Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Maganizo a Anthu Asintha pa Nkhani ya Khungu Ayamba Kufuna Khungu Loderako Osati Loyera

Maganizo a Anthu Asintha pa Nkhani ya Khungu Ayamba Kufuna Khungu Loderako Osati Loyera

Maganizo a Anthu Asintha pa Nkhani ya Khungu Ayamba Kufuna Khungu Loderako Osati Loyera

KODI inuyo mumaganiza kuti munthu wathanzi amayenera kuoneka motani? Anthu ambiri a ku Ulaya ndi ku North America amaganiza kuti munthu akakhala ndi thupi losalala ndiponso loderako ndiye kuti ndi wathanzi. Koma umu si mmene anthu ankaganizira kale. Zaka zambiri zapitazo, azimayi a ku Ulaya ankavala zipewa zotambalala ndipo ankanyamula maambulera kuti asapse ndi dzuwa. Anthu oyera ankaoneka kuti ndi apamwamba, pamene anthu oderako ankaoneka kuti ndi otsika, ogwira ntchito zamanja.

Kale kwambiri kuposa pamenepa, anthu ankayeretsa khungu lawo ndi zinthu zimene panopa tikudziwa kuti ndi zapoizoni. Mwachitsanzo, kale kwambiri, monga mu 400 B.C.E., Agiriki ankayeretsa khungu lawo podzola pawudala winawake wapoizoni. Poppaea Sabina, mkazi wa Mfumu Nero ya ku Roma, ankadzola pawudala wapoizoni ameneyu kuti kumaso kwake kuyere. M’zaka za m’ma 1500, azimayi ena achiitaliyana ankadzola mankhwala enaake apoizoni kumaso kwawo kuti kuziwala. Koma kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1920, katswiri wina wa masitayilo a zovala wa ku France dzina lake Coco Chanel anachititsa kuti zokhala ndi khungu loderako zitchuke. Kuyambira pamenepo, anthu ambiri amaona kuti kukhala ndi thupi loderako n’kumene kuli m’fasho. Choncho amatha nthawi yaitali kwambiri akuothera dzuwa.

Komabe, sikuti anthu onse amene amakonda kukhala panja amafuna kukhala ndi khungu loderako. Ena si chikhalidwe chawo kuothera dzuwa kuti ade. Iwo amakonda kukhala panja n’cholinga choti apume basi, uku akumva kufundira kwa dzuwa ndiponso kamphepo kayeziyezi kakuwaomba, osati kuti khungu lawo lide ndi dzuwa. Kodi n’chifukwa chiyani anthu onsewa amafunika kuteteza khungu lawo ku dzuwa?

[Chithunzi patsamba 3]

Anthu ali m’mphepete mwa nyanja kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900

[Mawu a Chithunzi]

Brown Brothers