Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kusiya Ntchito Yopha Anthu N’kuyamba Ntchito Yolimbikitsa Mtendere

Kusiya Ntchito Yopha Anthu N’kuyamba Ntchito Yolimbikitsa Mtendere

Kusiya Ntchito Yopha Anthu N’kuyamba Ntchito Yolimbikitsa Mtendere

YOSIMBIDWA NDI TOSHIAKI NIWA

Mwamuna wa ku Japan woyendetsa ndege amene anaphunzitsidwa kuti akadziphulitse powononga sitima ya nkhondo ya ku America m’kati mwa nkhondo yachiŵiri ya padziko lonse, akufotokoza mmene ankamvera podikirira kukadziphulitsako.

DZIKO la Japan linagonja momvetsa chisoni pa nkhondo yotchedwa Battle of Midway ya mu June 1942, ndipo chifukwa cha zimenezi linasiya kulanda mayiko amene linkalanda m’mbuyomu ozungulira nyanja ya Pacific. Kuyambira pa nthaŵi imeneyi, dziko la Japan linkangogonja pomenyana ndi dziko la United States ndi mayiko ogwirizana nalo, ndipo mayiko ameneŵa anayamba kulilanda madera onse amene lidagonjetsa kale.

Mu September 1943, boma la Japan linalengeza kuti ana a sukulu a ku yunivesite, amene poyamba samapita nawo ku nkhondo, tsopano ayamba kuwalemba usilikali. Mu December chaka chomwecho, ndili ndi zaka 20, ndinalembetsa nawo usilikali ndili ku yunivesite. Patatha mwezi umodzi, ndinayamba kuphunzira ntchito yoyendetsa ndege zouluka kuchokera pa sitima yapamadzi. Mu December 1944, ndinaphunzira kuyendetsa ndege yankhondo yotchedwa Zero.

Kagulu ka Asilikali Kapadera Kotchedwa Kamikaze

Zinthu zimasonyezeratu kuti dziko la Japan latsala pang’ono kugonja. Pofika mu February 1945, ndege za adani zinali kuponya mabomba ambiri a mtundu wa B-29 pa dziko la Japan. Panthaŵi yomweyi, magulu apadera a asilikali apamadzi a ku United States anayandikira nthaka ya dziko la Japan, ndipo ndege zawo zouluka kuchokera pa sitima za pamadzi zinayamba kuphulitsa mabomba.

Miyezi yochepa izi zisanachitike, akuluakulu a nkhondo a ku Japan anali atagwirizana zoti amenye nkhondo komaliza pogwiritsa ntchito njira yoti anthu azidziphulitsa pakati pa adani awo n’kufera nawo limodzi. Zimene anagwirizanazi zinangochititsa kuti nkhondoyi izipitirirabe ndiponso anthu ambiri azingofabe ngakhale kuti pa nthaŵi imeneyi zinali zachidziŵikire kuti dziko la Japan ligonja pa nkhondo imeneyi.

N’chifukwa chake anapanga kagulu ka asilikali apadera kotchedwa Kamikaze. Anakatcha dzina limeneli kuchokera ku mphepo imene amati ndi yochokera kwa Mulungu yotchedwa kamikaze. Mphepo ya mkuntho imeneyi akuti inakankhira kutali sitima za pamadzi za anthu a ku Mongolia amene anabwera kudzaukira dziko la Japan m’zaka za m’ma 1200. Pa nkhondo yoyamba imene kaguluka kanachita, kanali ndi ndege zankhondo za mtundu wa Zero zisanu, iliyonse yokhala ndi bomba lolemera makilogalamu 250 loti akadziphulitse nalo pokawononga sitima za adani.

Gulu la asilikali a padera lotchedwa Yatabe Naval Flying Corps, limene ine ndinali mmodzi wa asilikali ake, linauzidwa kuti likonze kagulu kapadera ka asilikali oti azikawononga adani podziphulitsa. Tonsefe anatipatsa fomu yoti tilembe yosonyeza ngati tikufuna kukhala nawo mbali ya kagulu kodziphulitsaka.

Ineyo ndinaona kuti n’kofunika kuti ndifere dziko langa. Komabe, ngakhale ndikanalola kuti ndife poulutsa bomba lodzipha naloli, akanathabe kundiombera ndisanakaphulitse adaniwo, ine n’kungofera zachabe. Kodi mayi anga akanasangalala ngati ndikanafa ndisanakwanitse zimene banja langa limafuna? Zinandivuta kwambiri kuti nditsimikize kuti kulowa nawo kagulu ka asilikali okadziphulitsaka ndiyo inali njira yabwino kwambiri yogwiritsira ntchito moyo wanga. Komabe, ndinavomera.

Mu March 1945, gulu loyamba la asilikali a Yatabe Special Attack Corps linakonzedwa. Ngakhale kuti asilikali anzanga 29 anatengedwa, ine sananditenge nawo. Ataphunzitsidwa mwapadera, anauzidwa kuti adzapita ku ulendo wokadziphulitsawo mu April kuchokera pa bwalo la ndege la Kanoya m’chigawo cha Kagoshima. Asananyamuke kupita ku Kanoyako, ndinapita kukawachezera anzangawo kuti ndimve maganizo awo pa ntchito yokafa nayoyo.

“Ife tikukafa,” anandiuza choncho mmodzi wa iwo mtima uli m’malo, “koma iwe usachite kuithamangira imfa. Amene apulumuke ayenera kudzauza ena kuti mtendere ndi chinthu cha mtengo wapatali kwambiri, ndipo adzagwire ntchito zolimba kuti aupeze.”

Pa April 14, 1945, anzangawo ananyamuka. Patatha maola angapo, tonsefe tinatchera khutu ku wailesi kuti timve kuti zinthu zayenda bwanji. Woulutsa mawu pa wailesiyo anati: “Gulu la asilikali apadera a Kamikaze la First Showa Unit ladumphira gulu la adani athu pa nyanja, kum’maŵa kwa Kikai Shima. Onse afa pankhondoyi.”

Ohka—Munthu Asanduka Bomba

Patatha miyezi iŵiri, anandisamutsira ku gulu lankhondo lapamadzi lotchedwa Konoike Naval Flying Corps kuti ndikakhale mmodzi wa asilikali ake apadera otchedwa Jinrai. Dzina loti Jinrai limatanthauza “bingu la Mulungu.” M’gululi tinali ndi ndege zimene zimagwira ntchito pamtunda (zotchedwa Attackers), ndege zankhondo zoperekeza, ndiponso ndege zoponya mabomba.

Ku ndege iliyonse ya Attacker ya mainjini aŵiri amamangirirako ka Ohka, dzina limene limatanthauza “maluwa.” Kamaimira asilikali onse achinyamata amene anali okonzeka kufa. Ka Ohka kanali kandege ka mpando umodzi wokha koyendera mphepo, mapiko ake anali otalika mamita asanu, ndipo kamalemera makilogalamu 440. Kutsogolo kwake amaikako bomba lolemera pafupifupi makilogalamu 1000.

Ndege yaikuluyo ikamayandikira pamene amafuna kuphulitsapo, munthu wina wodziŵa kuyendetsa ndege amakwera ka Ohka, kamene kenako amakadula kukachotsa ku ndege yaikuluyo. Kakatero kamauluka pang’ono pogwiritsa ntchito mphamvu ya maroketi atatu amene amatha kukaulutsa kwa masekondi khumi roketi iliyonse. Kenaka ka Ohka kaja kamakagwera chinthu chimene akufuna kuphulitsacho. Uku kunalidi kumsandutsa munthu kukhala bomba. Akangokaponya, panalibenso kubwerera!

Akamayesezera, woyendetsa Ohka amakwera ndege yankhondo ya Zero n’kudumphira chinthu chimene akufuna kuphulitsacho kuchokera pamwamba potalika mamita 6,000. Pali oyendetsa ndege angapo amene ndinawaona akufa pochita zimenezi.

Ndisanakaloŵe nawo kagulu kapaderaka, gulu loyamba la asilikali ake linanyamuka. Linali ndi ndege za Attacker 18 zokhala ndi ma Ohka, ndipo linaperekezedwa ndi ndege zankhondo 19. Ndege za Attacker zinali zolemera ndiponso zouluka pang’onopang’ono. Palibe ndi imodzi yomwe imene inakafika kumene imapita. Zonse zinaomberedwa ndi ndege zankhondo za ku United States, pamodzi ndi ndege zoperekeza zomwe zija.

Popeza ndege zonse zoperekeza zinali zitatha, gulu la asilikali a Jinrai ndiye kuti linafunikira kuchita nkhondo zake zonse zotsatira popanda ndege zoperekeza. Amene anapita kunkhondo m’njira imeneyi sanabwereko. Onse anafa ndipo anazimiririka ku nkhondo ku Okinawa.

Mapeto a Nkhondoyo

Mu August 1945, anandisamutsira ku gulu la asilikali otchedwa Otsu Naval Flying Corps. Malo okhala asilikali amene ndinatumizidwako anali mmunsi mwa phiri la Hiei-zan, pafupi ndi mzinda wa Kyoto. Chifukwa timayembekezera kuti magulu ankhondo a ku United States afika posachedwa pa nthaka ya dziko la Japan, anakonza zoti tidzaponye ma Ohka kuchokera pamwamba pa phirilo n’kuwaphulitsira pa sitima zankhondo za ku United States. Njanji zoti adzaikemo ndege zoponyera mabombawo anaziyala pamwamba pa phiripo.

Tinali kudikirira kuti atiuze kuti tinyamuke. Koma sanatiuze. Pa August 15, dziko la Japan linavomera kuti lagonja kotheratu ku dziko la United States ndi mayiko ogwirizana nalo, pamene mayikoŵa anaphulitsira mabomba amphamvu kwambiri pa mzinda wa Hiroshima ndi Nagasaki pa August 6 ndi August 9. Nkhondoyo tsopano inatheratu. Ine ndinapulumuka mwamwayi.

Kumapeto kwa August, ndinabwerera kwathu ku Yokohama, koma ndinapeza nyumba yanga itapserezedwa ndi mabomba amtundu wa B-29. Banja lathu linalibiretu pogwira. Mchemwali wanga pamodzi ndi mwana wake wamwamuna adaphedwa pamene mabombawo ankaphulitsidwa. Komabe, tonsefe tinatonthozedwako pang’ono chifukwa mchimwene wanga anabwerako wamoyo ku nkhondoko.

Zinthu zikadali zophwasuka komanso chakudya chikusowa kwambiri, ndinabwereranso ku yunivesite kuti ndikamalize maphunziro anga. Nditaphunzira kwa chaka chimodzi, ndinamaliza maphunzirowo ndipo ndinayamba ntchito. Mu 1953 ndinakwatira Michiko ndipo patapita nthaŵi tinakhala ndi ana aamuna aŵiri.

Kufunafuna Mtendere

Mu 1974, Michiko anayamba kuphunzira Baibulo ndi wa Mboni za Yehova. Kenaka anayamba kumapita ku misonkhano yawo komanso kuchita nawo ntchito yolalikira. Ine ndinamuletsa kuti asamachokechoke pakhomo. Iye anandifotokozera kuti utumiki wachikristu umabweretsa mtendere weniweni komanso chimwemwe. Ndinaganiza kuti ngati zimenezi zinali zoona, sindiyenera kumuletsa. M’malo mwake ndizimulola.

Chapanthaŵi imeneyi, ndinalemba anyamata a Mboni angapo ntchito yolondera usiku. Atabwera kudzayamba ntchito, ndinawafunsa kuti andifotokozere za gulu lawo ndi ntchito imene gulu lawolo limachita. Ndinadabwa kuona kuti anyamata ameneŵa anali ndi mzimu wodzipereka ndipo maganizo awo onse anali pantchito yawoyo, mosiyana ndi mmene analili anyamata ena a msinkhu wawo. Anaphunzira zimenezi m’Baibulo. Iwo anandifotokozera kuti Mboni padziko lonse lapansi sizisankhana mitundu ndipo zimamvera ndi mtima wonse lamulo la m’Baibulo loti azikonda Mulungu komanso anansi awo. (Mateyu 22:36-40) Zimaona Mboni zinzawo ngati abale ndi alongo awo, mosasamala kanthu kuti akukhala m’dziko liti.—Yohane 13:35; 1 Petro 2:17.

‘Zimenezo ndi nkhambakamwa chabe,’ ndinaganiza choncho. Popeza mipingo yosiyanasiyana ya Matchalitchi Achikristu imangokhalira kumenyana, sindinakhulupirire kuti Mboni za Yehova zingakhale zosiyana.

Ndinawafotokozera maganizo okayikira amene ndinali nawowa. Pogwiritsa ntchito Yearbook of Jehovah’s Witnesses, Mboni za chinyamatazo zinandisonyeza kuti Mboni za ku Germany zinaikidwa m’ndende, ngakhale kuphedwa kumene, chifukwa chokana kutenga mbali iliyonse mu ulamuliro wa Hitler. Ndinatsimikiza kuti Mboni za Yehova ndi Akristu oona.

Mkati mwa nthaŵi imeneyi, mkazi wanga anasonyeza poyera kudzipatulira kwake kwa Mulungu mwa kubatizidwa m’madzi mu December 1975. Pa nthaŵi yaubatizoyi anandipempha kuti ndiphunzire Baibulo. Koma chifukwa chakuti panali zinthu zambiri zofuna ndalama zimene ndinayenera kuchita, monga kulipirira ana anga sukulu komanso kubweza ngongole ya nyumba yathu, sindinavomere phunzirolo. Azibambo okwatira a mumpingomo panthaŵi imeneyi anali kusintha ntchito zawo kuti azitha kukhala ndi mpata wambiri wochitira zinthu. Ndinaganiza kuti inenso ndidzafunikira kutero. Koma atandisonyeza kuti n’kotheka kukhala Mkristu kwinakunso n’kumagwira ntchito yolembedwa, ndinavomera kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.

Kusankha Kutumikira Mulungu wa Mtendere

Patatha zaka ziŵiri ndikuphunzira Baibulo, amene amandiphunzitsa anandifunsa ngati ndinaganizapo zopatulira moyo wanga kwa Mulungu. Koma sindikanatha kuchita zimenezo, ndipo izi zimandisoŵetsa mtendere.

Tsiku lina ndinkatsika mofulumira masitepe a kuntchito kwathu. Kenaka ndinapunthwa n’kugubuduzika ndipo ndinakamenyetsa nkhongo yanga pansi n’kukomoka. Nditatsitsimuka, mutu unkandipweteka kwambiri ndipo ananditenga pa ambulansi kupita nane ku chipatala. Ngakhale nkhongo yanga inali yotupa kwambiri, mafupa a m’mutu sanaphwanyike ndipo magazi sankatulukira mkati.

Ndinayamikira kwambiri Yehova chifukwa cha moyo umene ndinali nawo! Kuyambira pamenepo, ndinatsimikiza kuti ndidzaugwiritsa ntchito kuchita chifuniro cha Yehova, ndipo ndinadzipatulira kwa iye. Mu July 1977, ndinabatizidwa ndili ndi zaka 53. Mwana wanga wamwamuna woyamba, Yasuyuki, nayenso anaphunzira Baibulo ndipo anabatizidwa zaka ziŵiri pambuyo pake.

Patatha zaka khumi chibatizidwire, ndinapuma pa ntchito. Nthaŵi yonseyi kuyambira pamene ndinabatizidwa ndinali kukhala moyo wachikristu, kwinakunso n’kumagwira ntchito. Panopa ndine mkulu ku Yokohama, umene uli mwayi wapadera kwambiri ndipo ndimathera nthaŵi yambiri mu utumiki wachikristu. Mwana wanga wamwamuna woyamba ndi mkulu ndiponso mtumiki wa nthaŵi zonse mu mpingo woyandikana nawo.

Chifukwa ndinapulumuka ku gulu lapadera la asilikali ankhondo ogwira ntchito yopha anthu podziphulitsa ija, ndine woyamikira kwambiri kuti ndili ndi moyo, ndipo ndimaona kuti ndi mwayi wapadera kuchita nawo ntchito yolalikira “uthenga uwu wabwino wa Ufumu.” (Mateyu 24:14) Ndine wotsimikiza kotheratu kuti njira yabwino kwambiri kuposa zonse yokhalira ndi moyo ndiyo kukhala mmodzi wa anthu a Yehova. (Salmo 144:15) M’dziko latsopano limene likubwera posachedwali, anthu sadzavutikanso ndi nkhondo, chifukwa “mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”—Yesaya 2:4.

Ngati ndi chifuniro cha Mulungu, ndingadzakonde kukumananso ndi anthu amene ndinkawadziŵa amene anamwalira pankhondo aja akadzaukitsidwa. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kuwafotokozera za moyo wamtendere umene angasangalale nawo pa dziko lapansi la paradaiso, mu ulamuliro wolungama wa Ufumu wakumwamba wa Mulungu!—Mateyu 6:9, 10; Machitidwe 24:15; 1 Timoteo 6:19.

[Chithunzi patsamba 25]

Pamene ndinali msilikali wapamadzi woyendetsa ndege

[Chithunzi patsamba 25]

“Ohka”—Munthu asanduka bomba

[Mawu a Chithunzi]

© CORBIS

[Chithunzi patsamba 26]

Ndili ndi anzanga asanapite ku nkhondo yokadziphulitsa. Ndine wachiŵiri kuchokera kumanzere, ndipo ndine ndekha amene ndinapulumuka.

[Chithunzi patsamba 27]

Ndili ndi mkazi wanga, Michiko, ndi mwana wanga wamwamuna woyamba, Yasuyuki

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

U.S. National Archives photo