Zimene Mungachite Kuti Muzigona Bwino
Zimene Mungachite Kuti Muzigona Bwino
VUTO LA KUGONA si lachilendo ayi. Zaka zoposa 2,400 zapitazo, wantchito wina m’nyumba ya Ahaswero, Mfumu ya a Peresi, analemba kuti ‘usiku winawake tulo ta mfumu tidamwazika.’—Estere 6:1.
Masiku ano pali anthu ochuluka zedi a vuto la kugona. Rubens Reimão, yemwe ndi katswiri wa nkhani zokhudza kugona ku Brazil, anati pafupifupi munthu mmodzi pa anthu atatu aliwonse padziko pano ali ndi vuto la kugona. * Dr. David Rapoport wa ku dipatimenti yoona za matenda a kugona pa yunivesite ya New York anati, kusagona bwino “kuli m’gulu la matenda amene avuta kwambiri m’zaka 100 zimene tayambazi.”
Chimaipitsanso zinthu n’chakuti anthu ambiri omwe ali ndi vutoli sadziŵa chifukwa chake. Ofufuza a pa yunivesite ya boma ya ku São Paulo m’dziko la Brazil, anati anthu atatu okha pa anthu 100 aliwonse omwe ali ndi vutoli ndi amene amakawapezadi ndi vutoli kuchipatala. Ambiri salimbana nalo n’komwe vutoli, motero amangozoloŵera kuti masana amakhala onyong’onyeka, n’kumasoŵa mtendere chifukwa cha tulo.
Usiku Umatalika
N’zosautsa kwambiri kumangotembenuka usiku wonse, m’maso muli gwa, anzanu akupha mkonono. Koma si kuti n’zodabwitsa kuti munthu asoŵeko tulo masiku ochepa chabe, ndipo izi zimachitika makamaka chifukwa cha kutopa kwambiri ndiponso mavuto ena amene timakumana nawo m’moyo. Koma vuto la kugona likakula, nthaŵi zina amakhala ali matenda, ndipo
ndi bwino kupita kuchipatala.—Onani bokosi lili pamwambali.Kodi mwina inuyo muli ndi vuto la kugona? Ngati mutayankha mafunso onse amene ali patsamba 9 n’kuona kuti n’zoonadi muli ndi vuto la kugona, musavutike nazo ayi. Kudziŵa kuti mukufunikira chithandizo, pakokha n’chinthu chofunika kwambiri pochiza vuto la kugona. Geraldo Rizzo, yemwe ndi dokotala wa matenda okhudza ubongo ku Brazil, anati anthu 9 pa anthu 10 aliwonse omwe ali ndi vuto la kugona angathe kuchizidwa bwinobwino.
Koma kuti alandire chithandizo choyenera m’pofunika kudziŵa bwinobwino chikuchititsa vutolo. Njira inayake yoyeza anthu a vutoli akamagona yathandiza kwambiri kupeza ndi kuchiza mavuto ambiri okhudza kugona.—Onani bokosi lili pamunsili.
Chifukwa china chimene anthu ambiri aakulu amakhalira ndi vuto la kugona n’chokhudzana ndi mkonono. Ngati munagonapo ndi munthu wochita mkonono, mukudziŵa mmene zimasokonezera tulo tanu. Nthaŵi zina mkonono umasonyeza kuti munthu ali ndi matenda enaake amene amachititsa kuti azipuma mobanika chifukwa mpweya umalephera kuloŵa bwinobwino kukhosi kuti ukafike m’mapapo. Kuti vutoli lithe, choyamba munthu ayenera kuwondako pang’ono, kusiya mowa, ndi mankhwala ena ofeŵetsa minofu. Komanso madokotala ena angathe kum’patsa munthuyo mankhwala kapena *
tizida tina toika mkamwa kapenanso kumuika pamakina othandiza kupuma bwino.Zikavuta kwambiri amatha kungochita opaleshoni yokonza kukhosi, chibwano, lilime, kapena mphuno kuti mpweya uzidutsa bwinobwino munthuyo akamapuma.
Ana nawo amatha kukhala ndi vuto la kugona. Angadziŵikire kusukulu kuti ali ndi vutoli ngati sakhoza bwino, ngati amangonyong’onyeka, komanso ngati samvetsera m’kalasi, ndipo nthaŵi zina zimenezi kuchipatala amatha kuzisokoneza ndi matenda a kusakhazikika maganizo.
Ana ena amachita kulimbana nato tulo, pofuna kuimba nyimbo, kucheza, kapena kumvetsera nthano, kapenanso kuchita china chilichonse mmalo moti akagone. Mwina amatero ponyadira makolo awo. Koma nthaŵi zina mwana amaopa kukagona chifukwa cholotalota zinthu zoopsa za m’mafilimu, za m’nkhani zosonyeza chiwawa, kapena chifukwa cha mikangano ya panyumbapo. Makolo angathandize kupeŵa zimenezi poonetsetsa kuti panyumba pawo pali mtendere. Ngati vuto la kugonali likupitirira ingothamangirani kuchipatala basi. Inde, ana ndi akulu omwe amafunika kugona bwino.
Zimene Mungachite Kuti Muzigona Bwino
Kuyambira kalekale anthu akhala akudziŵa kuti tulo tabwino sitibwera tokha ayi. Tulo tabwino timalira kuchita zinthu zambiri kuphatikizapo kusada nkhaŵa ndiponso kusadzitopetsa kwambiri.
Kugona bwino kumafunika kukhala ndi zizoloŵezi zabwino. M’pofunika kumachita zinthu zolimbitsa thupi panthaŵi yoyenera. Kuchita zinthu zolimbitsa thupi m’maŵa kapena madzulo kungathandize munthu kuti akhale ndi tulo panthaŵi yokagona. Koma kuchita zinthu zolimbitsa thupi mutangotsala pang’ono kukagona kumatha kuthaŵitsa tulo.
Kuonera mafilimu otenga mtima kapena kuŵerenga mabuku ochititsa chidwi kwambiri kungathenso
kuthaŵitsa tulo. Musanakagone, ndi bwino kuŵerenga buku lokhazikitsa pansi maganizo, kumvera tinyimbo tabwinotabwino, kapena kusamba madzi ofunda bwino.Akatswiri a za kugona amati mungathe kudziphunzitsa kuti mukangoona bedi muzifuna kugona. Ndipo mungatero posakhala pabedi pokhapokha mukafunadi kugona. Anthu amene amadya, kuŵerenga, kugwira ntchito, kuonera TV, kapena kuchita maseŵera a pa vidiyo ali pabedi amavutika kuti agone.
Kuti thupi lanu likonzekere kugona bwino m’pofunikanso kusamala ndi zakudya. N’zoona kuti mowa umam’patsa munthu tulo, koma tulo take sitikhala tabwino ayi. Usiku, osamwa khofi, tiyi, koko, chokoleti, ndiponso zakumwa monga Kokakola chifukwa zimathaŵitsa tulo. Komano, kudyako pang’ono chabe zinthu monga mango, mbatata, nthochi, mtedza, ndi zinthu zina zotere kumachititsa kuti thupi lipange timadzi tambiri tochititsa tulo. Koma nali chenjezo: Kugona mutakhuta kwambiri n’chimodzimodzi n’kugona ndi njala, tulo sitibwera ayi.
Chinanso chofunika kwambiri ndi malo amene timagona. Tulo sitivuta kubwera ngati mukugona malo osatentha kapena kuzizira kwambiri, m’chipinda mosawala kwambiri ndiponso mosasokosa, komanso pogona pabwino. Ndipotu mukagona malo abwino chonchi mungachite kuiwalako zodzuka kukacha. Komatu musaiwale kuti kugonereza, ngakhale Loŵeruka kapena Lamlungu, kungathe kukusokonezerani kagonedwe n’kuchititsa kuti muvutike kugona usiku wotsatira.
Munthu sangadzivulaze dala mbali yofunika ya thupi lake. Nakonso kugona ndi mbali yofunika ya moyo wathu ndipo si bwino kukunyalanyaza. Ndiponsotu nthaŵi yaitali m’moyo wathuwu imakhala yogona. Ndiyeno, kodi mungathe kusintha kuti muzigona bwino? Yambanitu lerolo!
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Tikati munthu ali ndi vuto la kugona ndiye kuti satha kugona bwinobwino ndiponso mokwanira.
^ ndime 9 Munthuyo amagona kumaso kwake atavalako chinthu chotulukira mpweya wochokera m’makinaŵa n’kudzera m’paipi yotha kupindikira mbali iliyonse. Mpweya umenewu umathandiza kuti munthuyo asabanike ndiponso kuti azipuma bwinobwino.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 15]
ZINTHU ZIKULUZIKULU ZOCHITITSA VUTO LA KUGONA
▪ MATENDA: osokonezeka maganizo; omabanikira kutulo; ogwedezeka miyendo mukagona; ofooka manja ndi miyendo; omva thupili kuyendayenda n’kumangodzidzimuka; chifuwa cha mphumu; matenda a mtima ndiponso mavuto a m’mimba
▪ KUSOKONEKERA MUTU: kuvutika maganizo, nkhaŵa, mantha aakulu, kufuna kutsimikizira kambirimbiri chilichonse chimene mwachita, vuto lokhala ndi mantha mukakumbukira zoopsa
▪ MALO AMENE MUMAGONA: kuwala, phokoso, kutentha, kuzizira, pogona poipa, ngati mkazi kapena mwamuna wanu amangoti fulukutufulukutu akagona
▪ ZINTHU ZINA: mowa ndiponso mankhwala ozunguza ubongo komanso mphamvu ya mankhwala a matenda ena ake
[Bokosi patsamba 15]
MMENE AMADZIŴIRA KUTI MUNTHU ALI NDI VUTO LA KUGONA
Pali njira yodziŵira ngati munthu ali ndi vuto la kugona. Amam’pima ndi zipangizo zosiyanasiyana panthaŵi imene wagona bwino kwambiri.
▪ Pali chipangizo chimene chimajambula mmene ubongo ukugwirira ntchito chomwe chimapima nthaŵi yonse imene munthu wakhala ali mtulo.
▪ China chimajambula mmene maso akuyendera munthu akakhala mtulo.
▪ Chinanso chimapima mmene minofu ya chibwano ndiponso miyendo yaumira kapena mmene yafeŵera pamene munthuyo ali mtulo.
▪ Palinso china chimene chimapima mmene mtima ukugundira usiku wonse.
▪ Amapimanso mmene mpweya umene munthu akupuma ukuyendera m’thupi. Amatero poona mmene mpweya ukuloŵera mphuno ndi mkamwa komanso mmene mimba ndiponso chifuwa zikutugumukira.
▪ Komanso amapima kuchuluka kwa mpweya m’mitsempha ya magazi pogwiritsira ntchito chida chimene amachiika ku chala cha munthuyo.
[Bokosi patsamba 16]
KUYESA MMENE MUMAGONERA
Kodi pa zinthu zili m’munsizi ndi ziti zimene mukuona kuti zingakusinzitseni? Manambala amene ali kumapeto kwa zinthuzo akuimira mfundo zinayi zotsatirazi. Chongani nambala imene ikuimira mfundo yomwe mukugwirizana nayo. Mukamaliza wonkhetsani manambala onse mwachongawo.
0 Sindingasinze
1 Mwina ndingasinze
2 Ndingasinze ndithu
3 Mosakayika ndingasinze
a Kukhala pansi n’kumaŵerenga 0 1 2 3
b Kuonera TV 0 1 2 3
c Kungokhala duu pagulu, monga poonera 0 1 2 3
zisudzo kapena pamsonkhano
d Kukwera nawo galimoto kwa ola lathunthu 0 1 2 3
popanda kuima
e Kungokhala duu mutatha kudya masana 0 1 2 3
popanda kumwako mowa
f Kukhala chogona masana popumula 0 1 2 3
g Kukhala pansi n’kumacheza 0 1 2 3
h Kukhala m’galimoto yoima podikirira galimoto zina 0 1 2 3
Kuwonkhetsa ․․․․․․․․․․․
Dziŵani kuti ngati mwapeza
1 mpaka 6: Palibe chodetsa nkhaŵa
7 mpaka 8: Zili bwino ndithu
Kuyambira pa 9: Pitani kuchipatala
[Mawu a Chithunzi]
Anakonza njira imeneyi ndi a yunivesite ya Stanford ku California m’dziko la United States of America
[Chithunzi patsamba 14]
Kusagona mokwanira n’koopsa
[Zithunzi patsamba 17]
Kuchita maseŵera olimbitsa thupi, kuŵerenga, ndi kudyako pang’ono kungakuthandizeni kuti muzigona tulo tokoma