Kodi M’tsogolomu Zinthu Zidzakhala Bwanji?
Kodi M’tsogolomu Zinthu Zidzakhala Bwanji?
ANTHU ali mbali yaing’ono chabe ya zinthu zonse zolengedwa. Zolengedwa zonse za padziko lapansi zili ndi malo awo, malingana ndi ntchito yawo yopatsidwa ndi Mulungu. Pali zinthu zambiri zimene anthufe ndi zinthu zina zamoyo timadalira, koma chinthu chachikulu kwambiri ndicho moyo wodabwitsawu. Ndiye chifukwa chake anthu ambiri amadandaula kwambiri ngati chinthu chamoyo china chatheratu.
M’magazini yonena zachilengedwe ndi malo ake yotchedwa Consequences, wasayansi wina dzina lake Anthony C. Janetos analembamo kuti: “Anthu ambiri akhoza kuvomereza kuti anthu tonse tili ndi udindo woteteza malo a zinthu zachilengedwe za padzikoli, ndiponso udindo woyang’anira bwino zinthu zochuluka zachilengedwe kuti tipindule nazo panopa ndiponso m’tsogolo. Kuti titero timafunika kuona kufunika kwa zinthu zachilengedwe zosiyanasiyana pa zinthu, monga njira zimene zachilengedwezi zimathandizira zinzake ndiponso mmene ifeyo tiyenera kuzigwiritsira ntchito. Timafunikanso kuona mmene ifeyo tingasamalire zachilengedwezi.”
Kodi Anthu Akuchitapo Chiyani?
Ndithudi, chifukwa chakuti mayiko a padziko lonse akuda nkhaŵa ndi kutha kwa zinthu zachilengedwe, nthumwi za mayiko ndi mabungwe ena zakumana ndi kupanga msonkhano wokhudza zinthu zachilengedwe. Kugwirizana kwa mayiko onseŵa kukusonyeza kuti nkhani yosunga zinthu zachilengedwe ikudetsa nkhaŵa anthu onse.
Pofunanso kumvetsetsa ubwino wa zinthu zachilengedwe zosiyanasiyana, akatswiri a sayansi ya zinthu zamoyo, sayansi ya zinyama ndi malo awo okhala ndiponso akatswiri ena ndi ena padziko lonse ananena kuti chaka cha 2001 mpaka 2002 chikhale Chaka Choganizira Zinthu Zachilengedwe Padziko Lonse. Katswiri wa sayansi ya zinthu zamoyo
pa yunivesite ya Colorado State University dzina lake Diana Wall, yemwe ndi wapampando pamsonkhanowo anati: “Kufufuza zinthu zachilengedwe kubweretsa mapindu ambiri chifukwa titulukira zinthu zina zatsopano, monga chibadwa cha zinthu zina ndiponso mankhwala amene angagwiritsidwe ntchito kuti mbewu zikhale bwino kapena kuti nthaka yoipitsidwa ikhalenso yabwino.” Wall anapitiriza kunena kuti: “Chofunika kwambiri ndicho kudziŵa kumene kuli mitundu ya zachilengedwe yatsopano ndi ntchito imene zimachita kuti malo awo akhalebe abwino komanso mmene ifeyo tingasamalire zachilengedwezi. Ndi bwino kudziŵa zimenezi kuti tidziŵe bwino zochita ndi dziko lathu, mitsinje yathu ndiponso nyanja zathu.”Pakufunika Kusintha Kwenikweni
Ngakhale kuti anthu achitapo zinthu zabwino ndithu, iwo makamaka akhala akulimbana ndi zinthu zazing’ono osati zimene zikubweretsa vutoli. Panopa ofufuza akuti anthu alibe mpata wokwanira wochitira zinthu. Ruth Patrick wa pa sukulu yapamwamba yotchedwa Academy of Natural Sciences of Philadelphia, ku Pennsylvania m’dziko la America ataganizira mofatsa za vuto limene anati ndi vuto la “kuchepetsa zinthu zachilengedwe,” ananena kuti “sitiyenera kuzengereza ngakhale pang’ono . . . Ndi bwino kwambiri kuti anthu afulumire kuchitapo kanthu mosazengereza.” Kuti zinthu zisinthe pankhani ya kuwonongeka kwa zinthu zachilengedwe, m’pofunika kuti anthu asiye mwamsanga kusakaza dzikoli ndiponso zinthu zamoyo zimene zilimo. Pakufunika zinthu zinanso kuphatikiza pa kuletsa kuwonongaku. Bungwe la World Resources Institute linati, “Motero, vuto la kusunga zinthu zachilengedwe lilinso m’gulu la mavuto okhudza chitukuko pakati pa anthu . . .”
Kuti zimenezi zitheke, ndithudi pafunika kuti anthu onse asinthe kwambiri. Buku lakuti Caring for the Earth limati, kuti anthu ayang’anire zinthu bwino m’pofunika kukhala ndi “miyezo yabwino, kuyendetsa bwino chuma ndiponso anthu achikhalidwe chosiyana ndi cha anthu ambiri amene alipo masiku anoŵa.”
Baibulo limanena momveka bwino kuti anthu sangathe n’komwe kusintha zinthu choncho. Yeremiya 10:23 amati: “Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Miyambo 20:24) M’mbiri yonse, choonadi chimenechi chaonekera poyera ndipo zotsatira za kunyalanyaza mfundo imeneyi zatipangitsa kuti tikumane ndi “nthaŵi zoŵaŵitsa” zimene zikutchulidwa pa 2 Timoteo 3:1-5. Mavesi ameneŵa amasonyezanso kuti nthaŵi zoŵaŵitsazi zikuchitika chifukwa anthu amaganiza molakwa. Choncho, pokhapokha ngati anthu atasintha mpamene njira iliyonse yothetsera mavuto amene timakumana nawo idzakhale yothandizadi kwanthaŵi yaitali.
Wayansi wina wotchuka wotchedwa Dr. Jane Goodall, atafunsidwa anathirira ndemanga kuti kuwononga malo a zachilengedwe “nthaŵi zambiri kumachitika chifukwa chakuti mayiko otukuka akuchita umbombo ndiponso akufuna kulemera kwambiri.” Ndipo katswiri wa sayansi ya zinthu zomera Peter Raven, yemwe kale anali mlembi wa bungwe la U.S. National Academy of Sciences, anachenjeza kuti “umbuli, tsankho, umphaŵi ndiponso umbombo zikubweretsa mavuto osiyanasiyana amene angathe kuwononga kwambiri dziko.” Choncho, zinthu zina zimene anthu ayenera kusintha ndizo dyera, umbombo, umbuli, kusaganizira zam’tsogolo ndiponso kudzigangira.
Njira Yabwino Kwambiri Yotetezera Zinthu Zachilengedwe
N’zosadabwitsa kuti Mlengi amene analenga zinthu zamoyozi, zomwe n’zochuluka zedi, amaganizira kwambiri tsogolo la zolengedwa zake. Baibulo limatiuza kuti posachedwapa Mulungu adzachitapo kanthu ‘powononga iwo akuwononga dziko.’—Chivumbulutso 11:18.
Kodi Mulungu adzabweretsanso zinthu zamoyo zimene zatheratu chifukwa cha kuwononga dziko kumene anthu achita? Ngati Mlengiyu akufuna kuti mitundu yosiyanasiyana ya zinyama idzaonekenso padziko lapansi, mosakaika adzatha kuilenganso. Angathenso kudzalenga zomera zimene zatheratu. Koma chifukwa chakuti Baibulo silitiuza zimenezi, si bwino kumangoganizira zinthu zopanda umboni zimenezi.
Ulamuliro wa Mulungu umatitsimikizira kuti cholengedwa chilichonse padziko lapansi chidzadalitsidwa. Wamasalmo anati, “Dziko lapansi likondwere. Nyanja ikokome ndi zonse zokhalamo; minda isekere ndi zonse zokhalamo. Pamenepo mitengo yonse ya ku nkhalango idzafuula mokondwera.”—Salmo 96:11, 12, New International Version.