Mmene Mungapezere Tulo Tokwanira
Mmene Mungapezere Tulo Tokwanira
ZINTHU zambiri zokhudza mmene tulo timakhalira zadziŵika pa zaka 50 zangothazi. Zimene zadziŵika n’zotsutsana ndi mfundo zimene zakhalapo kwa nthaŵi yaitali. Mfundo imodzi yotere n’njakuti tulo timangothandiza kuti thupi lipumeko basi chifukwa munthu akagona zochitika zambiri zam’thupi zimachitika mwapang’onopang’ono.
Pofufuza mmene ubongo umayendera ukamagwira ntchito, a zachipatala aphunzirapo kuti tulo tili m’magawomagawo amene amachitika mobwerezabwereza. Ubongo wa anthu sikuti umangokhala ayi, m’malo mwake m’magawo ena a tulo umakhala ukugwira ntchito kwambiri. Munthu akagona tulo tabwino, usiku uliwonse amayenera kumaliza magawo atuloŵa n’kubwereramonso mwina nthaŵi zinayi kapena kuposa pamenepo ndipo ayenera kugona nthaŵi yokwanira ndithu pa gawo lililonse.
Kugona N’kovuta Kukumvetsa
Tulo tabwino timagaŵidwa mosavuta m’magawo aŵiri: gawo lolota ndi gawo limene munthu salota. Mungathe kudziŵa kuti munthu ali m’gawo lolota ngati maso ake akuoneka kuyendayenda.
Gawo losalota tingathenso kuligaŵa m’magawo ena anayi. Mukangogona kumene, pang’onopang’ono mumayamba kuloŵa m’gawo loyamba limene mumakhala mutangoyamba katulo. Panthaŵi imeneyi minofu yanu imamasuka kwambiri ndipo muubongo mwanu mphamvu zimayenda modukizadukiza koma mwamsangamsanga. Usiku uliwonse zimenezi zimachitika kwa masekondi 30 kapena mpaka mphindi 7 pa nthaŵi yoyamba kuchitika. Mukaloŵa
m’gawo lachiŵiri la tulo, lomwe limatchedwa kuti tulo teniteni, mphamvu za muubongo mwanu zimachuluka, ndipo m’gawo limeneli mumakhalamo 20 peresenti ya nthaŵi yanu yogona. Mumatha kuganiza kapena kuona zinthu modukizadukiza koma simutha kudziŵa zimene zikukuchitikirani ndipo simungathe kuona ngakhale maso anu atakhala otseguka.Kenaka mumaloŵa m’gawo lachitatu lomwe tulo timakutengani kwambiri ndipo limaphera m’gawo lachinayi la tulo tofa nato. M’gawo limeneli, muubongo wanu mphamvu zimachuluka koma zimayenda mwapang’onopang’ono. Nthaŵi imeneyi ndiyo imakhala yovuta kwambiri kuti munthu akudzutseni chifukwa chakuti magazi anu ambiri amakhala ali m’minofu yanu. Panthaŵi imeneyi (yomwe nthaŵi zambiri imakhala theka la nthaŵi yanu yogona), thupi lanu limakhala likudzikonza malo amene awonongeka ndiponso m’pamene matupi a ana amakula. Ndi bwino kudziŵa kuti aliyense amene tulo take sitifika pamenepa, kaya ndi wachinyamata kaya ndi munthu wamkulu, akadzuka maŵa lake, nthaŵi zambiri amakhala wotopa, wamphwayi, kapenanso wosasangalala.
Potsiriza, gawo lonse losalota likatha pamabwera gawo lolota losiyana kwambiri ndi magawo ena olota amene achitikapo kale. M’gawo lolotali (lomwe limayamba pakatha mphindi 90 zilizonse), muubongo mumayamba kuchuluka magazi ndipo ubongo wanu umakhala ndi mphamvu zofanana ndi zimene umakhala nazo mukakhala maso. Komano simungathe kuyendetsa ziwalo zanu. Zimenezi zimathandiza kuti musamachitedi zinthu zimene mukulota chifukwa mungathe kudzivulaza kapena kuvulaza anzanu.
Magawo olotaŵa amamka natalika nthaŵi iliyonse imene ayambanso kuchitika ndipo zikuoneka kuti amathandiza kwambiri kuti munthu aziganiza bwino. Mofanana ndi kompyuta, ubongo umasanthula nkhokwe yake yonse yosungiramo zinthu zimene zangoloŵamo kumene, n’kuchotsamo zosafunika n’kusunga zimene zili zofunika kuzikumbukira kwa nthaŵi yaitali. Ngati tulo ta munthu sitikhalitsa m’gawo lolotali akuti amayamba kusokonezeka maganizo. Mwachitsanzo, anthu okhala ndi vuto lolephera kugona sakhala nthaŵi yaitali pa gawo lolotali, motero nkhaŵa zimawachulukira kwambiri.
Ndiyeno kodi chimachitika n’chiyani ngati sitigona mokwanira nthaŵi zambiri (kaya mofuna kapena mosachita kufuna)? Ngati timagona maola osakwanira, timadzichepetsera gawo lomaliza la tulo tolota, lomwe limakhala lalitali kwambiri ndipo n’lofunika kuti munthu aziganiza bwinobwino. Ngati timakonda kugona tulo todukizadukiza, mwina kumangogona kwa kanthaŵi kochepa kenaka n’kudzuka, nthaŵi zambiri tulo tathu sitifika pa gawo lija la tulo tofa nato, pomwe m’pofunika kuti thupi lathu lidzizikonza. Anthu amene akhala asakugona mokwanira kwa nthaŵi yaitali amavutika kuika maganizo pa chinthu chinachake kwa nthaŵi yaitali, amavutika kukumbukira zinthu komanso mawu, satha kutsata nkhani bwinobwino, ndiponso satha kuchita zinthu zaluso.
Kodi n’chiyani chimachititsa kuti thupi lifune kugona? Pali zinthu zingapo zimene zikuoneka kuti zimachititsa munthu kufuna kugona ndiponso kudzuka. Zikuoneka kuti timadzi tokhala
muubongo timakhudzanso zinthu zimenezi. Komanso, muubongomu muli malo enaake pamene pamakumana maselo amene amalamulira tulo m’thupi lathu. Malo ameneŵa ali pafupi ndi malo amene mitsempha yopita kumaso imakumanapo. Motero kuwala kumakhudza tulo tathu. Kuwala kwambiri kumathaŵitsa tulo ndipo mdima umayambitsa tulo.Katenthedwe ka thupi lanu n’kofunikanso. Nthaŵi imene thupi lanu limatentha kwambiri, imene nthaŵi zambiri imakhala cha kum’maŵa ndiponso cha kumadzulo, ndi imene mumakhala ogalamuka kwambiri. Thupi lanu likayamba kuzizira , mumayamba kumva tulo kwambiri. Ofufuza amavomerezana pamfundo yakuti anthu amasiyanasiyana pankhani ya kukhala maso ndi kugona.
Kodi Mumafunikira Kugona Tulo Tambiri Motani?
Asayansi amatiuza kuti anthu ambiri amafunikira kugona kwa maola pafupifupi eyiti usiku uliwonse. Koma zimene ofufuza apeza zikuonetsa kuti anthu amasiyanasiyana pankhaniyi.
Mutadzipenda nokha moona mtima mungathe kudziŵa ngati mumagona tulo tokwanira kapena ayi. Odziŵa bwino nkhaniyi nthaŵi zambiri amagwirizana kuti izi ndizo zizindikiro zakuti munthu amagona tulo tokwanira:
▪ Tulo timangobwera mosavuta popanda kumwa mankhwala kapena kuvutika kaye ndi maganizo osoŵetsa tulo.
▪ Simudziŵa kuti munadzuka pakati pausiku, ndipo ngati mutatero, mumatha kugonanso mwamsanga.
▪ Mumadzuka nthaŵi yanu yodzuka ikangokwana m’maŵa uliwonse ndipo nthaŵi zambiri simuchita kutchera wotchi yokudzutsani.
▪ Mukangodzuka n’kuyamba kuyendayenda, mumakhala wogalamuka ndiponso simukhala ndi tulo kwenikweni tsiku lonse.
Zimene Zingakuthandizeni
Nanga kodi anthu amene nthaŵi zina amalephera kugona angatani? Akatswiri ena anatchulapo malangizo othandiza aŵa:
1. Nthaŵi yogona ikayandikira, peŵani zakumwa zoledzeretsa komanso zakumwa zina zopha tulo monga khofi kapena tiyi. Anthu ambiri amadzinamiza poganiza kuti moŵa ungawathandize kugona. Komano achipatala anapeza kuti pamapeto pake moŵawo umathaŵitsanso tuloto.
2. Siyani Kusuta. Buku lina linati: “Anthu osuta fodya amavutika kwambiri kuti agone chifukwa chakuti fodya amawonjezera kuthamanga kwa magazi, amachititsa kuti mtima uzigunda kwambiri, ndiponso kuti ubongo uyambe kuchulukidwa zochita. Anthu osuta fodya amakondanso
kwambiri kudzuka usiku, mwina chifukwa cha chibaba chofuna kusuta.”3. Peŵani kuchita zinthu zolemetsa kwambiri kapena kuganiza kwambiri mutatsala pang’ono kugona. Maseŵera olimbitsa thupi amathandiza munthu kupuma bwino koma sizitero ngati mwachita maseŵeraŵa mutangotsala pang’ono kugona. Kulimbana ndi mavuto akuluakulu kapena zinthu zina zofunika kuganiza kwambiri mutangotsala pang’ono kugona, kungathe kusokoneza thupi lanu n’kuthaŵitsa tulo.
4. Onetsetsani kuti m’chipinda chanu chogona ndi mopanda phokoso, mwamdima ndiponso ngati n’kotheka, mozizirako ndithu. Pankhani ya phokoso, taganizirani kafukufuku wina wotchuka kwambiri wa anthu okhala pafupi ndi bwalo lina landege amene ankanena kuti anasiya kumva phokoso la ndegezo. Ataunika zimene amachita akagona kuti aone mmene tulo tawo timakhalira, anapeza kuti ubongo wawo unkaonetsa kuti ankadzidzimuka ndithu nthaŵi iliyonse ndege ikamatera komanso ikamanyamuka! Ofufuzawo ananena kuti zimenezi zikusonyeza kuti anthuwo ankagona mopereŵera ndi ola limodzi powayerekezera ndi anzawo ogona m’madera opanda phokoso. Zinthu zotsekera m’makutu kapena njira zina zochepetsera phokoso zikanawathandiza kwambiri kuti azigona tulo tabwino. Anthu ena amaona kuti phokoso lochepa longomveka chapansipansi, monga la fani yamagetsi, n’lothandiza kwambiri ngati mukufuna kuti musamamve phokoso la mumsewu.
5. Samalani ndi mankhwala Ogonetsa. Pali umboni wochuluka kwambiri wosonyeza kuti mankhwala akuchipatala ambiri atulo amavuta kusiya, amayamba kusagwira ntchito mukamapitiriza kuwamwa, ndiponso amabweretsa mavuto ena oopsa. Mankhwala otereŵa n’ngabwino kuwagwiritsira ntchito kwa nthaŵi yochepa basi.
Popeza kuti vuto losoŵa tulo lingabwere chifukwa chochulukidwa maganizo, akuti njira ina yothandiza kugona tulo tabwino ndiyo kuonetsetsa kuti nthaŵi yoti mwangotsala pang’ono kukagona ikhale yopanda phokoso ndi yosangalatsa. Ndi bwino kuiwalako kaye za mavuto amene mwakumana nawo patsikulo n’kumachita chinthu chinachake chimene mumakonda, monga kuŵerenga. Phindu la malangizo otsatiraŵa ochokera m’Baibulo n’loonekeratu ndiponso n’lalikulu zedi. Malangizowo n’ngakuti: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu . . . udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 26, 27]
Maganizo Ena Olakwika Amene Anthu Ambiri Amakhala Nawo
1. Kumwa zakumwa monga khofi ndiko njira yothandiza kwambiri kuti mukhale maso mukamayendetsa galimoto paulendo wautali.
Ofufuza anapeza kuti oyendetsa galimoto nthaŵi zambiri amadzinamiza pomaganiza kuti alibe tulo pamene kwenikweni ali nato. Ngati mukuyendetsa galimoto usiku chifukwa choti simungachitire mwina, ndibwino kuti pakapita nthaŵi pang’ono muziima pa malo abwino n’kugonako pang’ono (mwina kwa mphindi 15 kapena mpaka 30), kenaka n’kuyenda kapena kuthamangako pang’ono kwinaku mukumadziwongola manja ndiponso miyendo.
2. Ndikamasoŵa tulo usiku, njira yabwino n’kumagonako pang’ono masana.
Mwinadi ena angaone choncho, koma akatswiri ambiri amaona kuti ndi bwino kukhala ndi chizoloŵezi choti tsiku lililonse muzigona kwanthaŵi yaitali usiku wonse. Kugona pang’ono masana (mwina kwa mphindi 15 mpaka 30) kungakuthandizeni kuti mukhale ogalamuka madzulo, popanda kukusokonezerani tulo tausiku. Koma kugonako pang’ono kutatsala maola anayi kuti nthaŵi yogonera ikwane kungathe kusokoneza tulo tausiku.
3. Maloto amene timakumbukira aja amasokoneza tulo tathu.
Maloto (amene amachitika m’gawo lolota lija) n’chizindikiro cha tulo tabwino ndipo nthaŵi zambiri amachitika kanayi kapena kuposapo usiku uliwonse umene wagona bwinobwino. Ofufuza anapeza kuti maloto amene timakumbukira ndi maloto okhawo amene tinadzidzimuka ali m’kati kapena patapita mphindi zochepa malotowo atatha. Komano maloto oopsa, amatha kupangitsa munthu kukhala ndi nkhaŵa moti angavutike kwambiri kuti agonenso.
[Chithunzi pamasamba 24, 25]
Mukagona bwino mumakhala wogalamuka ndiponso simukhala ndi tulo kwenikweni tsiku lonse
[Chithunzi patsamba 25]
Masiku ano asayansi adziŵa kuti tulo tili m’magawo osiyanasiyana
[Chithunzi patsamba 26]
Samalani pankhani yomwa mankhwala ochititsa tulo
[Chithunzi patsamba 27]
Anthu osuta fodya amavutika kwambiri kupeza tulo powayerekezera ndi anthu ena