiponso zidebe zodzaza madzi. Magalimoto ndiponso mathirakitala anali kuliza mahutala, ndipo opalasa njinga anali kudutsa. Kunali kutatsala mtunda wa makilomita 20 kuti tifike.

Titafika ku Mole National Park

Kenako tinafika kunkhalangoyo. Zechariah amene anatiyendetsa ndi kutiyang’anira m’nkhalangoyo, anatiuza kuti nkhalango ya Mole Game Reserve anaikhazikitsa mu 1971 ndipo ndi yaikulu makilomita 4,840. Inali ndi mitundu 93 ya nyama zimene zimayamwitsa, mitundu 9 ya nyama zimene zimatha kukhala m’madzi ndi pamtunda pomwe, ndiponso mitundu 33 ya nyama zamtundu wa abuluzi. Zina mwa nyama zimenezi ndi mikango, akambuku, afisi, asimba, njovu, mphoyo, mtundu wa njati zazifupi, njiri, nyala, agwape, amwiri, ngondo, nsulu, anyani, apusi amitundu yosiyanasiyana, mbaŵala, nungu, ng’ona, ndiponso njoka zosiyanasiyana ndi nsato zomwe. Kuphatikizanso apo, mitundu ya mbalame imene imaoneka kuno n’njopitirira 300.

Tinali m’kati moingitsa tintchentche ting’onoting’ono toluma kwambiri uku tikuwayula udzu wofika m’mawondo, ndipo posakhalitsa tinafika pafupi ndi gulu la mbaŵala. Poyamba zimavuta kuti uzione, chifukwa ndi zamtundu wofanana ndi tchirelo. Tikuziyang’ana choncho, nazonso zinali dwii kutiyang’ana, mwakuti munthu sangathe kusiyanitsa kuti akuchita chidwi ndi mnzake ndani? Tili m’kati mojambula zithunzi tinadzidzimutsidwa ndi phokoso la kufwenthera kwa nyama yaukali limene linamveka chakumanja kwathu. Pochita ukali kuti tachidzidzimutsa chitafatsa, chimbaŵala champhongo chinavumbuluka kuthaŵira m’tchire lapatsogolo.

Kenaka, tinaona njovu zinayi zazikulu zili pansi pamtengo waukulu. Zinali kugwetsa nthambi ndi zitamba zake n’kumadya masamba akunsonga. Titaziyandikira mamita 10 okha, Zechariah anatiuza kuti tiyambe kujambula. Iye anamenya mbuyo ya mfuti yake n’kulira ngati chitsulo, ndipo potero njovuzo zinachoka pansi pamtengopo, ife n’kutengerapo mwayi wojambula zithunzi zabwino. Chapafupi pompo, njovuzo zinapeza zithaphwi ndipo zinayamba kusamba matope. Zechariah analongosola kuti njovuzo zimasintha mtundu malingana ndi mtundu wamatope amene zikusambamo. Nthaŵi zina zimakhala zofiira kapena zodera, mmalo mwa mtundu wawo weniweni wakuda.

Tinayendabe pang’ono ndipo tinatha kuona nkhalango yonseyo bwinobwino. Nkhalangoyi ilinso ndi mitengo yokongola ya kesha ndiponso mitengo ina yotchedwa shea. Pobwerera tinadzera njira yomwe zinadzera njovu zija. Njovuzo zinali patali ndithu, koma njovu yaikulu kwambiri pagululo inaimiritsa makutu ake, n’kuima mokonzekera ndeu ndipo inayamba kutitsatira. Kodi inkafuna kudzatigunda?

Zechariah anatiuza kuti tisachite mantha, koma nthaŵi yomweyo, iye ananyamula mfuti yake kuichotsa papheŵa ndipo anatipatutsa m’njira ya njovuzo. Tonse tinapitiriza kuyenda, wotiperekezayo atanyamula mfuti yake yotcheratchera, nafenso titanyamula makamera otcheratchera. Basi njovu zija sizinationenso.

Zechariah anatilongosolera kuti njovu za m’nkhalangoyi zinazoloŵera anthu mpaka zina zimatha kuwayandikira kwambiri. Njovuzo zikamaonekaoneka, asilikali operekeza anthu amazitcha mayina. Njovu ina anaipatsa dzina lakuti Chitupire chifukwa chakuti inali ndi mphuwa yaikulu pakhungu pake. Njovu ina anaipatsa dzina lakuti Nditalikire chifukwa inkakonda kuopseza alendo odzaona malo.

Kenaka tinakumana ndi anyani ambiri. Tinawaona akulendeŵera m’mitengo kapena akuthamangathamanga pansi. Wotiperekeza anatisonyeza nyani wamkazi atanyamula ana ake aŵiri, wina atam’bereka ndipo wina atam’kupatira. Wotiperekezayu akutiuza kuti anawo n’ngamapasa.

Komatu taonadi nyama zambiri lero. Zechariah akutiuza kuti, kuti muone nyama nthaŵi yachilimwe, kuyambira mwezi wa April mpaka June, muyenera kupita kuchitsime chifukwa n’kumene zimapita m’chigulu pokamwa madzi. Akutiuzanso kuti kuyenda m’nkhalangoyo mutakwera galimoto zoyenda m’matope, mungathe kuona nyama zina zambiri, komanso njati ndi mikango.

Tsopano nthaŵi yankhomaliro inafika. Tikudya, nyani wamkulu anakwera kumbuyo kwa galimoto ya bokosibode imene inaimikidwa pafupi ndi galimoto yathu ndipo anali kuyang’anitsitsa mwachidwi chakudya changa. Anyani ena akudutsa, pamodzinso ndi mbaŵala zina ndi njiri, ndipo pomaliza penipeni njovu zinayi zinatulukira pamwamba pachulu chapafupi pompo. Mwinatu imeneyi ndiyo inali njira yosavuta yosonkhanitsira nyama zimenezi kuti tizijambule.

Kumsika

Nthaŵi imene takhala ku Mole National Park n’njochepa kwambiri, koma tsopano tikuyamba ulendo wapagalimoto wamaola aŵiri wopita ku tauni ya Sawla, yomwe n’njakumidzi ndipo ndiko kumakhala anthu a mtundu wa a Lobi omwe ndi alimi. Akazi achilobi ali ndi chikhalidwe chodabwitsa chokulitsa milomo yawo mwadala. Ngakhale kuti masiku ano chikhalidwechi chikutha pang’onopang’ono chifukwa chakuti atsikana ayamba kuchangamuka ndi zochitika zamasiku ano, komabe azimayi ambiri amanyadirabe pokhala ndi milomo ikuluikulu. Moti kuuza mkazi wachilobi kuti ali ndi milomo yaing’ono ngati mwamuna amati n’chipongwe kwabasi.

Tinafika pamudzi wina ndipo tinaloŵa mumsika. Misasa yake anaimanga ndi nthambi zamitengo ndipo ili ndi madenga audzu. Tinaona mzungu mumsikamo ali yekhayekha pakati pa anthu akuda. Tinalankhula naye ndipo anatiuza kuti anafika kuno chaposachedwapa kuti adzatembenuze Baibulo m’chilankhulo cha Chilobi. Ankakhala m’mudzi wapafupi pamodzi ndi Alobiwa pofuna kudziŵa kulankhula bwino chilankhulo chawo. Ndinakumbukira Robert Moffat, amene anakhazikitsa mishoni pakati pa anthu olankhula Chitswana kumwera kwa Africa cha m’ma 1800 ndipo anatembenuza Baibulo m’chilankhulo chawo.

Mayi wachikulire wachilobi wamilomo ikuluikulu wakhala pabenchi mumsasa wina mumsikawo. Milomoyo ili ndi mabowo aŵiri ndipo analoŵetsamo timatabwa toyerera tatikulu ngati chikhadabo cha chala chamanthu. Nditangonyamula kamera yanga pofuna kum’jambula, iye ananyamukapo. Mnzanga wina analongosola kuti anthu achikulire amtunduwu amakhulupirira kuti mzimu wawo ungathe kuvulazidwa kwambiri ngati munthu atawajambula.

Tili m’njira kubwerera kutauni ya Sawla, kumene tinakagona, ndinkaganizira za nzeru ndiponso kuchuluka kwa zinthu zolengedwa ndi Mulungu zimene taziona. Iye analenga nyama ndiponso anthu mwaukatswiri. Nayenso wamasalmo anadzuma kuti: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.”—Salmo 104:24.

[Mapu pamasamba 24, 25]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

GHANA

[Chithunzi patsamba 24]

Njiri

[Chithunzi patsamba 24]

Fisi wamaŵanga

[Chithunzi patsamba 25]

Njovu

[Chithunzi patsamba 25]

Mvuu

[Chithunzi patsamba 25]

Gulu la mbaŵala

[Chithunzi patsamba 26]

Nyani wamkazi atanyamula ana aŵiri

[Chithunzi patsamba 27]

Ngondo

[Chithunzi patsamba 27]

Msika