Kodi Ndingatani Kuti Kuŵerenga Baibulo Kuzindisangalatsa?
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Kodi Ndingatani Kuti Kuŵerenga Baibulo Kuzindisangalatsa?
“Nthaŵi zina Baibulo limavuta kumvetsa, ndipo zimenezi zimagwetsa ulesi kwambiri,” anatero Annalieza, mtsikana wa zaka 17.
“Baibulo silinkandisangalatsa,”anatero Kimberly, mtsikana wa zaka 22.
ANTHU ambiri sakonda kuŵerenga. Motero angaone ngati buku lalikulu monga Baibulo n’lovuta kwambiri kuliŵerenga. Ngakhale anthu okonda kwambiri kuŵerenga angaone chimodzimodzi. Tammy, mtsikana wa zaka 17 ananena kuti: “Baibulo ndinkaliona ngati buku lalikulu kwambiri la mawu osadziŵika omwe anali ovuta kuwamvetsa. Kuŵerenga Baibulo kumafuna kuika maganizo onse pa kuŵerengako ndiponso kumafuna kulimbikira.”
Kuphatikizanso apo, ntchito ya kusukulu yokalembera kunyumba, ntchito zapakhomo, ndiponso zosangulutsa zingadye kwambiri nthaŵi ndi mphamvu zanu. Zingakulepheretseninso kuika maganizo pa kuŵerengako ndiponso simungaliŵerenge Baibulo mokusangalatsani. Alicia, amene ali m’gulu la Mboni za Yehova, nayenso amakhala ndi nthaŵi yokonzekera ndiponso yopitira kumisonkhano yachikristu komanso youza ena zimene amakhulupirira. Iye akuvomereza kuti: “Kuŵerenga Baibulo n’kovutadi chifukwa chakuti pali zinthu zina zambiri zimene umaona ngati n’zoyenera kuti uzichite.”
Komatu, Alicia, Tammy, ndiponso achinyamata ena ambiri aligonjetsa vutoli. Tsopano iwo amaŵerenga Baibulo nthaŵi zonse ndipo amasangalala akamatero. Kodi mukudziŵa kuti nanunso mungathe kutero? Lingalirani zinthu zitatu zimene mungachite kuti kuŵerenga Baibulo kuzikusangalatsani.
Konzani Nthaŵi Yoŵerenga Baibulo
Sally amene ndi mtsikana wazaka 18 anati: “Ndimaona kuti achinyamata amati kuŵerenga Baibulo n’kosasangalatsa chifukwa sanaliŵerenge mokwanira.” Monga mmene mumasangalalira mukamaseŵera maseŵera ena ake amene mumaseŵera kaŵirikaŵiri, mungasangalalenso n’kuŵerenga Baibulo mukamaliŵerenga nthaŵi zonse.
Koma nanga mungatani ngati simupeza nthaŵi yokwanira? Mtumwi Paulo anatilangiza kuti: “Penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa.” (Aefeso 5:15, 16) Mungathe kuwombola nthaŵi posataya nthaŵi yambiri pa zinthu zosafunika kwenikweni monga kuonera wailesi yakanema. Mawu amene Paulo anagwiritsa ntchito ponena kuti “nthaŵi” angatanthauze nthaŵi imene munthu angakhazikitse yochitira chinthu chinachake. Kodi mungaike nthaŵi yanji kuti muziŵerenga Baibulo?
Anthu ambiri amaŵerenga Baibulo m’maŵa, akatha kuŵerenga lemba ndi ndemanga zochokera m’kabuku kotchedwa Kusanthula Malemba Tsiku ndi Tsiku. * Ena amakonda kuŵerenga usiku asanagone. Sankhani nthaŵi yokuyenerani ndipo isintheni ngati mukufunikira kutero. Alicia ananena kuti: “Kusaumirira nthaŵi imodzimodzi kumandithandiza kwambiri kuti ndiziŵerenga Baibulo mosadukizadukiza.”
Achinyamata ena achikristu amakonza kuti mphindi 10 mpaka 15 patsiku zikhale zoŵerenga Baibulo tsiku lililonse. Pochita zimenezi, akwanitsa kuŵerenga Baibulo lonse chaka chimodzi kapena ziŵiri basi! Ngakhale mukuona ngati kuti simungakwanitse kutero, cholinga chanu chikhale chakuti muziŵerenga mbali inayake ya Baibulo tsiku lililonse. Mukatsimikiza kuŵerenga Baibulo panthaŵi yanu imene munaika, mudzawakonda kwambiri Mawu a Mulungu.—Salmo 119:97; 1 Petro 2:2.
Pempherani Kuti Mukhale ndi Nzeru
N’zoonadi kuti ngakhale anthu amene amaŵerenga Baibulo nthaŵi zonse amaona kuti mbali zina za Mawu a Mulungu n’zovuta kuzimvetsa. Amene analemba Baibulo, Yehova Mulungu, amafuna kuti muzimvetsa Mawu ake. Buku la Machitidwe limasimba za wapaulendo wina wa chiitiopiya amene sanali kumvetsa bwinobwino ulosi wa pa Yesaya chaputala 53. Munthuyu anali wofunitsitsa kupempha kuti athandizidwe, ndipo mngelo wa Yehova anatumiza mmishonale wotchedwa Filipo kuti akam’longosolere ulosiwo.—Machitidwe 8:26-39.
Motero kuŵerenga Baibulo kopindulitsa sikuyamba ndi kuŵerenga kwenikweniko ayi, koma kumayamba ndi pemphero. Asanatsegule Baibulo lawo, ena amaonetsetsa kuti apemphere kaye kwa Yehova kuti awapatse nzeru zakuti amvetsetse ndiponso alabadire maphunziro a m’malemba amene aŵerenge. (2 Timoteo 2:7; Yakobo 1:5) Mzimu wa Mulungu ungathenso kukukumbutsani malemba a m’Baibulo amene angakuthandizeni kuyankha mafunso kapena kuthana ndi ziyeso.
Mnyamata wina wachikristu akukumbukira kuti: “Pamene ndinali ndi zaka 12, bambo anga anasiyana ndi banja lathu. Tsiku lina ndinayamba kupemphera ndikugona, ndipo ndinkam’pempha Yehova kuti awabweze bambo anga. Kenaka ndinatenga Baibulo langa n’kuŵerenga pa Salmo 10:14 pamene pamati: ‘Waumphawi adzipereka kwa inu [Yehova]; wamasiye mumakhala mthandizi wake.’ Ndinakhala kaye phee. Ndinkangomva ngati kuti Yehova anali kundilankhulitsa n’kumandiuza kuti iye ndiye wondithandiza; iye ndiye Bambo wanga. Kodi palinso bambo wina amene ndingakhale naye woposa iye?”
Kodi chingakhale chizoloŵezi chanu kupemphera nthaŵi zonse musanayambe kuŵerenga Baibulo? Adrian anatchulapo mfundo yakuti: “Pempherani musanayambe kuŵerenga ndiponso mukamaliza kuŵerenga, kuti muzikambitsiranadi ndi Yehova.” Pemphero lochokera pansi pamtima lingakulimbikitseni kutsimikiza kuti musaphonye ndandanda yanu ya kuŵerenga Baibulo ndipo lingalimbikitse ubwenzi wanu ndi Mulungu.—Yakobo 4:8.
Muzikupangitsa Kukhala Kosangalatsa
Kimberly, mtsikana amene tam’tchula poyamba paja, ankaona kuti Baibulo n’losasangalatsa. N’zoona kuti Baibulo ndi buku lakale kwambiri, lolembedwa kale kwambiri asanatulukire makompyuta, mawailesi akanema, ngakhalenso ndege, komanso anthu opezeka m’Baibulo anafa kalekale kwambiri. Ahebri 4:12) Kodi buku lakale ngati limeneli lingapereke bwanji mphamvu?
Komabe, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.” (M’masiku a Ezara amene anali mlembi, amuna ndi akazi ambirimbiri, kuphatikizaponso “yense wakumva ndi kuzindikira” anasonkhana ku Yerusalemu kuti akamvetsere Chilamulo cha Mose chikuŵerengedwa. Panthaŵiyo, Chilamulochi chinali chitakhala kale kwa zaka zoposa 1000! Komabe Ezara ndi om’thandiza ‘anaŵerenga iwo m’buku m’chilamulo cha Mulungu momveka, natanthauzira, nawazindikiritsa choŵerengedwacho.’ Amuna ameneŵa atafotokozera Malembawo ndiponso kuwaŵerenga mogwira mtima, kodi chinachitika n’chiyani? ‘Anapita anthu onse kudya ndi kumwa, ndi kutumiza magawo, ndi kusekerera kwakukulu; popeza anazindikira mawu amene adawafotokozera.’—Nehemiya 8:1-12.
Kodi ‘mungatanthauzire’ bwanji zimene mukuŵerenga m’Baibulo? Cathy, mtsikana amene amaona kuti kuŵerenga n’kovuta, amaŵerenga mokweza kuti asatayike maganizo. Nicki amadziyerekezera kukhala munthu wa m’nkhani imene akuŵerengayo. Iye anati: “Ndimaganizira mmene ndikanamvera ndikanakhala kuti ndineyo. Nkhani imene ndakhala ndikuikonda kwambiri ndi ya Rute ndi Naomi. Ndingathe kuiŵerenga kambirimbiri. Nditasamukira kumzinda wina, nkhaniyi inandilimbikitsa chifukwa ndinkaganizira mmene Rute ankamvera pamene anali kupita kuchilendo komwe sanali kudziŵako aliyense. Ndinaona mmene iye anadalirira Yehova, ndipo nkhaniyi inandithandizadi kuti nanenso nditero.”—Rute, machaputala 1-4.
Kuti Baibulo likupatseni mphamvu muyenera kusinkhasinkha. Nthaŵi iliyonse mukaliŵerenga, ganizirani mofatsa malemba amene mukuŵerenga ndipo ganiziraninso mmene mungagwiritsire ntchito zimene mwaphunzira. Kuti mukometse kuŵerenga kwanu mungakondenso kufufuza m’mabuku othandiza kuphunzira Baibulo amene Mboni za Yehova zimafalitsa. *
Limbikani!
Kulimbikira kuŵerenga Baibulo n’kovuta. Ngakhale ndandanda yabwino kwambiri yoŵerengera Baibulo imafunika kuisintha nthaŵi ndi nthaŵi. Kodi mungatani kuti mulimbike pokwaniritsa cholinga chanu choŵerenga Baibulo tsiku lililonse?
Anzanu ndiponso a m’banja mwanu angakuthandizeni. Amber, mtsikana amene ali ndi zaka 15 ananena kuti: “Ndimakhala m’chipinda chimodzi ndi mng’ono wanga. Masiku ena ndimatopa kwambiri mwakuti ndimangofuna kugona, koma mng’ono wanga amandikumbutsa kuti ndiŵerenge kaye Baibulo. Motero sindiiwala ayi!” Ngati lemba linalake kapena nkhani inayake yakusangalatsani, uzaniko anzanu. Zimenezi zingakulitse chiyamikiro chanu cha Mawu a Mulungu ndipo zingathenso kukulitsa chidwi chawo poŵerenga Baibulo. (Aroma 1:11, 12) Ngati kwa tsiku limodzi kapena angapo mwachita mphwayi kuŵerenga Baibulo, musataye mtima! Yambirani pamene munalekezapo ndipo khalani ofunitsitsa kuposa kale lonse kuti mutsatire ndandanda yanu mosaphonya.
Osaiwala kuti pali madalitso ochuluka amene amabwera chifukwa choŵerenga Baibulo. Pomvetsera Yehova kudzera m’Mawu ake, angathe kukhala bwenzi lanu lapamtima. Mungathe kumvetsa bwino maganizo ake ndiponso mmene zinthu zimam’khudzira. (Miyambo 2:1-5) Choonadi chimenechi chochokera kwa Atate wathu wakumwamba chingatiteteze. “Mnyamata adzayeretsa mayendedwe ake bwanji?” anafunsa motero wamasalmo. “Akawasamalira monga mwa mawu anu.” (Salmo 119:9) Motero yambani ndiponso musaleke chizoloŵezi choŵerenga Baibulo. Muona kuti n’kosangalatsa kwambiri kuposa mmene mukuganizira!
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 11 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
^ ndime 22 Nsanja ya Olonda ya October 1, 2000, masamba 16-17, imapereka malingaliro angapo amene angakuthandizeni kudziŵa zambiri za m’Baibulo.
[Zithunzi patsamba 28]
Pemphero ndiponso kufufuza kungachititse kuti muzisangalala mukamaŵerenga Baibulo ndiponso kuti muzimvetsa tanthauzo la Malemba
[Chithunzi patsamba 29]
Kuyerekezera kuti nkhaniyo ikukuchitikirani inuyo kungachititse kuti Malembawo azikugwirani mtima