Mmene Zinyama Zimadyetsera ndi Kusamalira Ana Awo
Mmene Zinyama Zimadyetsera ndi Kusamalira Ana Awo
Yolembedwa ndi wolemba Galamukani! ku Spain
ANTHU nthawi zambiri amatha zaka pafupifupi 20 akulera ana awo. Koma nyama zambiri zimafunika kumaliza kudyetsa ndi kuphunzitsa ana awo m’miyezi yochepa chabe m’nyengo yachilimwe. Zitsanzo zingapo zili m’munsizi zisonyeza chintchito chachikulu cholera ana chomwe zinyama zimakhala nacho chaka chilichonse.
1. Indwa Yoyera Indwa yomwe ili pachinthunzipa sikhala ndi nthawi yopuma m’chilimwe. Popeza ili ndi ana ofunika kuwadyetsa, iyenera kupita maulendo ambirimbiri ku nyanja yomwe ili pafupiyo kukafuna achule, nsomba zing’onozing’ono, abuluzi, kapena ziwala. Imafunikanso kukonza chisa chake nthawi ndi nthawi. Makolo onse awiri amapita kokafuna chakudya n’kubwera nacho maulendo ambirimbiri tsiku lonse lathunthu. Ana a mbalamewo amadya zakudya zochuluka kwabasi. Pa milungu ingapo yoyambirira, tsiku lililonse akhoza kudya zakudya zolemera theka la kulemera kwa thupi lawo! Ngakhale zikaphunzira kuuluka, indwa zing’onozing’ono zimadalirabe makolo awo kwa milungu ina ingapo.
2. Kakwiyo Pafupifupi nthawi zonse, kakwiyo wamkazi amalera yekha ana ake. Amafunika agwire nyama yoti adye pafupifupi tsiku lililonse kuti akhute mokwanira akamayamwitsa ana ake, omwe nthawi zambiri amakhalapo atatu mpaka asanu. Zimenezi si zophweka chifukwa nthawi zambiri akamafuna kugwira nyama, amalephera. Kuwonjezera apo, pakatha masiku angapo alionse amafunika asamutsire banja lake kumalo ena chifukwa mikango nthawi zonse imakhala ikufunafuna kudya anawo. Anawo akakwana miyezi seveni, amayamba kuwaphunzitsa kusaka nyama okha. Zimenezi zimafuna nthawi yambiri, ndipo zimatenga mwina chaka chimodzi. Anawo nthawi zambiri amakhala ndi amayi awo kwa chaka chimodzi kapena chaka chimodzi ndi theka.
3. Mbalame yonga bakha yotchedwa little grebe Mbalame zimenezi zimakhala limodzi ndi ana awo nthawi zonse. Ana akangobadwa, amachoka m’zisa zawo za m’madzi n’kukwera pamisana pa makolo awo. Anawo amakwera pamsana pa kholo lawo, pakati pa phiko ndi nthenga zakumbuyo. Akakhala pamenepo amamva kufundira ndiponso amatetezedwa pamene mayi kapena bambo awo akusambira. Makolowo amasinthana ntchito. Wina akamagwira zakudya m’madzi, wina amakhala akusamalira anawo. Ngakhale kuti pakapita nthawi yochepa anapiyewo amaphunzira kupita okha m’madzi kukagwira nsomba zoti adye, amapitirizabe kugwirizana ndi makolo awo kwa nthawi yaitali ndithu.
4. Kadyansonga Akadyansonga nthawi zambiri amakhala ndi mwana mmodzi basi, ndipo n’zosavuta kumvetsa chifukwa chake. Mwana wa kadyansonga wongobadwa kumene, ngati amene ali pachithunzipa, akhoza kulemera makilogalamu 60 ndipo akhoza kutalika mamita awiri! Pakangotha ola limodzi atabadwa, mwana wa kadyansonga amayamba kuyenda ndi kuyamwa mkaka wa mayi ake. Amayamwa kwa miyezi nayini, ngakhale kuti amayamba kudya udzu akangobadwa kumene. Akaona choopsa, mwanayo amathawira pakati pa miyendo ya mayi ake, chifukwa mayi akewo amamuteteza pomenya mwamphamvu zinyama zina ndi miyendo yawo.
5. Mbalame yotchedwa common kingfisher Mbalame zimenezi zikamagwira nsomba zodyetsa ana awo zimafunika kudziwa bwino ntchito yawo ndiponso kusankha bwino nsombazo. Akatswiri ophunzira za mbalame atulukira kuti makolo onse awiri amadyetsa anapiye ongobadwa kumene nsomba zazing’ono zotalika sentimita imodzi kapena masentimita awiri. Khololo limanyamula nsombayo mosamala ndi mulomo
wake, mutu wa nsombayo utaloza kunja. Zimenezi zimathandiza kuti anapiye anjalawo asavutike pomeza, poti amayamba kumeza mutu wansombayo. Anapiyewo akamakula, makolowo amayamba kubweretsa nsomba zokulirapo. Makolowo amayambanso kudyetsa anapiyewo pafupipafupi malinga ndi msinkhu wawo. Poyamba mwanapiye aliyense amamudyetsa pafupifupi mphindi 45 zilizonse. Koma anapiyewo akatha masiku 18, amakhala ndi njala kwambiri, ndipo amawapatsa nsomba mphindi 15 zilizonse! Mbalame yaing’ono yomwe ili pachithunzipa yachoka kale m’chisa mwake ndipo posachedwapa iyamba kugwira yokha nsomba. Mwina mungaganize kuti panopa makolowo apuma kaye pa ntchito yawo yolera ana. Koma mbalame zimenezi sizitero ayi. Nthawi zambiri zimayambiranso chintchito chimenechi poberekanso ana ena chilimwe chomwecho.Mpaka pano pali zinthu zambiri zomwe sitikudziwa zokhudza momwe zinyama zosiyanasiyana zimasamalira ana awo. Koma akatswiri a zachilengedwe akamatulukira zinthu zambiri, m’pamenenso timaona bwino kuti zinyama zikamalera ana awo zimachita zinthu zambiri pongotsatira momwe zinalengedwera. Ngati Mulungu analenga zinyama choncho, mwachidziwikire amafunanso kuti anthu azidyetsa ndi kusamalira ana awo mwachikondi, chifukwa ana amafunika zimenezo.