N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Ali Osungulumwa?
N’chifukwa Chiyani Anthu Ambiri Ali Osungulumwa?
MASIKU ano, anthu ambiri ndi osungulumwa. Kusungulumwa kumakhudza anthu a misinkhu yonse ndiponso a mafuko onse, opeza mosiyanasiyana, ndiponso a zikhulupiriro zonse. Kodi munakhalapo osungulumwa? Kodi ndinu osungulumwa panopa? Mfundo n’njakuti, tonsefe panthaŵi inayake tinamvapo kuti tikufunika kukhala ndi munthu wina woti atimvetsere tikamalankhula, atilimbikitse kapena agwirizane ndi mmene tikumvera m’maganizo mwathu, ndiponso asonyeze kuti akumvetsa kuti ndife munthu patokha wosiyana ndi anthu ena onse. Timafuna munthu amene amamvetsa mmene ifeyo timamvera.
Koma kukhala tokhatokha sikutanthauza kuti ndife osungulumwa. Munthu angathe kukhala yekhayekha kwa nthaŵi yaitali, kumasangalala ndi zimene akuchita, popanda kusungulumwa n’komwe. Mosiyana ndi zimenezi, pali anthu ena amene safuna kukhala okhaokha m’pang’onong’ono pomwe. Buku lotanthauzira mawu lotchedwa The American Heritage Dictionary linati: “Kukhala nokhanokha kumatanthauza kusakhala ndi anthu ena koma sikutanthauza kusasangalala. . . . Kusungulumwa nthaŵi zambiri kumatanthauza kuvutika mtima chifukwa chokhala nokhanokha . . . Kusungulumwa kwambiri kumatanthauza kufunitsitsa kukhala ndi munthu wina,” kutanthauza kuti, kuvutika maganizo kapena kusasangalala. Mtima wa munthu wotereyu umafuna kuulimbikitsa mwa kukhala naye ndi kumusonyeza chikondi chochokeradi pansi pa mtima kuti uyambirenso kusangalala.
Kusungulumwa kumasautsa kwambiri ndipo kukhoza kukhala kopweteka zedi. Munthu amamva ngati chinachake chikusoŵeka. Amamva kuti anthu sakufuna kukhala naye, ndipo akumupatula. Tikhoza kumalephera kuganiza bwino ndiponso kukhala ndi mantha. Kodi
munamvapo choncho? Kodi n’chiyani chimayambitsa kusungulumwa?Mavuto ndi zochitika zosiyanasiyana zimakhudzanso anthu m’njira zosiyanasiyana. Mwina mumaona kuti anzanu safuna kukhala nanu chifukwa cha mmene mumaonekera, fuko lanu, kapena chipembedzo chanu. Kusintha kwa zinthu, monga kuyamba kuphunzira pasukulu yatsopano, kuyamba kugwira ntchito yatsopano, kapena kusamukira ku dera, mzinda, kapena dziko latsopano, kungakuchititseni kusungulumwa chifukwa chakuti mukusiya m’mbuyo anthu amene akhala anzanu kwa nthaŵi yaitali. Kumwalira kwa kholo kapena munthu amene munali naye pabanja kungakuchititseni kukhala wosungulumwa, mwina kwa zaka zambiri. Mfundo inanso n’njakuti tikamakula, anzathu kapena anthu odziŵana nawo amasintha, amachepa, kapena amatheratu kumene.
Si nthaŵi zonse pamene ukwati umachititsa kuti munthu akhale wosasungulumwa. Kusamvana kapena kusagwirizana kungachititse mavuto amene angapangitse munthu kukayikakayika ndipo kungachititsenso kuti mwamuna kapena mkazi ndi ana azingokhala okhaokha. Koma kupatulapo kusungulumwa koyamba chifukwa cha imfa ya wokondedwa wathu, kutha kwa ukwati, kapena kukhala tokhatokha mwinanso kusagwirizana maganizo, pali mtundu wina wa kusungulumwa umene ungatikhudze kwambiri. Izi zimachitika ubwenzi wathu ndi Mulungu ukawonongeka ndipo tikumva kuti Mulungu watitaya.
Kodi zinthu zina zimene tazitchula pamwambapa zinayamba zakuchitikiranipo? Kodi zingatheke kuthana ndi kusungulumwa?
[Zithunzi patsamba 4]
Kusintha kwa zinthu m’moyo, monga kuyamba kuphunzira pasukulu yatsopano ndiponso kumwalira kwa munthu amene tinali naye pabanja, kungayambitse kusungulumwa