Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kufunitsitsa Kusintha Zinthu

Kufunitsitsa Kusintha Zinthu

Kufunitsitsa Kusintha Zinthu

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU GERMANY

“N’kadakhala wamng’ono bwenzi nditayambitsa gulu lofuna kusintha zinthu!”anatero Anna, mayi wa zaka 80 wa ku Germany. “Ndiye mukanasintha chiyani?” Robert anafunsa choncho. “Zinthu zonse!” anayankha motero Anna.

AMBIRI angavomerezane naye Anna. Pa kafukufuku wina ku Germany yemwe anachitika cha m’ma 1993, anapeza kuti anthu aŵiri pa anthu atatu aliwonse amene anawafunsa ananena kuti akuona kuti ‘m’pofunika kuti zinthu ndiponso moyo wa anthu zisinthe kwambiri.’ Mwina zinthu zili chimodzimodzi m’dziko limene mukukhala.

Anthu akatopa ndi zochitika zinazake, nthaŵi zambiri amalonjezedwa kuti zinthu zisintha. Pankhani ya kusintha pa za maphunziro, Frederick Hess, pulofesa wothandizira wa za maphunziro ndi kayendetsedwe ka boma, analemba kuti: “Nthaŵi zambiri zinthu amazisintha mwachiphamaso chabe pofuna kuti anthu mitima ikhazikike pansi.” M’manyuzipepala timaŵerenga mitu ya nkhani yonena za kusintha kwa kayendetsedwe ka zachuma, zaumoyo, zaulimi ndiponso zamalamulo. Timamva za kufuna kusintha kayendetsedwe ka zamaphunziro, zosamalira anthu ovutika, ndi zandende. * Timaŵerengamonso zakuti anthu ena m’matchalitchi akufuna kuti ziphunzitso zisinthe.

Ubwino ndi Kuipa kwa Kusintha Zinthu

Kodi n’chiyani chikuchititsa anthu kufuna kusintha zinthu? Mwachibadwa, anthu onse amafuna kuti pazikhala kusintha pa moyo wawo. Anthu akhala akuyesa kusintha zinthu pogwiritsira ntchito mavoti, ndalama, malamulo, kapenanso zachiwawa zimene. Zonsezi n’chifukwa chakuti anthu amafunitsitsa kwambiri kukhala ndi moyo wabwino, kukonzera ana awo tsogolo labwino, kapena kutembenuza anthu ena onse kuti nawonso azifunitsitsa moyo wabwino, makhalidwe abwino ndiponso chilungamo. Anthu sadzasiya kufuna kusintha zinthu pokhapokha ngati umbuli, matenda, umphaŵi, ndi njala zitadzatheratu.

Ngakhale kuti ambiri amagwirizana nazo, ena sasangalala ndi anthu ofuna kusintha zinthuwo ngakhalenso zolinga zawozo. Anthu ena amafuna kuti zinthu zingokhala mmene zilili; zisasinthe ayi. Iwoŵa amaona kuti amene amafuna kusintha zinthu ndi anthu oganiza mwaphuma ofuna kusintha dzikoli komano zimene akuganizirazo n’zoti sizingatheke n’komwe. Buku lofotokoza za magulu osintha zinthu a ku Germany kuchokera mu 1880 mpaka 1933 lotchedwa Handbuch der deutschen Reformbewegungen linati, anthu ofuna kusintha zinthu “kaŵirikaŵiri amanenedwa, kujambulidwa zithunzi zonyazitsa munthu, ndiponso kusereulidwa. Munthu wina wolemba maseŵero wa ku France, dzina lake Molière, ananena mosereula kuti: “Palibe uchitsiru wina woposa uchitsiru womafuna kusintha zinthu kuti zikhale bwino padziko pano.”

Kodi inuyo mukuiona bwanji nkhaniyi? Kodi kusintha zinthu kungakonze dzikoli? Kapena kodi anthu ofuna kusintha zinthu ndi anthu ongoganiza mwaphuma basi? Nanga bwanji zinthu zimene zinasinthidwa kale? Kodi anthu amene anazisinthawo ndiye kuti anakwanitsa zolinga zawo? Nkhani zotsatirazi zilongosola zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Malingana ndi cholinga chake, magazini ya Galamukani! ‘siloŵerera m’ndale.’ Cholinga cha nkhani ya kusintha zinthuyi ndicho kungowadziŵitsa aŵerengi athu za nkhaniyi ndiponso kuwasonyeza njira yokhayo yomwe ingathetsedi mavuto athu anthufe.