Kodi Mulungu Amawaganiziradi Ana?
Zimene Baibulo Limanena
Kodi Mulungu Amawaganiziradi Ana?
CHAKA chilichonse, ana ambirimbiri amachitiridwa zinthu zowapezerera, amazunzidwa, ndipo amamenyedwa mwankhanza. Ambiri amagwira ntchito ngati akapolo m’malo oopsa kwambiri. Ena amabedwa n’kukakamizidwa kukhala asilikali kapena mahule. Ana ambiri sakhulupiriranso munthu aliyense chifukwa chogonedwa ndi wachibale wawo kapena kuzunzidwa m’njira zina zankhanza kwambiri.
Choncho m’pomveka kuti anthu ambiri a mtima wabwino amavutika maganizo akaona mmene ana akuvutikira. Ngakhale kuti amavomereza kuti dyera la anthu ndi kuloŵa pansi kwa makhalidwe abwino n’kumene kwachititsa kwambiri kuti ana azizunzidwa choncho, ena zingawavute kukhulupirira kuti Mulungu wachikondi angalole kupanda chilungamo koteroko kuchitika. Angamaone ngati Mulungu wataya ana ameneŵa ndipo mwina sawaganizira n’komwe. Kodi zimenezo n’zoona? Kodi kupezereredwa ndi kuzunzidwa kwa ana komvetsa chisoniku kumatanthauza kuti Mulungu sawaganizira? Kodi Baibulo limati chiyani?
Mulungu Amadana ndi Anthu Ozunza Ana
Yehova Mulungu sanafunepo kuti ana azipezereredwa ndi anthu akuluakulu ankhanza. Kuzunza ana ndi Genesis 3:11-13, 16; Mlaliki 8:9.
chinthu chimodzi choipa kwambiri chimene chinabwera chifukwa choti anthu anapandukira Mulungu m’munda wa Edene. Anthu atakana ulamuliro wa Mulungu m’njira yoteroyo, anayamba kuzunzana mwankhanza.—Mulungu amanyansidwa ndi anthu amene amapezerera anthu ofooka ndi opanda owateteza. Mitundu yambiri yakale imene sinkatumikira Yehova inkapereka ana nsembe, koma ponena za zimenezi Yehova anati: “Sindinauza iwo, sichinaloŵa m’mtima mwanga.” (Yeremiya 7:31) Mulungu anachenjeza anthu ake akale kuti: “Ukawazunza [ana amasiye] ndi kakuti konse, nakandilirira pang’ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwawo; ndi mkwiyo wanga udzayaka.”—Eksodo 22:22-24.
Yehova Amakonda Ana
Timadziŵa kuti Mulungu amakonda ana poona malangizo anzeru amene amapatsa makolo. Ana oleredwa m’banja labwino amakula bwino ndipo amasanduka anthu achikulire okhwima bwino maganizo. Choncho Mlengi wathu anayambitsa ukwati, woti ukhalepo kwa moyo wonse pamene “mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:24) M’Baibulo, anthu okwatirana okha ndi amene amaloledwa kugonana, kuti ngati patabadwa ana adzasamaliridwe bwinobwino m’banja.—Ahebri 13:4.
Malemba amatsindikanso kufunika koti makolo aziphunzitsa ana awo. Baibulo limati: “Ana ndiwo cholandira cha kwa Yehova; chipatso cha m’mimba ndicho mphoto yake. Ana a ubwana wake wa munthu akunga mivi m’dzanja lake la chimphona.” (Salmo 127:3, 4) Ana ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu, ndipo iye amafuna kuti anawo akule mosangalala. Mulungu amalimbikitsa makolo kutsogolera bwino ana awo pa moyo wawo, monga mmene munthu woponya mivi amailunjikira bwino mivi yakeyo. Mawu a Mulungu amalangiza kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.”—Aefeso 6:4.
Njira ina imene Yehova wasonyezera chikondi chake kwa ana ndiyo kuphunzitsa makolo kuteteza ana awo kwa anthu ochita zachiwerewere ndi ana. Mu mtundu wa Israyeli wakale, ngakhale “ana aang’ono” analamulidwa kuti azimvera Chilamulo, chimene chinkasonyeza khalidwe loyenera ndi losayenera la kugonana. (Deuteronomo 31:12; Levitiko 18:6-24) Mulungu amafuna kuti makolo achite zonse zomwe angathe kuti ateteze ana awo kwa munthu aliyense amene angawapezerere kapena kuwazunza.
Pali Chiyembekezo Choti Ana Adzasiya Kuzunzidwa
Chikondi chosatha chimene Yehova ali nacho pa ana chinasonyezedwa bwino kwambiri ndi Yesu Kristu, amene anasonyeza bwino kwambiri khalidwe la Atate wake. (Yohane 5:19) Pamene atumwi a Yesu analetsa makolo kubweretsa ana aang’ono kwa iye poganiza molakwika kuti akumuthandiza, Yesu anawadzudzula kwambiri. Iye anati: “Lolani tiana tidze kwa Ine.” Kenaka, “anatiyangata, natidalitsa.” (Marko 10:13-16) Ana si opanda ntchito pamaso pa Yehova Mulungu kapena Mwana wake.
Ndipo kudzera mwa Mfumu yake yoikidwa, Yesu Kristu, Mulungu posachedwapa adzachitapo kanthu kuthandiza ana amene akuzunzidwa. Anthu adyera ndi okakala mtima amene amapezerera ndi kuzunza anzawo m’dziko lino adzachotsedwa kosatha. (Salmo 37:10, 11) Koma ponena za ofatsa amene amafunafuna Yehova, Baibulo limati: “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.
Pakadali pano, Mulungu amasonyeza chikondi chake mwa kuthandiza mwauzimu ndiponso m’maganizo anthu onse amene amapezereredwa ndi kuzunzidwa. Iye akulonjeza kuti: “Ndidzafuna yotayika, ndi kubweza yopitikitsidwa, ndi kulukira chika yothyoka mwendo, ndi kulimbitsa yodwalayo.” (Ezekieli 34:16) Kudzera m’Mawu ake, mzimu wake woyera, ndi mpingo wachikristu, Yehova amatonthoza ana amene akuzunzika ndiponso amene ali paumphaŵi. N’zosangalatsa kudziŵa kuti panopa, monga momwe adzachitire m’tsogolo, ‘Atate wa zifundo ndi Mulungu wa chitonthozo chonse, amatitonthoza ife m’nsautso yathu yonse.’—2 Akorinto 1:3, 4.
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
© Mikkel Ostergaard /Panos Pictures