Ndizigwira Ntchito Yamanja Chifukwa Chiyani?
Achinyamata Akufunsa Kuti . . .
Ndizigwira Ntchito Yamanja Chifukwa Chiyani?
“Sindinkaganiza kuti ndingadzagwire ntchito yamanja. Ndinkangokonda kuseweretsa kompyuta yanga basi.”—Anatero Nathan.
“Ana ena ankatinyoza ife amene tinkagwira ntchito zamanja, ngati kuti tinalibe nzeru zokwanira zoti tikanatha kugwira ntchito za mtundu wina.”—Anatero Sarah.
ANTHU ambiri amaona kuti ntchito yamanja ndi yosasangalatsa, yauve, ndiponso yosasiririka. Pulofesa wina wa zachuma ponena za ntchito zamanja anati: “Ntchito zimenezi zimaoneka zotsika m’dziko la masiku anoli, lomwe limakonda ntchito zapamwamba.” Choncho n’zosadabwitsa kuti achinyamata ambiri amanyansidwa akangoganiza chabe zogwira ntchito yamanja.
Koma Baibulo limatilimbikitsa kuona mwa njira ina kugwira ntchito molimbika. Mfumu Solomo inafunsa kuti: “Kodi si chabwino kuti munthu adye namwe, naonetse moyo wake zabwino m’ntchito yake [yolimba]?” (Mlaliki 2:24) Mu nthawi za m’Baibulo, Aisrayeli anali alimi. Kugalawuza, kukolola, ndi kupuntha kunkafuna kugwira ntchito molimbika. Koma Solomo anati kugwira ntchito molimbika kungabweretse madalitso ambiri.
Patapita zaka zambiri, mtumwi Paulo anati: “Wakubayo asabenso; koma makamaka agwiritse ntchito, nagwire ntchito yokoma ndi manja ake.” (Aefeso 4:28) Paulo mwiniwakeyo ankagwiranso ntchito yamanja. Ngakhale anali munthu wophunzira kwambiri, nthawi zina ankapeza zosowa za pamoyo wake popanga mahema.—Machitidwe 18:1-3.
Kodi kugwira ntchito yamanja mumakuona bwanji? Kaya mukudziwa zimenezo kapena ayi, ntchito yamanja ingakuthandizeni m’njira zambiri.
Kuphunzira Zimenezi Kungakuthandizeni Pamoyo Wanu
Kugwira ntchito yamanja molimbika, kaya pogwiritsa ntchito hamala kapena potchetcha udzu, kungakuthandizeni kukhala ndi thanzi labwino. Mungapindulenso m’njira zina kuwonjezera pa kukhala
ndi thanzi labwino. Kodi mungathe kukonza tayala la njinga likaphwa? Kodi mungakonze windo lowonongeka kapena kukonza paipi ya madzi yotsekeka? Kodi mumatha kuphika? Kodi mungatsuke m’chimbudzi kuti muyere bwino ndiponso mukhale mwaukhondo? Zinthu zimenezi n’zofunika kuti anyamata ndi atsikana azidziwe, chifukwa zingadzakuthandizeni kukhala panokha bwinobwino tsiku lina.N’zochititsa chidwi kuti ngakhale Yesu Kristu akuoneka kuti anaphunzira ntchito zina zamanja ali padziko lapansi pano. Anaphunzira ukalipentala, mosakayikira kwa bambo ake omulera a Yosefe, chifukwa ankatchedwa kalipentala, kapena kuti mmisiri wa mitengo. (Mateyu 13:55; Marko 6:3) Nanunso mungaphunzire ntchito zothandiza zosiyanasiyana pogwira ntchito zamanja.
Mumaphunzira Makhalidwe Abwino
Kugwira ntchito molimbika kungakhudzenso momwe mumadzionera. Polemba nkhani ya bungwe loona za matenda a maganizo lotchedwa U.S. National Mental Health and Education Center, Dr. Fred Provenzano anati kuphunzira kugwira ntchito zamanja kungakuthandizeni kuti “muzidzidalira.” Kuwonjezera apo, “kungakuthandizeni kuti muzidziletsa ndiponso muzichita zinthu mwadongosolo, zimene zingakuthandizeni kuti musavutike kulembedwa ndi kukhazikika pantchito.” Mnyamata wina dzina lake John anati: “Kugwira ntchito yamanja kumakuthandizani kuphunzira kuleza mtima. Mumaphunzira kuthana ndi mavuto.”
Sarah, amene tinamutchula koyambirira uja anati: “Kugwira ntchito yamanja kunandiphunzitsa kugwira ntchito mwakhama. Ndinaphunzira kulamulira maganizo ndi thupi langa.” Kodi nthawi zonse ntchito yamanja imakhala yosasangalatsa? Nathan anati: “Ndinaphunzira kusangalala pogwira ntchito yamanja. Pamene ndinayamba kuidziwa bwino ntchitoyo, ndinaona kuti ndinayamba kupanga zinthu zooneka bwino. Zimenezi zinandithandiza kuyamba kudzidalira.”
Kugwira ntchito yamanja kungakupatseninso chimwemwe chimene chimabwera mukaona zotsatirapo za ntchito yomwe mwagwira. Mnyamata wina dzina lake James anafotokoza zimenezi motere: “Ndimasangalala kuchita ukalipentala. Ngakhale kuti nthawi zina ndimatopa kwambiri, ndikamaliza ndimayang’ana chinthu chomwe ndapangacho ndipo ndimasangalala kwambiri. Zimenezi zimandikhutiritsa kwabasi.” Brian akuvomerezana ndi zimenezi. Iye akuti: “Ndimasangalala kukonza magalimoto. Kudziwa kuti ungathe kukonza chinthu chomwe chawonongeka n’kuchisiya chili bwinobwino ngati chatsopano kumakuchititsa kuti uzidzidalira ndiponso umamva bwino mumtima.”
Utumiki Wopatulika
Kwa anyamata achikristu, kudziwa kugwira ntchito mwakhama kungawathandize pa utumiki wawo kwa Mulungu. Pamene Mfumu Solomo anapatsidwa ntchito yomanga kachisi wokongola kwambiri wa Yehova, anazindikira kuti ntchito imeneyi idzafuna khama ndiponso luso lalikulu. Baibulo limati: “Mfumu Solomo anatuma anthu kukatenga Hiramu ku Turo. Iyeyo anali mwana wake wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafitali, atate wake anali munthu wa ku Turo, mfundi wa mkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira ntchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomo nam’gwirira ntchito zake zonse.”—1 Mafumu 7:13, 14.
Unali mwayi wapadera kwambiri kwa Hiramu kugwiritsa ntchito luso lake kupititsa patsogolo kulambira Yehova. Zimene zinachitikira Hiramu zikusonyeza kuti mawu amene ali m’Baibulo pa Miyambo 22:29 ndi oona. Lemba limenelo limati: “Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.”
Masiku ano, ngakhale achinyamata amene anali ndi luso la zomangamanga pang’ono chabe kapena amene analibiretu luso limeneli atha kukhala ndi mwayi wapadera wothandiza nawo pomanga Nyumba za Ufumu. Chifukwa chogwira nawo ntchito zimenezi, ena aphunzira ntchito zosiyanasiyana monga zamagetsi, zamadzi, zomangamanga, ndi ukalipentala. Mwina mungafunse akulu a mumpingo mwanu ngati nanunso mungathandize nawo pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu.
James, amene wamanga nawo Nyumba za Ufumu zingapo, anati: “Anthu ambiri mumpingo alibe
nthawi yoti angathe kukathandiza nawo kumangako kapena sangathe kutero. Choncho mukathandizapo, ndiye kuti mukuthandiza mpingo wonse wathunthu.” Nathan, amene anaphunzira kukonza konkire, anaona kuti luso limeneli linamutsegulira khomo lotumikira Mulungu m’njira ina. Iye akukumbukira kuti: “Ndinatha kupita ku Zimbabwe n’kukagwiritsa ntchito luso langa kumanga nawo ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova. Ndinagwira ntchito kumeneko kwa miyezi itatu, ndipo imeneyi inali imodzi mwa nthawi zomwe ndinasangalala kwambiri pa moyo wanga.” Kwa achinyamata ena, kukonda kugwira ntchito mwakhama kwawathandiza kuti athe kugwira ntchito mongodzipereka pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko mwawo.Kudziwa ntchito yamanja kungakuthandizeninso kuti muzipeza ndalama zogulira zosowa za pamoyo wanu. Achinyamata ambiri a Mboni za Yehova ndi apainiya, kapena kuti anthu amene amalalikira nthawi zonse. Kuphunzira ntchito yamanja kwathandiza ena a iwo kumapeza ndalama zoti azitha kudzipezera zosowa popanda kuwononga nthawi ndi ndalama zambiri kuphunzira maphunziro enaake.
Mmene Mungaphunzirire
Kaya mukufuna kuphunzira ntchito yamanja kuti muzidzagwira ntchito imeneyo pamoyo wanu kapena mukungofuna kuti muzitha kukonza zinthu zikawonongeka panyumba panu, n’zachionekere kuti kuphunzira ntchito yamanja kuli ndi phindu lambiri. Mwina n’kutheka kuti m’dera lanu muli sukulu imene imaphunzitsa ntchito zoterozo. Koma n’kuthekanso kuti mungaphunzire zinthu zina kunyumba kwanu. Motani? Mwa kuphunzira kugwira ntchito zapakhomo. Dr. Provenzano, amene tinamutchula kale uja, analemba kuti: “N’zofunika kwambiri kuti achinyamata aphunzire ntchito zapakhomo chifukwa zimawathandiza kuti adzathe kudzisamalira bwinobwino akadzachoka pakhomo pa makolo awo.” Choncho khalani okonzeka kugwira ntchito yomwe ikufunika kugwira panyumba panu. Ngati pali udzu wofunika kutchetcha kapena mpando wothyoka wofunika kukonza, bwanji osagwira ntchito zimenezo?
Ntchito zamanja si ntchito zonyozeka, m’malo mwake zikhoza kukuthandizani m’njira zambiri. Musamapewe ntchito zimenezi. M’malo mwake, yesetsani kusangalala ndi ntchito ya manja anu, chifukwa monga momwe lemba la Mlaliki 3:13 limanenera, umenewu “ndiwo mtulo wa Mulungu,” kapena kuti mphatso yochokera kwa Mulungu.
[Mawu Otsindika patsamba 29]
Kuphunzira ntchito yamanja kwathandiza achinyamata ambiri kufutukula utumiki wawo kwa Mulungu
[Zithunzi patsamba 30]
Nthawi zambiri makolo angakuphunzitseni ntchito zomwe muyenera kudziwa