Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Anthu Amaba M’masitolo?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amaba M’masitolo?

N’chifukwa Chiyani Anthu Amaba M’masitolo?

“Sindiona kuti n’kulakwa kuba m’masitolo, ndimaona kuti n’kutengako zinthu zofunikira kwambiri zimene iweyo ulibe.”—ANATERO WANSEMBE WINA WA ANGILIKANI.

PALI nthano inayake imene anthu amakamba yoti munthu wina dzina lake Robin Hood ankaona kuti kuba kwake sikunali kulakwa. Nthano ya Angelezi imeneyi imati Robin Hood ankabera anthu olemera n’kumapatsa anthu osauka zinthu zimene wabazo. Wansembe amene analankhula mawu ali pamwambawo nayenso amakhulupirira kuti umphawi ndi chifukwa chomveka chobera. Ponena za anthu oba m’masitolo, iye anati: “Ndimawamvera chisoni kwambiri, ndipo ndimaona kuti sakulakwa ngakhale pang’ono.” Iye anati tsiku limodzi pachaka eni masitolo akuluakulu ayenera kulola anthu osauka kulowa m’masitolomo n’kutenga chilichonse chomwe angapeze popanda kulipira.

Koma anthu ambiri oba m’masitolo amaba pa zifukwa zina osati chifukwa cha umphawi. Ku Japan, apolisi anamanga apolisi anzawo awiri amene anaba m’masitolo. Ku United States, munthu amene anali mmodzi mwa akuluakulu a kampani inayake yopanga zakudya anagwidwa akuba m’sitolo ya kampaniyo. Achinyamata oti ali ndi ndalama m’thumba mwawo nthawi zambiri amaba zinthu zoti sakuzifuna n’komwe. Kodi n’chiyani chimachititsa kuti anthu ngati amenewa aziba?

‘Zimasangalatsa’

Munthu akamaba m’sitolo amachita nthumanzi, mtima wake umakhala uli m’malere, koma amadziona kuti ndi wopambana kwambiri. Mofanana ndi atsikana awiri tinawatchula mu nkhani yapita ija, anthu ena amene amaba m’masitolo amasangalala kwambiri akamamva chonchi, ndipo pofuna kuti azimva choncho nthawi zonse n’chifukwa chake amaba. Mzimayi wina ataba koyamba, anati: “Mtima wanga unkagunda kwambiri. Ndinasangalala kwambiri n’taona kuti sanandigwire!” Pofotokoza mmene ankamvera ataba kwa nthawi yaitali ndithu, iye anati: “Ndinkachita manyazi ndi khalidwe langa, komabe zinkandisangalatsa. Ndinkadziona kuti ndine wochangamuka kwambiri. Kuba osagwidwa kunkandichititsa kumva kuti ndine wopambana kwambiri.”

Mnyamata winawake dzina lake Mavuto anati, atatha miyezi ingapo atasiya kuba m’masitolo, ankalakalaka atabanso. * “Ndinkangofuna n’tabanso. Nthawi zina ndikaona wailesi ili m’sitolo ndinkaganiza kuti, ‘Ndikhoza kuitenga mosavuta wailesi imeneyo. Ndikhoza kuizembetsa osagwidwa.’”

Anthu ena amene amaba pongofuna kuti asangalale, sikuti zinthu zimene amabazo amakhala akuzifuna n’komwe. Nyuzipepala ina ya ku India inati: “Akatswiri a maganizo amati anthu oterewa amaba chifukwa choti amasangalala n’kuchita zinthu zoletsedwa. . . . Ena mpaka amakabweza zinthu zimene anabazo.”

Zifukwa Zina

Anthu ambirimbiri amadwala matenda ovutika maganizo. Nthawi zina anthu odwala matendawa amachita zinthu zoipa, monga kuba m’masitolo, chifukwa cha matenda awowo.

Banja la mtsikana winawake wa zaka 14 linali logwirizana ndiponso lopeza bwino. Ngakhale kuti anali wochokera ku banja labwino loterolo, mtsikanayo ankavutika maganizo kwambiri, ndipo ankangoona kuti “zinthu zamusokonekera kwambiri.” Iye anati: “Ndinkangomva choncho nthawi zonse.” Mtsikanayo anayamba kumwa mowa ndi kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Kenaka tsiku lina anamugwira akuba m’sitolo. Patapita nthawi anayesera kawiri konse kuti adziphe.

Ngati mwana wabwino wayamba kuba m’masitolo mwadzidzidzi, makolo ayenera kuganizira zoti mwina mwanayo akudwala matenda ovutika maganizo. Dr. Richard MacKenzie, amene ndi katswiri wa matenda a achinyamata, anati: “Ndimakhulupirira kuti mwana wanu akayamba khalidwe lililonse lachilendo muzilitenga ngati chizindikiro choti mwina ali ndi matenda a maganizo, mpaka mutapeza kuti pali chifukwa china chimene chikumuchititsa zimenezo.”

Achinyamata ena amaba chifukwa chofuna kufanana ndi anzawo, ndipo angafunike kuyamba kaye aba kuti anzawo enaake ayambe kucheza nawo. Ena amaba chifukwa chofuna kuthetsa kunyong’onyeka. Akatswiri oba m’masitolo amapeza zofunika pamoyo wawo m’njira imeneyi. Kaya amaba chifukwa chiyani, akubawa amaba katundu wa ndalama zokwana madola mamiliyoni ambiri m’masitolo tsiku lililonse. Koma winawake amafunika kulipira katundu wobedwayo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Mayina ena mu nkhani zino asinthidwa.

[Bokosi patsamba 21]

NTHENDA YOCHITITSA MUNTHU KUMAFUNA KUBA

Maria anati: “Kuyambira ndili mwana, ndakhala ndi vuto loba m’masitolo. Chilakolako chofuna kubachi chinakula kwambiri mpaka ndinafika pomaba katundu wa ndalama zokwana madola 500 patsiku.

“Kuba sikundisangalatsa, koma mtima wangawu umangoti dyokodyoko mpaka ndibe basi. Ndikufunitsitsa n’tasintha.” Chifukwa choti amalephera kudziletsa kuti asabe, Maria akuganiza kuti ali ndi nthenda yochititsa munthu kumafuna kuba.

Anthu amene ali ndi nthenda imeneyi “amangofuna kuba nthawi zonse, ngakhale kuti chinthu chimene akubacho sakuchifuna.” Vuto limeneli n’lalikulu kuposa chizolowezi chabe, ndipo likuoneka kuti limayamba chifukwa cha mavuto aakulu a m’maganizo.

Anthu ena amaganiza kuti mbava zimene zimaba nthawi ndi nthawi zili ndi nthenda imeneyi, koma madokotala amakhulupirira kuti ndi anthu ochepa kwambiri amene amadwaladi nthendayi. Malinga ndi zomwe linanena bungwe linalake loona za matenda a maganizo lotchedwa American Psychiatric Association, ndi anthu osakwana 5 pa anthu 100 alionse amene amaba m’masitolo amene amadwala nthenda imeneyi. Choncho m’pofunika kusamala musanayambe kukhulupirira kuti munthu winawake amaba m’masitolo chifukwa cha nthenda imeneyi. Pangakhale zifukwa zina zimene munthuyo amabera.

[Chithunzi patsamba 21]

Makolo achikondi amayesetsa kumvetsetsa chifukwa chimene mwana wawo amabera m’masitolo