Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Sukulu Yamkaka Yopanda Zoseŵeretsa

Sukulu Yamkaka Yopanda Zoseŵeretsa

Sukulu Yamkaka Yopanda Zoseŵeretsa

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU GERMANY

Tsiku lina m’maŵa ana atabwera ku sukulu yamkaka, anapeza kuti makalasi onse anali opanda kanthu ndipo munangotsala mipando ndi matebulo basi. Anafunafuna zidole zosiyanasiyana uku ndi uku, koma sanapeze chilichonse. Munalibenso mabuku kapena timatabwa ndi timapulasitiki toseŵeretsa. Ngakhale mapepala ndi masizasi munalibe. Zidole zonse zinali zitachotsedwa ndipo zinali zoti sazibweretsanso kwa miyezi itatu. Kodi n’chiyani chinali chitachitika?

Sukulu yamkaka imeneyi ndi imodzi mwa masukulu amkaka ambiri a ku Austria, ku Germany, ndi ku Switzerland amene akutenga nawo mbali pa njira yophunzitsira yatsopano ndiponso yotsogola kwambiri yotchedwa Sukulu Yamkaka Yopanda Zoseŵeretsa. Ngakhale kuti zingamveke zodabwitsa, njira yophunzitsira imeneyi, imene akatswiri azaumoyo a m’bungwe la European Union aiyamikira kwambiri, cholinga chake n’kuletsa anthu kuzoloŵera zinthu zoipa. M’zaka zaposachedwapa ochita kafukufuku azindikira kuti, ngati munthu anaphunzira luso locheza bwino ndi anthu ali wamng’ono, zimakhala zovuta kuti akhale ndi chizoloŵezi choipa cha mtundu uliwonse. Lipoti la m’nyuzipepala inayake linati, luso limeneli limaphatikizapo “kulankhula ndi anthu, kumasuka ndi anthu achilendo, kutha kuthetsa kusagwirizana maganizo, kuvomereza zotsatirapo za zochita zako, kukhala ndi zolinga, kuzindikira pakakhala vuto, kupeza thandizo, ndi kupeza njira yothetsera vutolo.” Anthu amene amakhulupirira njira imeneyi akuti luso loterolo liyenera kuyamba munthu akadali wamng’ono kwambiri, ndipo kukhala opanda zoseŵeretsa nthaŵi zina kumathandiza ana kukhala ndi luso loterolo ndiponso kumathandiza anawo kutulukira luso lawo lina losiyanasiyana ndi kuthetsa manyazi.

Zochitika pa miyezi itatu yopanda zoseŵeretsa imeneyi anazikonza mosamala kwambiri ndipo anakambirana zimenezi ndi makolo ndi anawo. Poyamba, ana ena amasoŵa chochita akakhala opanda zoseŵeretsa. Lipotilo linati “pali sukulu zamkaka zina kumene anawo amapulupudza kwambiri milungu inayi yoyambirira,” ndipo aphunzitsi ndi onse amene akuyendetsa nawo ntchitoyi amasoŵa pogwira. Koma ana sachedwa kusintha ndipo amaphunzira kutulukira zinthu zatsopano. Chifukwa chosoŵa zoseŵeretsa, anawo amakambirana, kukonza zinthu, ndi kuseŵerera limodzi kwambiri kuposa kale, ndipo zimenezi zimawathandiza kukulitsa luso lawo locheza ndi anthu ndi lolankhula. Ana ena amene kale sankalankhulitsana ndi anzawo chifukwa chotanganidwa ndi zidole tsopano aphunzira kucheza ndi anzawo. Makolo nawonso aona kuti anawo akusintha. Tsopano amaseŵera bwino ndi anzawo kuposa kale ndipo akutulukira zinthu zatsopano zambiri, anatero makolowo.