Ukamaudyerera Ubwana Wako
Ukamaudyerera Ubwana Wako
MWANA amadyerera ubwana wake makamaka akamaleredwa bwino. Koma kodi kulera bwino mwana kumafunanji? N’kutheka kuti mwamvapo malangizo okhudza nkhani imeneyi monga akuti: Muzipatula nthaŵi yokhalako ndi ana anu. Amvetsereni. Alangizeni bwinobwino. Amvereni madandaulo awo ndiponso zimene zimawakondweretsa. Khalani bwenzi lawo lenileni koma musaiwaliretu zoti ndinu kholo lawobe. Inde, makolo angathandizidwe kwambiri kuchita bwino udindo wawo pogwiritsira ntchito mfundo zimenezi zomwe anthu ambiri amakonda kuzitchula. Komabe pali chinthu china chofunika kwambiri kuposa zonsezi.
Padziko lonse makolo ambiri aona kuti chofunika kwambiri pa kulera bwino mwana ndicho kutsatira mfundo za m’Baibulo. N’chifukwa chiyani amatero? Chifukwa chakuti Mlembi wanzeru wa Baibulo, Yehova Mulungu, ndiye anayambitsa banja. (Genesis 1:27, 28; 2:18-24; Aefeso 3:15) Ndiyetu n’zoonekeratu kuti njira yabwino kwambiri yodziŵira mmene mungalelere ana ndiyo kufufuza m’Mawu ake ouziridwa. Komano, kodi Baibulo, lomwe ndi buku lakalekale, lingatilangize motani pa za khalidwe la masiku ano lofulumizitsa ana kumachita zachikulu? Tiyeni tioneko mfundo zina za m’Malemba zokhudza nkhaniyi.
“Monga mwa Mayendedwe a Ana”
Yakobo, mwana wa Isake, anali ndi ana oposa 12. M’Baibulo muli mawu anzeru omwe iye ananena okhudza ulendo winawake womwe banja lake linayenda. Mawuwo ndi akuti: ‘Ana ali ambowa, . . . Mbuyanga [Esau, mkulu wake wa Yakobo] atsogoleretu kapolo wake, ndipo ine ndidzayenda pang’onopang’ono, . . . monga mwa mayendedwe a ana.’—Genesis 33:13, 14.
Yakobo ankadziŵa kuti ana ake sangachite zinthu ngati anthu aakulu. Anali “ambowa,” kapena kuti anthete, ang’onoang’ono, opanda mphamvu, ndiponso ofunika chisamaliro chachikulu kusiyana ndi anthu akuluakulu. Mmalo mokakamiza ana ake kuti aziyenda ngati mmene iye akuyendera, anali kuyenda pang’onopang’ono mogwirizana ndi kayendedwe ka anawo. Mwa kuchita zimenezi iye anasonyeza nzeru zimene Mulungu amasonyeza kwa ana ake apadziko lapansi. Atate wathu wa kumwamba amadziŵa zomwe tingathe kuchita ndiponso zomwe sitingathe. Satiyembekezera kuchita zinthu zomwe sitingathe.—Salmo 103:13, 14.
Ngakhale zinyama zina zimasonyeza nzeru zoterozo, chifukwa chakuti Mulungu anazipanga kuti zikhale “zanzeru.” (Miyambo 30:24) Mwachitsanzo, akatswiri a zachilengedwe anapeza kuti gulu la njovu limayenda mogwirizana ndi kamwana ka njovu komwe kali pagululo. Limayenda pang’onopang’ono mpaka kamwanako katazoloŵera kuyenda.
Anthu ena masiku ano satsatira nzeru za Mulungu. Koma inu musatengere zimenezo. Kumbukirani kuti mwana wanu ndi wanthete, sangathe Miyambo 17:17.
kuchita zinthu zomwe anthu akuluakulu amachita. Mwachitsanzo, ngati mwana wanu mukumulera popanda mayi kapena bambo wake ndipo muli ndi vuto linalake lomwe mukulakalaka mutam’fotokozera, peŵani kuchita zimenezo. Mmalo mwake pezani mnzanu wachikulire amene angakuthandizeni vutolo, makamaka atakhala munthu amene angakuthandizeni kugwiritsira ntchito malangizo anzeru a m’Baibulo.—Moteronso, mwana wanu musamamuunjikire mavuto, kum’panikiza ndi ntchito, mpaka kusoŵa popumira, moti n’kumalephera kusangalala ndi ubwana wake. Chitani zinthu zoyenererana ndi mwana wanuyo, osati mongotengera zimene anthu akuchita masiku ano. Baibulo limalangiza mwanzeru kuti: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano.”—Aroma 12:2.
“Kanthu Kali Konse Kali ndi Nthaŵi Yake”
Mfundo ina yanzeru ya m’Baibulo imati: “Kanthu kali konse kali ndi nthaŵi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pa thambo chili ndi mphindi yake.” N’zoona kuti pali nthaŵi yogwira ntchito. Ana amakhala ndi zambiri zochita, monga ntchito za kusukulu, ntchito za pakhomo, ndiponso ntchito zauzimu. Komabe, Baibulo, pa mfundo yomweyo limapitiriza kunena kuti palinso “mphindi yakuseka” ndi “mphindi yakuvina.”—Mlaliki 3:1, 4.
Ana amafunika kwambiri kukhala ndi nthaŵi yoti aziseŵera, kuseka, kusangalala ndi nyonga zawo, opanda nkhaŵa zilizonse. Ngati amati akangodzuka amapita kusukulu, akabwerako n’kupitanso kukaphunzira zina ndi zina, ndiponso kugwira ntchito zina zikuluzikulu, anawo sangapeze nthaŵi yoseŵera. Zimenezi zingawadandaulitse, mwinanso kuwatayitsa mtima kumene.—Akolose 3:21.
Taonani mmene tingagwiritsire ntchito mfundo yomweyi m’njira zinanso. Mwachitsanzo, popeza kuti kanthu kalikonse kali ndi nthaŵi yake, kodi sizikusonyeza kuti munthu ukakhala mwana ndiye kuti ndi nthaŵi yodyerera ubwana wako? Mwina mukuvomereza kuti inde, koma nthaŵi zina mwana wanu angakane zimenezi. Nthaŵi zambiri, anyamata ndi atsikana ang’onoang’ono amafuna kuchita zinthu zomwe amaona anthu akuluakulu akuchita. Mwachitsanzo, atsikana ang’onoang’ono angamalakelake kuvala ndi kumaoneka ngati azimayi. Kutha msinkhu adakali ang’onoang’ono kungalimbikitse maganizo ofuna kumaoneka ngati achikulire.
Makolo anzeru amaona kuti kuchita zimenezi n’koopsa. Akamatsatsa malonda ena komanso zosangalatsa zina m’dziko lopanda mkhalidweli amawaonetsa anawo ngati anthu odziŵa bwino zogonana ndiponso oganiza mwachikulu. Atsikana ang’onoang’ono ambiri akumadzola zodzoladzola, kuvala zinthu monga mphete ndi zibangiri, komanso zovala zokopa amuna. Koma n’kuloleranji kuti ana azioneka mokopa kwa anthu oipa omwe kwawo n’kungofuna kuwagona anawo basi? Mwa kuthandiza ana kumavala mogwirizana ndi msinkhu wawo, makolo amagwiritsira ntchito mfundo ina ya m’Baibulo yakuti: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.”—Chitsanzo chinanso ndi ichi: Kulola mwana kuona kuti maseŵera ndiwo chinthu chofunika kwambiri kungam’pangitse kukhala ndi moyo wosaganizira mfundo yakuti chilichonse chili ndi nthaŵi yake. Baibulo limalangiza bwino kuti: “Chizoloŵezi cha thupi chipindula pang’ono, koma chipembedzo chipindula zonse, popeza chikhala nalo lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.”—1 Timoteo 4:8.
Musalole kuti ana anu azikhulupirira kuti kupambana ndiye kofunika kwambiri. Makolo ambiri amapangitsa kuti masewera asamasangalatse pokakamiza ana awo kuti akhale akatswiri pa maseŵerawo, kuti azipambana zivute zitani. Motero ana ena amakakamizika kuchita zachinyengo kapenanso kuvulaza anzawo n’cholinga choti apambane. Kunena zoona, munthu kuti apambane safunika kuchita zoipa zoterozo!
Kuphunzira Kudziletsa
Nthaŵi zambiri ana amavutika kuphunzira kuti kanthu kali konse kali ndi nthaŵi yake. Akamafuna chinthu chinachake, zimawavuta kwambiri kuyembekezera modekha. Chomwe chikuipitsanso zinthu kwambiri n’chakuti zikuoneka kuti anthu ambiri ali ndi mtima wa papsa tonola. Nthaŵi zambiri, ofalitsa nkhani zokhudza zinthu zosangalatsa amapereka uthenga wakuti, “Pezani zimene mtima wanu wafuna ndipo muzipeze nthaŵi yomweyino!”
Musalole kuti zimenezi zikupusitseni n’kuyamba kusasatitsa ana anu. “Kulola kupitidwako zinthu zina kumasonyeza kuti munthuyo ndi wololera komanso wougwira mtima,” limatero buku lofotokoza za ana lakuti The Child and the Machine. Bukuli limanenanso kuti: “Kudziletsa ndiponso kuchita zinthu zogwirizana ndi anthu ena kuli ngati mankhwala amphamvu othetsera ziwawa zambiri zomwe zikuchitika pakati pa achinyamata kusukulu komanso panthaŵi yomwe sali kusukulu.” Pa Miyambo 29:21, Baibulo lili ndi mfundo yothandiza kwambiri yakuti, munthu wosasatitsa wantchito kuyambira ubwana wake, wantchitoyo pambuyo pake amadzakhala wantchito wosayamikira zimene mumam’chitira. Ngakhale kuti lembali likunena makamaka mmene munthu angakhalire ndi wantchito wake wachinyamata, makolo ambiri aona kuti mfundoyi imawathandizanso kwambiri ana awo.
Zina zofunika kwambiri kwa ana ndi zimene Baibulo limati ‘maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.’ (Aefeso 6:4) Kulangiza ana mwachikondi kumawathandiza kukhala odziletsa ndi odekha. Makhalidwe ameneŵa adzawathandiza kukhala mosangalala ndiponso okhutira m’moyo wawo wonse.
Zonse Zosokoneza Ubwana wa Munthu Zikadzatha
Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi Mulungu wachikondi ndiponso wanzeru, amene anauzira mfundo zothandiza kwambiri zimenezi ankafuna kuti dziko lathuli likhale mmene lililimu? Kodi ankafuna kuti ana azikulira m’dziko lomwe nthaŵi zambiri lili ndi mavuto ambiri mmalo mokhala ndi zosangalatsa zochuluka?’ Mungalimbikitsidwe kudziŵa kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Kristu Yesu, amakonda kwambiri anthu, kuphatikizapo ana a misinkhu yonse. Posachedwapa adzachotsa kuipa konse padzikoli.—Salmo 37:10, 11.
Kodi mungakonde kukhala ndi chithunzithunzi cha nthaŵi ya mtendere ndi yosangalatsa imeneyo? Tangoganizani izi, zomwe zinafotokozedwa bwino kwambiri m’Baibulo zakuti: “Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalungwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango ndi choŵeta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera.” (Yesaya 11:6) Pano, pakati pa anthu omwe nthaŵi zambiri amasokoneza ubwana wa munthu mwankhanza kapena kufulumizitsa mwana kumachita zachikulu mopanda chifundo, kudziŵa kuti Mulungu akulonjeza kuti anthu adzakhala mosangalala kwambiri padziko pano n’kolimbikitsa kwambiri! N’zoonekeratu kuti Mlengi safuna kuti ana asamadyerere ubwana wawo kapenanso kuti wina aziwafulumizitsa kumachita zachikulu, koma kuti azisangalala ndi kuudyerera bwinobwino ubwanawo.
[Chithunzi patsamba 18]
Mmalo movutitsa mwana wanu ndi mavuto anu, kambiranani ndi wachikulire mnzanu
[Chithunzi pamasamba 18, 19]
Ana amafunika aziseŵerako