Khoti Lalikulu Livomera Kumva Mlanduwu
Khoti Lalikulu Livomera Kumva Mlanduwu
CHAPOSACHEDWAPA, Khoti lalikulu kwambiri ku United States lakhala likulandira milandu yopitirira 7000 pachaka ndipo pa milandu yonseyi lakhala likuvomera kuzengapo 80 kapena 90 yokha. Apa tingati linkangolola mlandu umodzi wokha pa milandu 100 iliyonse!
M’mwezi wa May, 2001, Mboni za Yehova zinapempha Khoti Lalikululi kuti liuonenso mlandu wawo ndipo zinafunsa funso lakuti: “Kodi malamulo aboma amanena kuti anthu ochita ntchito ya m’Malemba imene inayamba kalekale, yoyenda khomo ndi khomo n’kumauza ena chikhulupiriro chawo kapena kuwagaŵira mabuku awo a Mawu a Mulungu popanda kuwalipiritsa, n’chimodzimodzi ndi anthu otsatsa malonda m’makomo, amene amayenera kukatenga kaye chilolezo kuboma?”
Pa October 15, 2001, Dipatimenti yoona za milandu ya bungwe la Watchtower inauzidwa kuti Khoti Lalikulu ku United States lavomera kumva mlandu wawo umene ankaimba akuluakulu a tauni ya Stratton!
Khotilo linavomera kumva mbali imodzi chabe ya mlanduwo yokhudza za ufulu woyankhula, yakuti, kodi Lamulo Loyamba Lowonjezera limakhudzanso za ufulu wouza anthu ena nkhani inayake popanda kudziŵitsa kaye boma?
Zikatere, oweruza 9 akhotilo amayamba amvetsera kaye maganizo a amene adula chisamaniwo ndiponso amene akuimbidwa mlanduwo. A Mboni ali ndi maloya awo; nawonso a tauni ya Stratton ali ndi awo. Kodi pamenepa zinthu zithapo bwanji?
[Bokosi patsamba 5]
KODI LAMULO LOYAMBA LOWONJEZERA NDI LOTANI?
“LAMULO LOYAMBA LOWONJEZERA (KUKHAZIKITSA CHIPEMBEDZO, UFULU WOPEMBEDZA, WOYANKHULA, WOFALITSA NKHANI, WOSONKHANA, WODANDAULA) Nyumba ya Malamulo siingapange lamulo lililonse loletsa kukhazikitsa chipembedzo chinachake, kapena loletsa chipembedzocho kuchita zinthu mwaufulu; kapena loletsa ufulu woyankhula kapena wofalitsa nkhani; kapenanso ufulu wakuti anthu asonkhane pamodzi mwabata, ndiponso ufulu wodandaulira boma kuti lisinthe chinthu chinachake.”—Amatero Malamulo a Dziko la United States.
“Lamulo Loyamba Lowonjezera ndi limene pagona ufulu wonse wa anthu a ku United States. Lamulo limeneli sililola Nyumba ya Malamulo kukhazikitsa malamulo oletsa ufulu wa kuyankhula, kusonkhana, kapenanso kudandaula. Anthu ambiri amaona kuti ufulu woyankhula ngofunika kwambiri ndipo kuti ndiwo maziko a ufulu wina uliwonse. Lamulo Loyamba Lowonjezera limaletsanso Nyumba ya Malamulo kukhazikitsa chipembedzo cha boma kapena kuika malamulo ochepetsa ufulu wachipembedzo.” (Zachokera mu The World Book Encyclopedia) N’zochititsa chidwi kuti pa mlandu wina womwe chigamulo chake chinasintha zinthu wokhudzanso Mboni za Yehova wa Cantwell ndi boma la Connecticut, (mu 1940), Khoti Lalikulu ku United States linagamula kuti Lamulo Loyamba Lowonjezera sikuti limangoletsa “Nyumba ya Malamulo” yokha koma limaletsanso boma lililonse m’dzikolo kuika malamulo osemphana ndi ufulu wa anthu wotchulidwa m’Lamulo Loyamba Lowonjezera lija.
[Zithunzi patsamba 5]
Nkhani imeneyi ikukhudza kuyendera khomo ndi khomo pa zifukwa zosiyanasiyana
[Mawu a Chithunzi patsamba 4]
Photograph by Franz Jantzen, Collection of the Supreme Court of the United States