Kukhala ndi Mphamvu Ngati Wachinyamata Mpaka Muyaya
Kukhala ndi Mphamvu Ngati Wachinyamata Mpaka Muyaya
MWAMUNA amene anali pambali pa Yesu anali atatsala pang’ono kufa. Iye anapempha kuti: “Yesu, ndikumbukireni mmene mulowa Ufumu wanu.” Yesu anayankha kuti: ‘Indetu, ndinena ndi iwe lero lino, udzakhala ndine m’Paradaiso.’ (Luka 23:42, 43) N’zoona kuti munthu amene dzina lake silinatchulidwe ameneyu sankafa chifukwa cha matenda a ukalamba, koma ankaphedwa chifukwa cha zochita zake zaupandu. Komabe, anthu amene akukalamba angalimbikitsidwe kwambiri ndi zomwe zinachitika panthawi imeneyi, pamene munthuyu analibiretu pogwira.
Timagoma kwambiri ndi chikhulupiriro chachikulu cha mwamuna ameneyu. Ngakhale kuti Yesu anali kufa pa mtengo wozunzirapo pambali pake, mwamunayu sankakayikira n’komwe zoti Yesu adzalamulira monga Mfumu mu Ufumu wa Mulungu. Ndiponso, anali ndi chikhulupiriro kuti tsiku linalake Yesu adzamukumbukira. Tangoganizirani zimenezi: Munthu wotembereredwa ameneyu adzauka kwa akufa m’paradaiso wokongola, Yesu ali Mfumu!
Zomwe zikuchitikira anthu panopa n’zofanana ndi zomwe zinali kuchitikira mpandu woipa amene anali atatsala pang’ono kufa ameneyu. N’zofanana bwanji? Kaya tikhale a zaka zingati, tonsefe tikulipira mtengo wa uchimo ndipo tikufunika kupulumutsidwa. (Aroma 5:12) Mofanana ndi mpandu uja, nafenso tingatembenukire kwa Kristu Yesu kuti tikhale ndi chiyembekezo, kuphatikizapo chiyembekezo choti tidzapuma ku mavuto opweteka amene amakhalapo pa ukalamba. Zoonadi, Yesu akupatsa anthu chiyembekezo chokhala ndi moyo wosatha, komanso kukhala ndi thupi ndi maganizo angwiro m’paradaiso pa dziko lapansi.—Yohane 3:16, 36.
Zonse Zidzakhala Zatsopano kwa Okalamba ndi Achinyamata Omwe
Mu Ufumu wa Kristu, anthu okhala pa dziko lapansi ‘adzakondwera nawo mtendere wochuluka.’ (Salmo 37:11) Palibe amene adzanene kuti ‘ndikudwala.’ (Yesaya 33:24) Ngati tinkalephera kuchita zinazake pa chifukwa chilichonse, tidzayambiranso kutha kuchita zimenezo, chifukwa “wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzayimba.” (Yesaya 35:6) Anthu okalamba adzasandukanso anyamata; thupi lawo ‘lidzakhala se, kuposa la mwana.’—Yobu 33:25.
Komabe, kodi m’pomveka kukhulupirira kuti zimenezi zidzachitikadi? Choyamba, taganizirani za amene analonjeza za Paradaiso kwa munthu amene anali kufa uja. Nthawi zambiri, makamu a anthu anapititsa kwa Yesu anthu olumala, ofooka, akhungu, ndi osamva. Iye mofunitsitsa ‘anachiritsa nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.’ (Mateyu 9:35, 36; 15:30, 31; Marko 1:40-42) Iye anasonyeza bwino zomwe Ufumu wake udzachite. Yesu anaukitsanso anthu angapo amene anamwalira. (Luka 7:11-17; Yohane 11:38-44) Mwa kuchita zimenezi, anapereka umboni wotsimikizira lonjezo lake loti “onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.”—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
Tangoyerekezerani kuti mwadzuka m’Paradaiso ndipo muli ndi thupi latsopano, maso abwino, makutu anu akumva bwinobwino kulira kwa mbalame ndi mawu a anthu achimwemwe, manja ndi miyendo yanu zasiya kupweteka, ndiponso mutu wanu ukuganiza bwino kwambiri. “Masiku oipa” a ukalamba adzakhala atatheratu. (Mlaliki 12:1-7; Yesaya 35:5, 6) Ngakhale imfa ‘idzatheratu,’ idzamezedwa kwamuyaya.—1 Akorinto 15:26, 54.
Zomwe zikuchitika padzikoli panopa tikaziyerekezera ndi ulosi wa m’Baibulo zikusonyeza kuti tikuyandikira mapeto a ukalamba. (Mateyu 24:7, 12, 14; Luka 21:11; 2 Timoteo 3:1-5) Tikuyandikira nthawi imene okalamba amene asonyeza chikhulupiriro mwa Mulungu ndipo amutumikira adzakhalanso ndi moyo wamphamvu ngati achinyamata, koma pa nthawi imeneyi adzakhala achinyamata kwamuyaya!
[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]
Muziugwiritsa Ntchito Ubongo Wanu
Monga momwe kuchita zinthu zolimbitsa thupi kumalimbitsira minofu, kugwiritsa ntchito ubongo kwambiri kumathandizanso ubongo kuti uzigwira ntchito bwino. Kuti ubongo uzigwira bwino ntchito, tiyenera kumachita zinthu zatsopano. M’munsimu muli njira zina zomwe mungathandizire ubongo wanu kuti upange ndi kulimbitsa tinjira tatsopano totumizira mauthenga n’kumagwira ntchito bwino.
▪ Yambani kuchita zinthu zatsopano, monga zojambulajambula, zosemasema, ndi masewera ogwiritsa ntchito ubongo monga bawo ndi ena otero; phunzirani chinenero china.
▪ Muzikumana ndi anthu osiyanasiyana; muzicheza nawo kuti musamanyong’onyeke komanso kuti muzikumbukira bwino zinthu.
▪ Yambani kukonda zinthu zauzimu. “Musadere nkhawa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 4:6, 7.
▪ Werengani mabuku abwino; uzani munthu wina zimene mwawerengazo.
▪ Kumbukirani ndi kufotokozera wina nkhani zomwe mwamva pa wailesi kapena pa TV kuti muzitha kukumbukira bwino zinthu zimene mwangozimva kumene ndiponso zimene munazimva kalekale.
▪ Gwiritsani ntchito dzanja limene simuligwiritsa ntchito kwambiri (lakumanzere ngati ndinu wakumanja kapena lakumanja ngati ndinu wakumanzere) pogwiritsa ntchito choyatsira TV muli patali, podina manambala pa telefoni, kapena potsuka mano.
▪ Muzigwiritsa ntchito kwambiri mphamvu yanu ya kumva, kununkhiza, kukhudza, kuona ndi kulawa monga momwe mungathere tsiku lonse.
▪ Phunzirani za malo ochititsa chidwi, apafupi ndi akutali omwe, ndipo pitani ku malo amenewo.
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Lonjezo la Yesu n’loti ukalamba wopweteka udzatha posachedwapa, ndipo m’malo mwake anthu adzakhala ndi mphamvu ngati achinyamata kwamuyaya