Mulungu Ali ndi Dzina!
Mulungu Ali ndi Dzina!
Kodi dzina la Mulungu ndani? Anthu onse ali ndi mayina awo. Ndipotu anthu ambiri amapatsa mayina ngakhale ziŵeto zawo! Ndiye kodi sizingakhale zomveka kuti Mulungu akhale ndi dzina? N’zosachita kufunsa kuti anthu amafunika kukhala ndi mayina n’kumatchulana mayinawo. Ndiyeno kodi akakhala Mulungu, ziyenera kusintha? N’zodabwitsa kuti anthu mamiliyoni ambiri amene amati amakhulupirira Mulungu yemwe ndi mwini wa Baibulo satchula dzina lake. Koma dzina la Mulungulo lakhala likudziŵika kwa zaka zambirimbiri. Poŵerenga nkhani zino, muona kuchuluka kwa maulendo amene anthu ambiri ankatchula dzina la Mulungu. Chofunika kwambiri n’chakuti muona zimene Baibulo limanena pankhani ya kufunika kodziŵa dzina Mulungu.
CHA m’ma 1600, mayiko angapo a ku Ulaya ankapanga ndalama za siliva zokhala ndi dzina la Mulungu. Pa ndalama za siliva za ku Germany za mu 1634, panali dzina lakuti Yehova. Anthu ambiri anafika pomatchula ndalama zoterozo kuti masiliva a Yehova, ndipo zinakhala zikugwira ntchito kwa zaka makumi angapo ndithu.
Yehova * ndilo dzina la Mulungu limene lakhala likulembedwa moteromo kwa zaka zambirimbiri. M’chihebri, chinenero chimene pochiŵerenga amayambira kumanja kupita kumanzere, dzinalo limaoneka ndi zilembo zinayi zotere, יהוה. Zilembo zinayi za Chihebri zimenezi amazimasulira kuti YHWH. Dzina la Mulungu lolembedwa moteromo linakhalanso likulembedwa pa ndalama za siliva za ku Ulaya kwa zaka makumi angapo.
Dzina la Mulungu limapezekanso m’makoma, m’zipilala, ndiponso m’zosemasema zosiyanasiyana komanso m’mabuku a nyimbo a matchalitchi ambiri. Malinga ndi kunena kwa buku la ku Germany lotchedwa Brockhaus, akuti panthaŵi inayake chinali chizoloŵezi cha olamulira a Chipulotesitanti kuvala chinthu chinachake chokometseredwa ndi chizindikiro cha dzuŵa ndi zilembo zinayi zoimira dzina la Mulungu. Chizindikiro choterocho chinkakhalanso pa mbendera ndi ndalama za siliva, ndipo ankachitcha chizindikiro cha Yehova ndi Dzuŵa. Apa zikuonekeratu kuti anthu a ku Ulaya okonda kupembedza kwambiri amene analipo m’ma 1600 ndi m’ma 1700 ankadziŵa zoti Mulungu Wamphamvuyonse ali ndi dzina. Komanso chachikulu n’chakuti sankaopa kutchula dzinalo.
Nakonso ku America panthaŵi ya atsamunda dzina la Mulungu silinali chinthu chachilendo. Mwachitsanzo taonani za msilikali amene ankafuna kusintha boma ku America, dzina lake Ethan Allen. Malinga ndi zimene analemba m’mabuku ake, akuti mu 1775 iyeyu analamula adani ake kuti amugonjere “m’dzina la Yehova Wamphamvuyo.” Kenakanso panthaŵi ya ulamuliro wa Abraham Lincoln, alangizi ambiri
ndithu polembera makalata a Lincoln ankatchula mobwerezabwereza dzina la Yehova. Zikalata zina zotchuka ku America zimene zili ndi dzina la Mulungu zilipobe m’malaibulale ambiri kuti anthu onse aziziona. Zimenezi ndi zitsanzo zina zochepa chabe za mmene dzina la Mulugu lakhalira likusonyezedwa mwapadera.Bwanji masiku ano? Kodi anthu aiwala dzina la Mulungu? Ayi ndithu. Mabaibulo ambiri amagwiritsira ntchito dzina la Mulungu m’mavesi ambiri. Buku la Encyclopedia International limafotokoza momveka bwino kuti dzina lakuti Yehova ndiye “katchulidwe kamakono ka dzina la Mulungu lopatulika m’Chihebri.” Buku lina latsopano la The New Encyclopædia Britannica limafotokoza kuti Yehova ndi “dzina la Mulungu limene Ayuda ndi Akristu amanena.”
Mwina mungafunse kuti, ‘Koma kodi za dzina la Mulungu n’zoti anthu masiku ano azichita kukhala nazo chidwi?’ Mwa kulemba m’njira zosiyanasiyana, dzina la Mulungu amalisonyezabe pamalo ambiri ofikapo anthu. Mwachitsanzo, pa mwala wapangodya ya chinyumba china mu mzinda wa New York City m’polembedwa mochita kusema dzina lakuti Yehova. Mu mzinda womwewo, dzinalo analilemba mochititsa kaso m’Chihebri pa siteshoni ina ya pansi panthaka imene sitima zimadutsadutsapo. Komabe, mwina sikulakwa kunena kuti pa anthu masauzande ambirimbiri amene ayendapo m’madera ameneŵa, ndi ochepa okha amene aonapo kuti zolembedwa zimenezo n’zofunika kwambiri.
Kodi dzina la Mulungu ndi lofunika kwa anthu kwanuko? Kapena anthu ambiri potchula Mlengi amangoti “Mulungu” poganiza kuti ndilo dzina lake lenileni? Mwina zimene inuyo mwaonapo n’zakuti anthu ambiri saganizira n’komwe zoti Mulungu angakhale ndi dzina. Bwanji za inu amene? Kodi mumakhala womasuka kutchula dzina la Mulungu lakuti Yehova?
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 Nkhani zino zikusonyeza kalembedwe kosiyanasiyana kokwanira 39 ka dzina lakuti Yehova m’zinenero zoposa 95.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 4]
Mfumu Imene Inapangitsa Dzina la Yehova Kudziŵika
Mu 1852 gulu la amishonale linanyamuka kuchokera ku Hawaii ulendo wopita kuzisumbu za Micronesia. Amishonaleŵa ananyamula kalata yowadziŵikitsa yomwe inali ndi chidindo cha Mfumu Kamehameha yachitatu, yomwe inkalamulira panthaŵiyo kuzisumbu za ku Hawaii. Kalatayi, yomwe poyamba anailemba m’chinenero cha ku Hawaiiko polembera olamulira osiyanasiyana a pazisumbu za ku Pacific, inali ndi mawu ena aŵa: “Anthu amene afika pa zisumbu zanuwo ndi aphunzitsi ophunzitsa za Mulungu Wammwambamwamba, Yehova, omwe akufuna kukudziŵitsani za Mawu Ake kuti mudzapulumutsidwe kwamuyaya. . . . Ndikukulimbikitsani kuti aphunzitsi abwino ameneŵa muwalemekeze ndiponso mugwirizane nawo komanso ndikukulimbikitsani kuti muwamvere malangizo awo. . . . Ndikukulimbikitsaninso kutaya mafano anu onse ndipo Ambuye Yehova akhale Mulungu wanu woti muzimupembedza ndi kumukonda ndipo iye adzakudalitsani ndi kukupulumutsani.”
[Chithunzi]
Mfumu Kamehameha yachitatu
[Mawu a Chithunzi]
Hawaii State Archives
[Chithunzi patsamba 3]
Zilembo zinayi zimenezi n’zimene zimaimira dzina la Mulungu m’Chihebri