“Ndikufuna Ndizingoliwerengabe”
“Ndikufuna Ndizingoliwerengabe”
▪ Chaka chathachi, pa misonkhano yachigawo ya Mboni za Yehova padziko lonse lapansi, anatulutsa buku latsopano la masamba 224 la zithunzi zokongola, lomwe alikonza makamaka n’cholinga chophunzitsa ziphunzitso zoyambirira za m’Baibulo. Bukuli mutu wake ndi wakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Munthu wina amene wawerenga bukuli analemba kuti: “Ndikufuna ndizingoliwerengabe. Bukuli latenga mfundo zonse zabwinozabwino za m’mabuku onse ophunzirira amene ndawerengapo, ndipo laziphatikiza pamodzi m’masamba owerengekawa basi.”
Wina anati: “Tsamba lililonse limakulimbikitsa kuti upitirizebe kuwerenga. Ndimakondanso mmene analongosolera pamapeto pa chaputala chilichonse za zimene tingapeze m’chaputala chotsatira. Muli ndime zambiri zimene zimandikhudza mtima kwambiri. Pali zinthu zambiri zimene zimandipangitsa kulikonda kwambiri bukuli, zimene nditati ndilembe zingakhalenso buku palokha!”
Palinso munthu wina yemwe anayamikira polemba kuti: “Zoonadi, bukuli ndi la mtengo wapatali kwambiri, mtengo wake wauzimu ndi wosayerekezeka, ndipo bukuli likhala lothandiza kwambiri pophunzitsa anthu atsopano.”
Tsopano mukhoza kuitanitsa buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? m’zinenero zoposa 140. Ngati mukufuna kuitanitsa bukuli lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
□ Popanda kulonjeza kuti ndidzachita chilichonse, ndikupempha kuti munditumizire buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
□ Chonde nditumizireni munthu kuti ayambe kuchita nane phunziro la Baibulo lapanyumba laulere.