Mphaka Amene Ali Pangozi Kwambiri Padziko Lonse Lapansi
Mphaka Amene Ali Pangozi Kwambiri Padziko Lonse Lapansi
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SPAIN
Anthu kwa nthaŵi yaitali adziŵa za maso akuthwa ndi kuchangamuka kwa mphaka wa mtundu wa lynx. Munthu akamamvetsetsa bwino zinthu, anthu a ku Spain amati munthu ameneyo “ali ndi maso a mphaka” ameneyu. Koma n’zomvetsa chisoni kuti tsopano mphaka wa ku Spain ameneyu (Lynx pardinus) akutchuka kaamba ka chifukwa china osati maso ake akuthwa kapena kuchangamuka kwake. Mphaka ameneyu akuti ndi “mphaka amene ali pangozi kwambiri pa amphaka onse a padziko lapansi.” *
Zaka zapitazo, mphakayu ankapezeka ku Portugal ndi ku Spain konse ndipo mwina ankapezekanso mpaka kumapiri a ku France a Pyrenees. Masiku ano, pali magulu otalikirana ochepa okha amene amapezeka kuchigawo chakumwera chakumadzulo kwa dera la ku Ulaya la Spain, Portugal, ndi Gibraltar. Koma ndi magulu aŵiri okha mwa ameneŵa amene ali ndi amphaka ochuluka mokwanira oti angathe kuberekana, ndipo chiŵerengero cha amphaka onse amene alipo chachepa modetsa nkhaŵa kwambiri.
Malinga ndi zimene ena anayerekezera, akuti amphaka a ku Spain ameneŵa tsopano angotsala osakwana ndi 200 omwe. Kodi n’chiyani chachititsa kuti apululuke chonchi? Ena akuti chimene chachititsa kwambiri kuti amphakaŵa athe ndi kutha kwa chakudya chawo chachikulu, amene ali akalulu, omwe apululuka ndi miliri ingapo ya matenda enaake a akalulu. Kuwonjezera apo, amphaka ena aphedwa ndi anthu opha nyama popanda chilolezo kapena agundidwa ndi magalimoto mumsewu. Ndipo malo abwino okhala amphakaŵa akucheperachepera. Lipoti laposachedwapa la bungwe loteteza zachilengedwe lotchedwa World Wildlife Fund linati mavuto ameneŵa achititsa kuti amphaka ochepa amene atsalawo azikhala m’timagulu ting’onoting’ono totalikirana.
Ngakhale kuti pali ndalama zokwana madola 35 miliyoni zimene zaikidwa padera kuti azigwiritse ntchito populumutsa amphakaŵa kuti asatheretu, gulu la akatswiri enaake anati zinthu panopa “sizili bwino.” Malinga ndi zimene ananena Nicolás Guzmán, woyendetsa bungwe lotchedwa National Plan for the Conservation of the Iberian Lynx, akuti pa amphaka osakwana 200 amene atsala panopa, ‘ndi amphaka 22 mpaka 32 okha amene ali aakazi oti angathe kubereka.’ Iye anati, ‘Kupulumuka kwa mtundu umenewu wa amphaka kudzadalira amphaka aakazi ameneŵa.’ N’zomvetsa chisoni kuti zimene zachitikira amphaka a ku Spain ameneŵa n’zofanana ndi zimene zachitikira zinyama zambiri zokongola zapadziko lathuli.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Mphaka wa ku Spain ameneyu anamuika pa gulu la nyama zimene “zili pangozi yaikulu” mu chikalata chotchedwa Red List, chimene amalembapo nyama zimene zatsala pang’ono kutha chokonzedwa ndi bungwe loteteza zachilengedwe lotchedwa International Union for Conservation of Nature and Natural Resources.
[Mawu a Chithunzi patsamba 18]
Foto © Fernando Ortega
sos lynx