Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuvutikira Chikhulupiriro ku Ulaya mu Ulamuliro wa Chipani cha Nazi

Kuvutikira Chikhulupiriro ku Ulaya mu Ulamuliro wa Chipani cha Nazi

Kuvutikira Chikhulupiriro ku Ulaya mu Ulamuliro wa Chipani cha Nazi

YOSIMBIDWA NDI ANTON LETONJA

Pa 12 March, 1938, magulu a nkhondo a Hitler analoŵa m’dziko la Austria. Mawailesi anali pokopoko kuimba nyimbo za asilikali za perete ndiponso kunena mawu otamanda andale. Anthu a kwathu ku Austria, mitima inali m’mwamba kwabasi pofuna kuteteza dziko lawo.

HITLER atatenga ulamuliro mochita kulanda, anthu a ku Austria ankangoti basi zinthu zakhala bwino kwambiri. Ambiri ankakhulupirira kuti ulamuliro wakewo, umene iye ankati udzakhalapo mpaka zaka 1000 ndiwo udzathetse umphaŵi ndi ulova. Ngakhale ansembe a Chikatolika anatengeka mtima n’kumasonyeza nawo chizindikiro chosonyeza kugwirizana ndi Hitler.

Ngakhale kuti panthaŵiyo ndinali ndi zaka 19 basi, sindinatengeke ndi zinthu zimene Hitler ankalonjeza. Sindinkakhulupirira zakuti pali boma lililonse la anthu limene lingathetse mavuto onse a anthu.

Kuphunzira Choonadi cha M’Baibulo

Ndinabadwa pa April 19, 1919, mu mzinda wa Donawitz ku Austria, ndipo m’banja mwathu ndine mwana wachitatu komanso chitsirizira. Bambo anga anali munthu wakhama pantchito yawo ya mu mgodi wa malasha. Mu 1923 anatenga banja lathu lonse n’kupita nafe ku France komwe anakaloŵa ntchito m’tauni yotchedwa Liévin, yomwe inali ndi migodi. Chifukwa choti ankakonda kwambiri zandale, iwo sankakhulupirira n’komwe zopemphera, koma amayi anali Mkatolika wosasunthika. Kuyambira tili ana, amayiwo ankatiphunzitsa kuti tizikhulupirira Mulungu ndipo ankapemphera nafe usiku uliwonse. Kenako maganizo a bambo osakonda zopemphera aja anafika poipa moti mpaka analetseratu amayi kumapita kutchalitchi.

Chakumapeto kwa m’ma 1920, tinakumana ndi Vinzez Platajs, mnyamata yemwe makolo ake anali a ku Yugoslavia, ndipo ife tinkangomutchula kuti Vinko. Iyeyu ankadziŵana ndi a Mboni za Yehova, omwe kalelo tinkawatcha kuti Ophunzira Baibulo. Patapita nthaŵi pang’ono, Wophunzira Baibulo wina anayamba kumatichezera kwathu. Koma popeza kuti bambo anawaletsa amayi kupita kutchalitchi, amayiwo anam’funsa Vinko ngati n’zotheka kuti munthu n’kumalambira Mulungu ali panyumba. Vinkoyo anatchula mawu a pa Machitidwe 17:24, amene amanena kuti Mulungu “sakhala m’nyumba za kachisi zomangidwa ndi manja,” ndipo anafotokoza kuti malo abwino kulambira Mulungu ndi panyumba. Amayiwo anakondwera nazo n’kuyamba kumasonkhana nawo m’nyumba za anthu Ophunzira Baibulo.

Bambo anakalipa n’kuwauza kuti ati asiye zopusa zawozo. Pofuna kuti tisamasonkhane ndi anthu Ophunzira Baibulowo, iwo anatiumiriza kuti tizipita ku Misa Lamlungu lililonse! Popeza kuti amayi anawakanira zimenezo kwamtuwagalu, bambo analimbikira zakuti ndikhale mnyamata wothandizira Misa. Ngakhale kuti mayi anamvera zofuna za bambozo, iwo anapitirizabe kundiphunzitsa mfundo za m’Baibulo n’kufika poti ine n’kumvetsadi ndipo ankanditenga akamapita kumisonkhano ya anthu Ophunzira Baibulo.

Mu 1928, Vinko ndi mchemwali wanga Josephine, amene tinkamutchanso kuti Pepi, anaonetsa kudzipereka kwawo kwa Yehova pobatizidwa m’madzi. Aŵiriŵa anadzakwatirana. M’chaka chotsatira anabereka mwana wawo wamkazi, dzina lake Fini ndipo anabadwira ku Liévin. Patapita zaka zitatu, anawapempha kuti akakhale atumiki anthaŵi zonse ku Yugoslavia komwe kunali malamulo osiyanasiyana oletsa ntchito ya Mboni za Yehova. Ngakhale kuti ankakumana ndi mavuto ambirimbiri, iwo sanalekebe kutumikira Yehova mosangalala komanso mwakhama. Zimene ankachitazo zinandilimbikitsa kuti nanenso ndiyambe kulakalaka utumiki wanthaŵi zonse.

Kukula Mwauzimu

N’zodandaulitsa kuti mu 1932 makolo athu anafika mpaka posudzulana chifukwa cha kusamvana kwawo. Ine ndi amayi tinabwerera ku Austria, koma mchimwene wanga Wilhelm (Willi), anatsalira ku France. Zitachitika zimenezi, sitinkamvanso kaŵirikaŵiri za moyo wawo ndipo nawonso sankamva za moyo wathu. Anafika mpaka pomwalira asakutionabe ndi diso labwino.

Ine ndi amayi tinakhazikika m’tauni inayake ya ku Austria yotchedwa Gamlitz. Popeza kuti kumeneku kunalibe mipingo yoyandikana nafe, nthaŵi zambiri iwo ankakambirana nane nkhani zochokera m’mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Zinali zosangalatsa kuti munthu wina wotchedwa Eduard Wohinz ankabwera kunyumba kaŵiri mwezi uliwonse pa njinga n’cholinga chodzatilimbikitsa mwauzimu, ndipo ankayenda makilomita 100 kuchoka ku Graz kudzafika kwathu!

Ulamuliro wa Hitler wankhanza utangoyamba kumene mu 1938, Mbale Wohinz anamangidwa. Tinamva chisoni kwambiri titadziŵa kuti anachita kumupha ndi mpweya wa poizoni m’chipatala chinachake cha ku Linz. Anali wokhulupirika kwambiri ndipo zimenezi zinatilimbikitsa kuti nafenso tipitirize kutumikira Yehova mokhulupirika kwambiri.

Chaka cha 1938 Chinali Chosautsa

Mu 1935 n’kuti ku Austria a Mboni asakuwalola kuchita ntchito yawo. Ndiye magulu a nkhondo a Hitler ataloŵa m’dziko la Austria mu 1938, kuchita utumiki wathu kunayamba kuopsa kwambiri. Anthu oyandikana nafe ankadziŵa kuti ine ndi amayi ndife a Mboni za Yehova, motero tinaganiza zoti tisamadzionetsere. Ndinafika mpaka pomagona m’chinyumba chosungiramo zakumunda pofuna kuti anthu a chipani cha Nazi asandipeze.

Chakumayambiriro kwa chaka cha 1938 ndinali nditamaliza sukulu ndipo ndinkagwira ntchito mu bekale. Chifukwa chakuti ndinkakana kunena kuti “Hitler Mpulumutsi Wathu” kapenanso kukhala m’gulu la anyamata ankhanza a Hitler, anandichotsa ntchito. Koma zitatero mpamene ndinatsimikiza mtima kwambiri kuti ndionetse kudzipereka kwanga kwa Yehova Mulungu pobatizidwa m’madzi.

Ine ndi amayi tinabatizidwa pa April 8, 1938. Unali usiku pamene ifeyo pamodzi ndi anzathu ena okwana seveni tinakakumana kutchire m’kanyumba kenakake. Nkhani ya ubatizo itatha, tinkachoka mmodzimmodzi kudutsa m’kanjira kakang’ono kupita kumene kunali madzi. Kumeneko anatibatizira m’kadamu kochita kuŵaka ndi simenti.

Pa April 10, 1938, anachita chisankho chongofuna kudziŵa ngati anthu akufuna kuti dziko la Austria lizilamulidwa ndi dziko Germany. Pena paliponse m’dzikomo anakhomapo zikalata zokopa anthu zolembedwa kuti “Voterani Hitler!” Ine ndi amayi sankatiika m’gulu la mbadwa za dzikolo zoyenera kuvota chifukwa chakuti tinakakhalitsa ku France, ndipo zimenezi zinadzandipulumutsa m’tsogolo mwake. Nthaŵi ndi nthaŵi Franz Ganster, yemwe ankachokera ku Klagenfurt kum’mwera kwa dziko la Austria, ankatibweretsera magazini a Nsanja ya Olonda. Motero tinalimbikitsidwa ndi Mawu a Mulungu nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse isanayambike.

Mchimwene Wanga Willi

Chichokereni ku France, zaka zoposa zisanu ndi zinayi zinadutsa ine ndi amayi tisanayankhulaneko ndi Willi. Ngakhale kuti amayi ankam’phunzitsa za m’Baibulo adakali mwana, iye anapusitsidwa n’kumakhulupirira kuti utsogoleri wa Hitler pa zandale ndiwo udzakonze zinthu m’tsogolo. M’mwezi wa May, mu 1940, khoti linalake la ku France linalamula Willi kuti akhale m’ndende zaka ziŵiri chifukwa choswa lamulo lakuti asamagwirizane ndi chipani cha Nazi. Koma sanachedwe kum’tulutsa magulu ankhondo a ku Germany ataloŵa m’dziko la France. Panthaŵi imeneyo anatilembera kalata ali mumzinda wa Paris. Tinakondwera kudziŵa kuti anali adakali moyo, koma tinachita nthumanzi titamva zimene ankachita.

Pa nthaŵi ya nkhondoyo Willi ankatiyendera kaŵirikaŵiri popanda vuto lililonse chifukwa chakuti ankagwirizana ndi asilikali apadera a Hitler, omwe ankawatcha kuti a SS. Kupambana kwa asilikali a Hitler kunam’gometsa kwambiri. Nthaŵi zambiri ndikati ndimuuzeko zimene Baibulo limanena, ankangoti: “Zopusa zimenezo! Sukuona mmene ankhondo a Hitler akulandira mayiko ena? Posachedwapa dziko lonse likhala m’manja mwa anthu a ku Germany!”

Mu February 1942, Willi atabwera kunyumba patchuthi, ndinam’patsa buku lotchedwa Enemies, limene linafalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Ndinadabwa kwambiri kuona kuti anamaliza kuliŵerenga mosapumira. Anayamba kuzindikira kuti ulamuliro wa Hitler udzatha basi. Iye anaona kuti anali kutsatira ulamuliro wauchinyama ndipo sanafunenso zochedwachedwa motero anasiyiratu zoipazo.

Mmene Willi Ankaonera Choonadi cha M’Baibulo

M’mwezi wotsatira pamene Willi anabwera kudzationa, anali atasinthiratu. Iye anati: “Anton, ndaona kuti ndinkalakwitsa!”

Ndipo ine ndinamuuza kuti: “Ndiye mwazindikira mochedwatu achimwene.”

“Usatero ayi, sindinachedwe! Paja Baibulo limanena kuti ‘munthu ayenera kuchita chilichonse chimene angathe kuchita adakali moyo,’ ndipo tizingothokoza Mulungu kuti ineyo ndidakali moyo!”—Mlaliki 9:10.

Ndiye ndinam’funsa kuti: “Nanga ukuganiza kuchita zotani makamaka?”

Iye anayankha kuti: “Basi, sindikufunanso kupitiriza ntchito ya usilikaliyi. Ndikufuna ndisiyane nawo a chipani cha Naziŵa, ndione kuti zikhala bwanji.”

Nthaŵi yomweyo ananyamuka kupita ku Zagreb m’dziko la Yugoslavia kukaonanso mchemwali wathu, Pepi. Atasonkhanapo kangapo ndi Mboni za Yehova zomwe zinali zoletsedwa kumeneko, anabatizidwa mwachinsinsi. Ndithudi, mwana woloŵerera uja anabwerera!—Luka 15:11-24.

Pofuna kuthaŵa achipani cha Nazi ku France, Willi anaganiza zothaŵira ku Switzerland, koma asilikali a dziko la Germany anam’gwira. Anakamuimba mlandu mu khoti la asilikali ku Berlin, ndipo pa July 27, 1942, analamula kuti aphedwe chifukwa chothaŵa usilikali. Anandilola kuti ndikamuone m’ndende ya asilikali yotchedwa Berlin-Tegel. Anandipititsa m’kachipinda kenakake ndipo posakhalitsa Willi anatulukira atam’mangirira kwa msilikali amene ankalondera. Nditamuona ndinagwetsa misozi. Sanatilole kukupatirana ndipo anangotipatsa mphindi 20 zokha zoti titsanzikane.

Willi anaona kuti ndikulira ndipo anati: “Kodi ukulira chiyani Anton? Uyenera kukondwera! Ine ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa chondithandiza kuti ndidziŵenso choonadi! Ndikanati ndifere Hitler, bwenzi ndilibenso mwayi uliwonse. Koma popeza ndifera Yehova, ndili ndi chikhulupiriro chonse kuti adzandiukitsa ndiponso kuti tidzaonananso ndithu!”

M’kalata yake yotitsanzika analemba kuti: Mulungu wathu wokondedwa, amene ndimam’tumikira, amandipatsa chilichonse chimene ndimafuna ndipo sindikukayika kuti akhala nane mpaka mapeto, kuti ndipirire komanso kuti ndisagonje. Ndikubwerezanso kunena kuti, sindikudandaula ngakhale pang’ono ndiponso kuti ndakhalabe wolimba nji mwa Ambuye!”

Tsiku lotsatira, Willi ananyongedwa kundende ya ku Brandenburg kufupi ndi dziko la Berlin pa September 2, 1942. Apa n’kuti ali ndi zaka 27. Zimene anachitazi zikugwirizana ndi mawu a pa Afilipi 4:13, amene amati: “Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”

Vinko Anakhulupirika Mpaka Imfa

Ankhondo a ku Germany anali ataloŵerera m’dziko la Yugoslavia mu 1941, motero Pepi ndi mwamuna wake Vinko komanso mwana wawo Fini, wa zaka 12, anafunika kubwerera kwawo ku Austria. Panthaŵiyo n’kuti a Mboni ambiri m’dziko la Austria ali m’ndende kapenanso m’makampu ozunzirako anthu. Popeza kuti am’banja la mchemwali wangayo sanali mbadwa za ku Germany, anawatumiza kukagwira ukaidi pa famu inayake cha kum’mwera kwa dziko la Austria, kufupi ndi kwathu.

Kenaka pa August 26, 1943, apolisi osadziŵika kwa anthu omwe ankawatcha kuti a Gestapo anam’manga Vinko. Pamene Fini ankati atsanzike bambo akewo, wamkulu wa apolisiwo anam’menya zolimba moti ananyamuka m’malere n’kukagwera poteropo. Kaŵirikaŵiri apolisiwo ankam’panikiza nawo mafunso Vinko ndi kum’menya modetsa nkhaŵa, kenako anapita naye kundende yotchedwa Stadelheim mu mzinda wa Munich.

Pa October 6, 1943, apolisiwo anandimanga ndili kuntchito ndipo ananditumizanso kundende yomweyo ya Stadelheim komwe kunali Vinko. Popeza ndinkadziŵa Chifalansa, ankandiuza kuti ndizimasulira chiyankhulocho kwa akaidi a Chifalansa omwe anagwidwa pankhondo. Ndikamayenda kundendeko powongola miyendo, ndinkapeza mipata yocheza ndi Vinko.

Patapita nthaŵi Vinko anadzam’lamula kuti aphedwe. Akuti anam’peza ndi mlandu wopereka mabuku ofotokoza za m’Baibulo kwa a Mboni ndiponso kupereka ndalama kwa akazi a Mboni omwe amuna awo anali m’makampu ozunzirako anthu. Anam’samutsira kundende ya kufupi ndi ku Berlin ija komwe Willi anam’nyongera. Anakam’dula mutu kumeneko pa October 9, 1944.

Nthaŵi yomaliza imene Vinko anaonana ndi banja lake inali yolilitsa kwambiri. Anaonana naye atamangidwa unyolo komanso atasinthiratu chifukwa chomenyedwa ndipo sanathe kukupatirana naye chifukwa cha unyolowo. Fini anaonana ndi bambo akewo komaliza ali ndi zaka 14. Amakumbukirabe mawu omaliza amene bambo ake anamuuza akuti: “Fini, uziwasamalira amayi ako!”

Bambo ake atamwalira, Fini analandidwa m’manja mwa mayi ake n’kum’pereka kubanja linalake chijeremani la la chipani cha Nazi, ati kuti am’sinthe. Nthaŵi zambiri ankangokhalira kum’menya molapitsa. Asilikali a dziko la Russia ataloŵa m’dziko la Austria, anawombera banjalo, lomwe linkam’zunza kwambiri. Iwo ankaona kuti banjalo linali nganganga pambuyo pa chipani cha Nazi.

Nkhondoyo itatha, mchemwali wanga anapitiriza kukhala mtumiki wanthaŵi zonse mpaka pamene anamwalira mu 1998. Ankachita utumikiwu pa nthambi ya Mboni za Yehova ku Switzerland ali ndi mwamuna wake wachiŵiri, Hans Förster. Fini anatengera chitsanzo cha makolo ake ndipo pano ali ku Switzerland, kutumikira Mulungu woona,Yehova.

Ufulu Uja Ndinaupeza!

Chakumayambiriro kwa 1945 ndende yathu ya mu mzinda wa Munich inali m’gulu la nyumba zimene zinaphwasulidwa ndi mabomba. Mzinda wonsewo unaphwasukiratu. Tsiku loti woweruza amve m’landu wanga linafika nditakhala kale m’ndende chaka chathunthu ndi theka. Kunali kutangotsala masabata aŵiri okha kuti nkhondoyo itheretu pa May 8, 1945. Panthaŵi yomva mlandu wangawo anandifunsa kuti: “Kodi ulolera kugwira ntchito ya asilikali?”

Ndiye ndinayankha kuti: “Mkaidi saloledwa kuvala yunifolomu kapena kunena kuti ‘Hitler Mpulumutsi Wathu.’” Atandifunsa ngati ndingakonde kukhala msilikali ku Germany, ndinangoti: “Ingondipatsani chikalata chopitira kunkhondoko ndipo ndilembapo maganizo anga!”

Patangotha masiku ochepa chabe, nkhondo inatha ndipo anandiuza kuti ndili ndi ufulu wopita kwathu. Zitangotero, ndinasamukira ku tauni yotchedwa Graz komwe kunakhazikitsidwa mpingo waung’ono womwe unali ndi a Mboni okwanira 35. Koma panopa ku Graz kuli mipingo yokwanira 8.

Wondithandiza Wachikondi

Nkhondo itangotha, ndinakumana ndi mphunzitsi wachitsikana, dzina lake Helene Dunst yemwe poyamba anali m’chipani cha Nazi. Ulamuliro wa Nazi unam’khumudwitsa kwambiri. Nthaŵi yoyamba kucheza naye, iye anandifunsa kuti: “Zimatheka bwanji kuti inu nokha muzidziŵa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova pamene ena sadziŵa?”

“N’chifukwa chakuti anthu ambiri safufuza m’Baibulo,” ndinam’yankha choncho. Kenako ndinam’sonyeza dzina la Mulunguyo m’Baibulo.

Iye anadabwa, n’kunena kuti: “Ndiye kuti ngati Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova, tiyenera kudziŵitsa aliyense zimenezi!” Iye anayamba kulalikira choonadi cha m’Baibulo ndipo patatha chaka, anasonyeza kudzipereka kwake kwa Yehova pobatizidwa m’madzi. Tinadzakwatirana pa June 5, 1948.

Pa April 1, 1953, tinakhala atumiki anthaŵi zonse a Mboni za Yehova. Kenaka anatiitana ku kalasi ya nambala 31 ya Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo, yomwe inali kufupi ndi ku South Lansing mu mzinda wa New York. Kumeneko tinakalimbikitsidwa kwambiri pokhala limodzi ndi ophunzira anzathu ochokera m’mayiko 64.

Titamaliza maphunziro athuwo anatitumizanso ku Austria. Kwa zaka zingapo, tinkagwira ntchito yochezera mipingo n’cholinga chowalimbikitsa abale mwauzimu. Kenaka anatiitana kuti tikatumikire pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Luxembourg. Kenakanso anatipempha kuti tisamukire ku ofesi ya nthambi ya ku Austria, yomwe ili mu mzinda wa Vienna. Mu 1972 tikutumikirabe komweko, tinayamba kuphunzira chiyankhulo cha ku Serbia ndi ku Croatia pofuna kuti tizilalikira anthu ambiri a ku Yugoslavia amene anasamukira mu mzindawu pofuna ntchito. Tikunena pano, kuno ku Vienna kuli mipingo yokwanira 8 ya chiyankhulochi ndipo anthu a m’mipingoyi amachokera pafupifupi m’madera onse a ku Ulaya!

Pa August 27, 2001, mkazi wanga Helene anamwalira. Iye anali mnzanga weniweni amene wakhala akundithandiza kwa zaka 53 zimene tinakhala m’banja mosangalala. Panopa ndimayembekezera kwambiri nthaŵi ya chiukiririro.

Ndaonadi Kuti Mulungu Amandikonda

Ngakhale kuti ndakumana ndi zovuta zonsezi, ndimakhutirabe ndi ntchito imene ndikuchita pa ofesi ya nthambi ya kuno ku Austria. Posachedwapa, ndakhala ndi mwayi womapezeka pa chionetsero chonena za anthu amene anavutika mu ulamuliro wa Nazi n’kumasimba zimene ndinakumana nazo. Kuyambira mu 1997, chionetserochi chachitika m’mizinda ndi m’matauni 70 a kuno ku Austria, ndipo pachionetserochi amafunsa anthu amene anapulumuka m’ndende za Nazi ndi m’makampu ozunzirako anthu kuti asimbe za chikhulupiriro ndi kulimba mtima kumene Akristu oona anasonyeza m’ndendezo.

Ndimaona kuti ndi mwayi waukulu kuti ineyo ndinkawadziŵa anthu okhulupirika ameneŵa. Anachitadi mogwirizana ndi mawu a pa Aroma 8:38, 39, akuti: “Ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chilichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chili mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.”

[Chithunzi patsamba 13]

Banja lathu lonse mu 1930 (kuyambira kumanzere kupita kumanja): ineyo, Pepi, bambo, Willi, amayi, ndi Vinko

[Chithunzi patsamba 14]

Mchimwene wanga Willi, atatsala pang’ono kuti aphedwe

[Chithunzi patsamba 15]

Vinko ndi ine tinatsekeredwapo m’ndende iyi ya Stadelheim, ku Munich

[Zithunzi patsamba 15]

Mwana wa Vinko, Fini, anam’pereka kubanja la nkhanza la chipani cha Nazi ndipo iye ngokhulupirikabe mpaka pano

[Chithunzi patsamba 16]

Helene anali mnzanga wapamtima pa zaka 53 zomwe tinakhala m’banja

[Chithunzi patsamba 16]

Apa ndikukamba nkhani pachionetsero chonena za anthu amene anavutika mu ulamuliro wa Nazi