Kodi N’zotheka Kukhala Mopanda Mantha?
Kodi N’zotheka Kukhala Mopanda Mantha?
KODI n’zotheka kuti munthu amene akukhala m’dziko loopsa la masiku anoli akhale wopandiratu mantha? Ayi. Ngakhale anthu amene amakhulupirira Mulungu amakumana ndi zinthu zoopsa zomwe zimawadetsa nkhawa. Mwachitsanzo, m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino, mtumwi Paulo, yemwe anayenda maulendo ambiri, ananena kuti anachita mantha chombo chake chitasweka, ndipo anakumana ndi zoopsa m’mitsinje, kwa olanda, ndi m’mudzi. (2 Akorinto 11:25-28) Mofanana ndi Paulo, masiku ano anthu ambiri timakumananso ndi zinthu zoopsa.
Kuti tidzichepetsere nkhawa, tiyenera kumachita zinthu mosamala ndiponso mwanzeru. Baibulo limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” (Miyambo 22:3) Kodi zinthu zina zothandiza zomwe tingachite n’zotani?
M’pofunika Kusamala
N’zochititsa chidwi kuti ngakhale kuti Baibulo linalembedwa kalekale, lili ndi mfundo zambiri zimene zikadali zothandiza popewa zoopsa masiku ano. Mwachitsanzo, Baibulolo limati: “Wanzeru maso ake ali m’mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima.” (Mlaliki 2:14) N’chinthu chanzeru kumaonetsetsa anthu amene ali nanu pafupi ndi kupewa malo a mdima ngati mungathe kutero. Mwina popita kunyumba mukhoza kusiya kuyenda njira zachidule n’kumadzera njira zomwe zili zowala bwino, ngakhale zitakhala zazitalipo. Baibulo limachenjezanso kuti: “Awiri aposa mmodzi . . . Ndipo wina akam’laka mmodziyo, awiri adzachirimika.” (Mlaliki 4:9, 12) Ngati mumakhala ku dera loopsa, kodi mungakonze zoti muziyenda limodzi ndi munthu wina popita kunyumba?
Ngati mwakumana ndi wachifwamba, n’chinthu chanzeru kukumbukira kuti moyo ndi wamtengo wapatali kwambiri kuposa katundu. (Mateyu 16:26) M’pofunikanso kukumbukira kuti anthu akasonkhana pamodzi chifukwa chokwiya ndi zinazake, amakhala oopsa ndipo simungathe kudziwa zomwe angachite.—Eksodo 23:2.
Genesis 39:12) Ngati simungathe kuchokapo, munganene kuti: “Choka!” kapena “Osandigwira!” kapenanso “Zomwe ukunenazo zikundinyansa.” Ngati mungathe, muzipewa kupita kumalo kumene anthu amakonda kuvutitsa anzawo.
Ngati mukuvutitsidwa ndi munthu amene akusonyeza kuti akufuna kuchita zachiwerewere, munthu amene akunena nthabwala zotukwana, kapena munthu amene akufuna kukugwiragwirani, ndi bwino kumukaniza mwamphamvu. Mwina mungafunike kuchoka pamalopo, ngati momwe anachitira Yosefe pamene mkazi wofuna zachiwerewere anamugwira. Iye ‘anathawa, natulukira kubwalo.’ (Zimene Mungachite Ngati Mumakhala Mwamantha Panyumba
Kodi mungatani ngati mumaopa mwamuna wanu chifukwa ndi wachiwawa? Chingakhale chinthu chanzeru kuganizira pasadakhale momwe mungathawire panyumbapo ngati mwadzidzidzi mwamuna wanuyo wayamba chiwawa, ndipo mukuona kuti akhoza kukuvulazani inuyo kapena ana anu, kapenanso ngati moyo wanu kapena wa ana anu uli pangozi. * Baibulo limafotokoza momwe Yakobo anakonzeratu mosamala zomwe adzachite ngati mchimwene wake Esau angayambe zachiwawa. Malinga ndi momwe zinthu zinachitikira, sanafunike kuchita zomwe anakonzeratuzo, koma anaganiza bwino kukonzekereratu. (Genesis 32:6-8) Kukonzekereratu kungaphatikizepo kupeza munthu amene angakusungeni mutathawa mwadzidzidzi. Mukhoza kukambirana pasadakhale ndi munthuyo zomwe mungadzafunikire. Zingakhale zothandiza kusunga mapepala ofunika ndi zinthu zina zofunika pamalo osavuta kufikapo.
Mukhozanso kukamunenera mwamuna wanuyo ku polisi kuti apolisiwo akutetezeni. * Baibulo limaphunzitsa kuti aliyense ayenera kututa zomwe wafesa. (Agalatiya 6:7) Ponena za udindo umene maboma ali nawo, Baibulo limati: “Ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu.” (Aroma 13:4) Kumenya munthu kunyumba ndi mlandu waukulu wofanana ndi kumenya munthu panjira. Kulondalonda munthu ndi mlandunso m’mayiko ena.
Kuchita zinthu zomwe tanena panozi kungachepetseko mantha. Koma Baibulo limatiuza zambiri osati malangizo okha. Baibulo ndi buku lokhala ndi maulosi oonadi amene amafotokoza zomwe Mulungu akuchita panopa ndi zomwe adzachite m’tsogolo. Kodi Baibulo limapereka chiyembekezo chotani kwa anthu amene amakakamizika kukhala mwamantha?
Kodi Mantha Amene Ali Paliponsewa Akusonyezanji?
N’zochititsa chidwi kuti mtumwi Paulo analemba kuti: “Masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, . . . opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino.” (2 Timoteo 3:1-3) Mawu amenewo akufotokozadi za nthawi zochititsa mantha!
Mateyu 24:3, 7, 8; Luka 21:10, 11) Choncho “zoopsa” zimene tikuona zomwe zikuchititsa kuti anthu ambiri azikhala mwamantha masiku ano siziyenera kutidabwitsa. Koma kodi zikusonyeza chiyani?
Pamene Yesu ankalankhula za “mathedwe a nthawi ya pansi pano,” anati: “Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina: ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m’malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba.” (Yesu anati: “Pakuona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.” (Luka 21:31) Mu nthawi yathu ino, tiyembekezere kuti boma la Mulungu liyamba kulamulira anthu onse kuchokera kumwamba. (Danieli 2:44) Kodi moyo udzakhala wotani panthawi imeneyo?
Kukhala Mopanda Mantha
Baibulo limafotokoza za nthawi ya m’tsogolo ya mtendere pamene nkhondo zidzatha, anthu ochita zoipa sadzakhalakonso, ndipo anthu onse padziko pano adzakhala okonda Mulungu. Petro, mtumwi wa Yesu, analemba za tsiku la m’tsogolo “la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza.” Sipadzakhala munthu woipa aliyense woopseza anthu chifukwa padziko lapansi ‘padzakhalitsa chilungamo.’ (2 Petro 3:7, 9, 13) Tangoganizirani mpumulo womwe tidzakhale nawo tikadzayamba kukhala pakati pa anthu okhulupirika ndi okondanadi! Kudziwa zimenezi kumatithandiza kuona zinthu zoopsa zomwe zikuchitika panozi mwamtundu wina. Tikudziwa kuti sizidzapitirira mpaka kalekale.—Salmo 37:9-11.
Kuti alimbikitse anthu amene anali kuda nkhawa, mneneri wa Yehova anauzidwa kuti: “Nenani kwa a mitima ya chinthenthe, limbani, musawope; taonani, Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu; Iye adzafika ndi kukupulumutsani.” (Yesaya 35:4) Choncho atumiki a Mulungu woona ayenera kulimba mtima poyembekezera zinthu zomwe zikubwera m’tsogolo muno. (Afilipi 4:6, 7) Kwa anthu amene akhala mwamantha moyo wawo wonse, n’zolimbikitsa kwambiri kuzindikira kuti Yehova sanasinthe cholinga chake choyambirira. Cholinga chimenecho n’choti dziko lapansi lidzadze ndi anthu amene amamudziwa, amenenso amasonyeza makhalidwe ake achikondi.—Genesis 1:26-28; Yesaya 11:9.
Tikudziwa kuti palibe chimene chingalepheretse Yehova kukwaniritsa zinthu zimene, mwachikondi chake, akufuna kuchitira anthu. (Yesaya 55:10, 11; Aroma 8:35-39) Tikamvetsetsa mfundo imeneyi, mawu a mu salmo lina lodziwika bwino amakhala ndi tanthauzo lapadera. Mu salmo limeneli timawerenga kuti: “Yehova ndiye mbusa wanga; . . . Atsitsimutsa moyo wanga; anditsogolera m’mabande a chilungamo, chifukwa cha dzina lake. Inde, ndingakhale ndiyenda m’chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzawopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine.” (Salmo 23:1-4) Ngakhale kuti zinthu zoopsa mwina ziwonjezeka, dziko limene anthu azidzakhala mopanda mantha likubweradi ndipo lili pafupi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Ponena za pamene kupatukana ndi mwamuna kapena mkazi wanu kungakhale kogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo, onani Galamukani! ya February 8, 2002, tsamba 28.
^ ndime 10 Kuti mumve zambiri zothandiza anthu amene amamenyedwa panyumba, onani Galamukani! ya November 8, 2001, masamba 3-12, ndi Galamukani! ya February 8, 1993, masamba 3-14.
[Zithunzi pamasamba 8-10]
Mulungu posachedwapa abweretsa dziko limene anthu azidzakhala mopanda mantha