Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Nsapato Zanu Zimakukwanani Bwinobwino?

Kodi Nsapato Zanu Zimakukwanani Bwinobwino?

Kodi Nsapato Zanu Zimakukwanani Bwinobwino?

“Amene amadziŵa pamene nsapato imapweteka ndi munthu amene wavala nsapatoyo.”—AKUTI ANANENA ZIMENEZI NDI WANZERU WA KU ROME.

KODI ndi liti pamene munagula nsapato komaliza? Kodi zinakukwanani bwanji? Zinakukwanani bwinobwino? Kodi zinakutengerani nthaŵi yaitali bwanji kuti musankhe? Kodi amene anakuthandizani kuyesa anakuthandizanidi bwino? Kodi munazigula chifukwa cha kaonekedwe kapena chifukwa cha mmene phazi lanu limakwanira bwino? Kodi zikukukwanani bwinobwino panopa mutazivala kwa kanthaŵi? Kapena zimakupwetekani penapake?

Kugula nsapato si nkhani yapafupi. Ndipo kupeza saizi yoyenera n’kovuta kwabasi. N’chifukwa chiyani tikutero?

Kupeza Saizi Yokwana Bwinobwino

Choyambirira, kodi phazi lanu lalikulu n’lamwendo uti, wakumanja kapena wakumanzere? Kodi mukuganiza kuti mapazi anu ndi ofanana? Muganizenso kaŵiri! Mfundo ina yoti muiganizire ndiyoti phazi lililonse lili ndi masaizi anayi: saizi yoyamba, mukakhala pansi, yachiŵiri, mukaimirira, yachitatu, mukamayenda kapena kuthamanga, ndipo yachinayi, kukamazizira kapena kutentha. Kodi masaiziŵa ndi osiyana bwanji?

Ponena za saizi yoyambayo, mukakhala pansi, buku lakuti Professional Shoe Fitting limati: “Iyi ndi saizi ya nsapato mukaika phazi lanu pansi (mutakhala pa mpando).” Saizi yachiŵiri, monga mmene tanenera pamwambapa, amayesa saizi ya phazi lanu muli choimirira. Mukaimirira, kutalika ndi kunenepa kwa phazi lanu kumasintha. Buku limene tatchulali limafotokoza kuti: “Mafupa ndi minofu ya phazi la munthu amene wakhala pansi amakhala osakungika koma akangoimirira phazi lake ‘limakungika’ ndipo limasintha saizi.” Koma pali masaizi enanso aŵiri.

Saizi yachitatu ndi pamene mukuyenda, kuthamanga, kudumpha kapena kuchita maseŵera ena. Zimenezi “zimasintha saizi, kunenepa ndi kutalika kwa phazi.” Saizi yachinayi ikukhudzana ndi mmene phazi limasinthira chifukwa cha kutentha, kuzizira ndi chinyezi. Chifukwa cha zimenezi phazi limatha kukula mooneka ndithu. Choncho, n’zosadabwitsa kuti mumamva kampumulo mukavula nsapato zanu ngati munazivala tsiku lonse, makamaka ngati munavala saizi yolakwika! Ndipo nthaŵi zambiri mumakhala mutavala saizi yolakwika kumene.

Kodi Mapazi Anu Amawayeza Bwanji?

Kwa zaka zambiri, Eric anakhala akugula nsapato ya saizi 10 ndi theka kapena saizi 11, yonenepa. Panthaŵi imeneyi amakhala ndi chikundu pa chala chake chachiŵiri ndiponso chikhadabo cha pachala chake chachikulu chakumanzere chinali chopindika, ndipo izi zimamusowetsa mtendere kwambiri. Dokotala wake wamapazi anamuuza kuti akayezetse mapazi ake kwa katswiri woyeza saizi ya nsapato. Eric anadabwa kumva kuti saizi yomukwana bwino inali saizi 12 ndi theka, ndipo kunenepa kwake inayenera kukhala saizi A! * Saizi “A” imatanthauza phazi loonda. Kodi masaizi aŵiri amenewa, kutalika ndi kunenepa, ndi okwanira kuti mupeze saizi yokukwanani bwino? Kodi mungayeze bwanji phazi lanu?

Chida chodziŵika m’mayiko ena chimene amayezera saizi ya phazi amachitcha Brannock. (Onani chithunzi.) Angagwiritse ntchito chida chimenechi kuti apeze miyezo itatu: kutalika kwa phazi lonse, kutalika kuchoka pa chidendene kufika pamene pamakumana zala, ndi kunenepa kwa pamene pamakumana zala. Komabe, phazi lililonse ndi losiyana kukula ndi kunenepa kwake. N’chifukwa chake timayesa nsapato tisanagule. Apa m’pamene tingapuse. Kodi munayesako nsapato zimene mwazikonda kwambiri koma n’kupeza kuti zikupweteka penapake? “Nsapato imeneyi ikatanuka,” wogulitsayo akutero. Mukugula nsapatozo kenako n’kuyamba kudandaula patangopita masiku kapena milungu yochepa mutayamba kuzivala. Zikatero ndiye kuti n’kuyambika kwa chikundu china, kupindika kwa chikhadabo, kapena kutupa kwa mfundo ya chala chachikulu!

Kodi Mukuti Mwapeza Saizi Yokukwanani Bwino?

Kodi n’zotheka kupeza saizi yokukwanani bwino? Buku lakuti Professional Shoe Fitting likuyankha mosapita m’mbali kuti ayi. Chifukwa chiyani? “Chifukwa pali mavuto ambiri. . . . Munthu sakhala ndi mapazi ofanana ndendende saizi, kunenepa, kutalika kapena mmene amagwirira ntchito.” Choncho, ngati nsapato yakwana bwino phazi lanu lalikulu sindiye kuti ya phazi linalo ikukwanani bwino. “Koma zimenezi sizikutanthauza kuti n’zosatheka kupeza saizi yokwana bwino, kungoti tifunika kusamala tikamati yokwana ‘bwino’.”

Ngati mukufuna kudziŵa kuti ndi malo ati m’nsapato yanu pamene pamapweteka, onani nsapato zanu zakale. Onani m’kati mwake. Kodi m’pati pamene panapereseka kwambiri? Nthaŵi zambiri mudzapeza kuti m’pamene pamaponda chidendene, kuchidendene, ndiponso pamene pamakumana mafupa azala. Kodi zimenezi zikutiuza chiyani? Zikutiuza kuti “zigawo zina za nsapato sizigwirana bwinobwino ndi phazi. Zigawo zina zimapereseka kwambiri pamene zina sizikhudzidwa n’komwe.”

Ngakhale mmene khosi la nsapato lilili limathandizanso kuti zizikukwanani bwinobwino. Kodi mukudziŵa kuti nsapato zilipo za mitundu yosiyanasiyana? Pali yamtundu wa bal, imene pomanga zingwe, zikopa za m’mbali zimakumana kumunsi kwa phazi pafupi ndi zala. Koma ngati muli ndi phazi lonenepa, nsapato yamtundu wa blucher ndi yabwino kwa inu, chifukwa chakuti zikopa za m’mbali sizikokedwa kwambiri pafupi ndi zala. (Onani chithunzi.) Kodi n’chifukwa chiyani zimene talongosolazi zili zofunika? Buku tatchula lija limati: “Nthaŵi zambiri chidendene chimapweteka chifukwa chakuti nsapato ikuthina kwambiri pakhosi, ndipo chidendenecho chakankhikira kumbuyo.”

Nanga Bwanji Nsapato Zazitali za Azimayi?

Nsapato zazitali chidendene zimene azimayi amakonda kuvala zimabweretsa mavuto osiyanasiyana. Nsapatozi zimasintha kaimidwe ka thupi. Nthaŵi zambiri zimachititsa munthu kuweramira kutsogolo, zimene pamapeto pake, zimachititsa kuti maondo azipindika kwambiri kuti thupi lithe kuima moongoka. Nsapato zazitali chidendene zimachititsanso kuti akatumba azikungika, ndipo amaonekera kwambiri.

Choncho, kuti nsapato izimukwana bwino mzimayi, kapena izimupweteka, zagona pa chidendene. Buku la Professional Shoe Fitting lija limati pali zifukwa zazikulu zitatu zimene amapangira nsapato zazitali chidendene: ‘(1) “msinkhu,” kuti munthu azioneka wamtali, (2) kukongoletsa nsapatozo—chidendene ndi chimodzi mwa zinthu zimene zimakongoletsa nsapato ndipo (3) kukongoletsa azimayi, mwachitsanzo, nsapato zazitali za azimayi zimachititsa kuti miyendo yawo izioneka kwambiri.’

Azimayi ayenera kusamala kwambiri ndi kupendama kwa chidendene cha nsapato, chifukwa kumakhudzana ndi mmene kulemera kwa thupi kukufikira kuchidendene. Ngati kulemera kukudzera kumbuyo kapena kutsogolo kwa chidendene zili ndi mavuto ake. N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chidendene chikhoza kuthyoka munthuyo n’kugwa modetsa nkhaŵa.

Kuchokera pa zimene takambiranazi, n’zoonekeratu kuti kusankha nsapato yokwana bwinobwino kumatenga nthaŵi ndiponso nthaŵi zina kumafuna ndalama zochulukirapo, chifukwa chakuti nsapato yabwino imatenga nthaŵi yaitali kuti ipangidwe. Koma nsapato zanu zingakuthandizeni kuti muzimva bwino mukazivala, ndipo zimakhudza ngakhale thanzi lanu. Choncho musapupulume. Yezetsani mapazi anu bwinobwino. Musatengeke ndi fashoni kapena kaonekedwe.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 M’mayiko ena amagwiritsa ntchito manambala komanso zilembo za alifabeti kuti asonyeze kunenepa kwa phazi.

[Bokosi patsamba 29]

Zofunika Kukumbukira Posankha Nsapato

William A. Rossi ndi Ross Tennant akupereka malangizo otsatiraŵa m’buku lawo lakuti Professional Shoe Fitting.

“Anthu ena amaganiza kuti akayezetsa phazi lawo ndiye kuti apeza saizi ya nsapato yowakwana ndendende, koma sizili choncho.” N’chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa chakuti saizi ya nsapato ingasiyanesiyane malinga ndi kutalika kwa chidendene, kasokedwe kake, chikopa chake, ndiponso amene anapanga nsapatoyo. Zimenezi zili choncho makamaka masiku ano chifukwa chakuti pali opanga nsapato ambiri m’mayiko osiyanasiyana amenenso ali ndi miyezo yosiyanasiyana.

Akamayeza phazi lanu, ngati mwavala sokosi muziikokera kutsogolo kuti zala zanu zisamakhale zopindika zimene zingachititse kuti apeze saizi yolakwika.

Kodi azikuyezani motani? Muli chokhala pansi kapena choimirira? “Kuyeza kasitomala atakhala pansi ndi ulesi.” Zimachititsa kuti mupeze saizi yolakwika. Choncho, muziimirira pamene akuyeza phazi lanu. Komanso muziyeza mapazi onse. Musaganize kuti phazi lanu la kumanzere n’limene lili lalikulu. Yezani mapazi onse!

“Ukatswiri woyeza nsapato ndi ntchito ya anthu okhawo amene amaidziŵa bwino. Iwoŵa amagwira ntchito m’masitolo apamwamba kwambiri mmene muli anthu odziŵa kufunika koyeza nsapato mwaukatswiri.”

[Zithunzi patsamba 28]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Zigawo za nsapato

khosi

nsalu ya m’kati

chopondetsera chidendene

kutsogolo kwa chidendene

kupansi

pamimba

popondetsa chidendene

chikopa cha m’mbali

pokhala lilime

molowa zala

chidendene

khosi

pamimba

phaka

kupansi

[Zithunzi patsamba 29]

Chida choyezera phazi chotchedwa “Brannock”

[Chithunzi patsamba 30]

Nsapato zonse zimatsatira masitayelo seveni awa

[Zithunzi patsamba 30]

Mitundu ya khosi

Blucher

Bal