Zimene Zimachititsa Moyo Kukhala Wopanikizika ndi Zotsatirapo Zake
Zimene Zimachititsa Moyo Kukhala Wopanikizika ndi Zotsatirapo Zake
KODI moyo umakhala wopanikizika chifukwa chiyani? Katswiri wina anati moyo umakhala wopanikizika chifukwa cha “zochitika zilizonse zimene zimapangitsa munthu kumva kuti thupi lake kapena maganizo ake ali pampanipani, kaya zikhale zochitika kunja kwa thupi lake kapena m’kati mwa thupi lake.” Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kupanikizika kulikonse kumene munthu angamve pamoyo wake n’koipa? Ayi. Monga momwe Dr. Melissa C. Stöppler ananenera, “kumva kupanikizika pang’ono nthawi zina kukhoza kukhala kothandiza. Tikamamva kupanikizika pang’ono pamene tikugwira ntchito inayake nthawi zambiri timaigwira bwino ndiponso timaigwira mwamphamvu.”
Choncho kodi kupanikizika kumakhala koipa kukafika pati? Stöppler anati: “Munthu akapanikizika kwambiri n’kumalephera kuchitapo kanthu kuti asinthe zimenezi m’pamene kupanikizikako kumakhala koipa.” Taonani zinthu zina zimene nthawi zambiri zimachititsa anthu kukhala ndi moyo wopanikizika.
Kupanikizika Pofuna Kupeza Zofunika Pamoyo
Mfumu Solomo anati ndi “chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake.” (Mlaliki 2:24) Komabe, kwa anthu ambiri apantchito, kuntchito n’kumene amakhala pampanipani woopsa.
Lipoti la bungwe la European Agency for Safety and Health at Work linati anthu apantchito nthawi zambiri amapanikizika ndi ntchito yawo pa zifukwa zingapo. Chifukwa chimodzi n’choti sipakhala kulankhulana kokwanira pakati pa mabwana ndi antchito awo. Chifukwa china n’choti mabwana samva kaye maganizo a antchito asanasinthe zinthu zimene zingakhudze antchitowo. Zifukwa zina ndi kusagwirizana ndi antchito anzawo, kuda nkhawa kuti ntchito yawo ikhoza kutha nthawi ina iliyonse, kapena kusalipidwa mokwanira. Kaya chifukwa chake chikhale chotani, kulimbana ndi nkhawa zakuntchito kungachititse makolo apantchito kukhala otopa kwambiri moti sakhala ndi mphamvu zokwanira zoti asamalire mabanja awo. Ndipo mabanja awowo nthawi zina angafunike chisamaliro chachikulu. Mwachitsanzo ku United States, m’chaka chimodzi chinachake anthu pafupifupi 50 miliyoni anali kusamalira munthu wodwala kapena wokalamba wa m’banja mwawo. Mavuto azachuma angachititsenso
kwambiri banja kukhala ndi moyo wopanikizika. Rita, mayi wa ana awiri, anakumana ndi mavuto azachuma pamene mwamuna wake, Leandro, anachita ngozi yagalimoto n’kuyamba kuyendera njinga ya olumala. Rita anati: “Mavuto azachuma amayambitsa nkhawa. Ngati ulibe ndalama zokwanira zolipirira zonse zofunika panyumba, sukhala wosangalala.”Amayi Olera Okha Ana Amakhala Pampanipani Kwambiri
Amayi olera okha ana nawonso amakhala pampanipani pamene akuyesetsa kupezera mabanja awo zofunika pamoyo. Kudzuka m’mawa kuti aphike chakudya, kuveka ana zovala n’kukawasiya kusukulu, kuthamanga kuti akafike nthawi yabwino kuntchito, kenaka n’kuyamba kulimbana ndi mavuto a kuntchito kwawo, kungatopetse kwambiri mayi wolera yekha ana moti angafike polephera kuganiza bwinobwino. Ndipo mayi akaweruka ku ntchito, mpanipani wina umayambikanso pamene akuthamanga kukatenga ana ake kusukulu, kuphika chakudya chamadzulo, ndi kugwira ntchito zapakhomo. María, mayi amene akulera yekha atsikana anayi a zaka zapakati pa 13 ndi 20, anati moyo wake ndi wopanikizika kwambiri moti nthawi zina amamva ngati aphulika.
Ana Opanikizika
Katswiri wina wa chikhalidwe cha anthu dzina lake Ronald L. Pitzer anati: “Achinyamata ambiri amakhala ndi moyo wopanikizika kwambiri.” Amavutika pamene thupi ndi maganizo awo zikusintha chifukwa cha unamwali. Amakumananso ndi mavuto kusukulu. Malinga ndi buku lotchedwa
Childstress!, tsiku lililonse kusukulu “ana amakumana ndi mavuto ndiponso amapanikizika chifukwa cha maphunziro awo, masewera, anzawo, ndi zimene amalankhulana ndi aphunzitsi awo.”Kumadera ena, ana amakhala ndi nkhawa chifukwa choopa kuti achitiridwa zachiwawa kusukulu, kuphatikiza pa mantha amene achinyamata ambiri ali nawo panopa chifukwa cha uchigawenga ndi masoka ena. Mtsikana wina analemba kuti: “Ngati makolo akungokhalira kunena za momwe dzikoli laopsera masiku ano, ifenso tizikhala ndi mantha.”
Makolo ayenera kulimbikitsa ana awo. Koma malinga ndi Pitzer: “Ana ndiponso achinyamata akamayesera kulankhula ndi makolo awo za zinthu zimene zikuwachititsa mantha, nthawi zambiri makolowo amatsutsa zimenezo, kuzichepetsa, kapena kungozinyalanyaza kumene.” Nthawi zina makolo amalephera kuchitapo kanthu chifukwa cha mavuto amene akukumana nawo pa ukwati wawo. Tito, mnyamata winawake wamng’ono amene makolo ake anasudzulana pamapeto pake, anati: “Zinkaoneka ngati makolo anga ankangokhalira kukangana nthawi zonse.” Monga momwe buku la Childstress! likunenera, “kumenyana ndi kukangana si zinthu zokhazo zimene zimachititsa ana kukhala ndi moyo wopanikizika. Makolo akamangokhala ndi mkwiyo, umene umaonekerabe ngakhale aziyesera kulankhulana mawu okoma, ana amavutika maganizo.”
Zotsatirapo za Moyo Wopanikizika
Kaya ndinu achinyamata kapena achikulire, ndipo kaya moyo wanu ndi wopanikizika chifukwa cha ntchito kapena sukulu, kukhala wopanikizika kwa nthawi yaitali kungawononge kwambiri thanzi lanu. Mukamamva kuti mwapanikizika, mtima ndi magazi anu zimathamanga. Shuga amachuluka m’thupi mwanu. Timadzi tinatake ta m’thupi timatuluka n’kupita m’magazi mwanu. Dokotala wina analemba kuti: “Ngati mukukhala wopanikizika kwa nthawi yaitali, zinthu zonse za m’thupi mwanu zimene zimakhudzidwa munthu akapanikizika (ubongo, mtima, mapapo, mitsempha ya magazi, ndi minofu) zimagwira ntchito kwambiri kapena moperewera nthawi zonse. Zimenezi zingawononge thupi kapena maganizo anu pakapita nthawi.” Matenda amene angayambe chifukwa chokhala moyo wopanikizika ndi ambiri, monga matenda a mtima, sitiroko, kusokonezeka kwa chitetezo cha m’thupi, kansa, matenda a minofu ndi mafupa, ndi matenda a shuga, kungotchulapo ochepa chabe.
Zimene zikudetsa nkhawa kwambiri ndi njira imene anthu ambiri, makamaka achinyamata, amayesera kuchepetsera kupanikizika pa moyo wawo. Dr. Bettie B. Youngs anadandaula kuti: “N’zokhumudwitsa kwambiri kuti achinyamata akamafuna kuiwala mavuto awo amayamba kuchita zinthu monga kumwa mowa mwauchidakwa, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kujomba kusukulu, kupulupudza, chiwerewere, chiwawa, ndi kuthawa panyumba. Zinthu zimenezi zimawabweretsera mavuto aakulu kwambiri kuposanso amene amayesera kuthawa aja.”
Masiku ano aliyense amapanikizikako nthawi zina. Ndi mmene moyo wa masiku ano ulili ndipo sitingasinthe zimenezi. Koma monga momwe nkhani yotsatirayi isonyezere, pali zambiri zomwe tingachite kuti tichepetse kupanikizika pa moyo wathu.
[Mawu Otsindika patsamba 6]
Moyo wake ndi wopanikizika kwambiri moti nthawi zina amamva ngati aphulika
[Chithunzi patsamba 5]
Makolo olera okha ana amakhala pampanipani nthawi zambiri
[Chithunzi patsamba 6]
Achinyamata akhoza kupanikizika kwambiri chifukwa cha sukulu