Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mbalame za M’mphepete mwa Nyanja N’zimene Zimauluka Kwambiri Padziko Lonse

Mbalame za M’mphepete mwa Nyanja N’zimene Zimauluka Kwambiri Padziko Lonse

Mbalame za M’mphepete mwa Nyanja N’zimene Zimauluka Kwambiri Padziko Lonse

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU SPAIN

TANGOYEREKEZERANI kuti mumakhala miyezi iwiri yachilimwe ku chigawo chozizira kwambiri cha kumpoto kwa dziko lapansi, kumene panthawi imeneyi dzuwa sililowa. Koma nthawi yozizira ikamayandikira, mumapita ku South America, Australia, kapena ku South Africa. Ndipo kwa chaka chonse, mumakhala mukuyendayenda, kufunafuna zakudya zimene mumazikonda zopezeka m’mphepete mwa nyanja pa makontinenti onse. Mmenemu ndi mmene mbalame zambiri za m’mphepete mwa nyanja zimakhalira.

Mbalame zimenezi zimakonda kudya m’madzi osaya. * M’miyezi yozizira ya kumpoto kwa dziko lapansi, mbalamezi zimakumana pamodzi m’malo amatope amene mitsinje imakumana ndi nyanja, m’magombe, m’malo amatope omwe kale anali m’madzi, kapena m’malo a miyala a m’mphepete mwa nyanja, kumene sikukhala anthu ambiri. M’miyezi yotentha, pamene anthu ambiri ofuna kukaona malo amapita ku magombe, mbalame zambiri za m’mphepete mwa nyanja zimapita kumpoto kwa dziko lapansi kapena kufupi ndi kumeneku. Kumeneku kumakhala nyengo yotentha yaifupi, ndipo imapatsa mbalamezi mpata wokhala pazokha ndiponso zimapezako chakudya chochuluka chomwe zimafunikira kuti zilere ana awo.

Mbalame za m’mphepete mwa nyanja sizikhala ndi mitundu yowala kwambiri, koma kuuluka kwawo kochititsa chidwi ndi mapiko awo owala amasangalatsa anthu ambiri. Buku lotchedwa Shorebirds—Beautiful Beachcombers limati: “[Mbalamezi] zimatha kuuluka nsonga za mapiko awo zikukhudza madzi kapena zimauluka pamwamba potalika makilomita sikisi kapena kuposa pamenepo kuchokera pansi. Ndithudi ndi mbalame zodziwa kuuluka mwaluso.”

Zimatetezeka Chifukwa Chokhala M’magulu

Mbalame za m’mphepete mwa nyanja nthawi zambiri zimasonkhana m’magulu aakulu kumene kuli zakudya zambiri. Zikuoneka kuti zimakhala zotetezeka zikakhala m’chigulu. Mbalame zinazake zokhala ngati mphamba zimakonda kusaka mbalame imene ili payokha, pamene zikaona chigulu cha mbalame zimagwa ulesi. Ndipo pakakhala mbalame zambirimbiri zikuunguzaunguza adani, zimathandiza kuti mdani aonedwe msanga. Kuti zitetezedwe mwa njira imeneyi, mbalame zambiri za m’mphepete mwa nyanja za mitundu yosiyanasiyana zimasonkhana pamodzi.

Gulu la mbalamezi likayamba kuuluka, zimakhala zochititsa chidwi kwambiri kuona. Mbalame mahandiredi angapo, mwinanso masauzande angapo, zikuulukira pamodzi moyandikana, zimakhotakhota pouluka, zimakwera ndi kutsika, ngati kuti pali dzanja losaoneka lomwe likuziwongolera zonsezo. Buku lakuti Handbook of the Birds of the World limati: “N’zodabwitsa kwambiri kuti mbalame zambirimbiri chonchi zimatha kuulukira pamodzi mothamanga kwambiri, ndipo zimatha kusinthasintha kaulukidwe kawo mogwirizana bwino.” Mwakuonetsetsa mafilimu ojambula zinthu zomwe zikuyenda mwamsanga amene anajambula mbalame zinazake, akatswiri a mbalame azindikira kuti mbalame imodzi imatha kuyambitsa kaulukidwe kenakake kamene mbalame zina zonsezo zimatsanzira.

Zimatha Kuuluka Kuzungulira Dziko Lonse Lapansi

Mbalame zina za m’mphepete mwa nyanja zimaulukadi padziko lonse lapansi. Mwachitsanzo pali mbalame zina zimene zimaswana kumpoto kwambiri kwa dziko lapansi kuposa pafupifupi mbalame zina zonse. Mbalame za m’mphepete mwa nyanja zikhoza kufika pafupifupi pa gombe lililonse pa dziko lapansi ndipo zimauluka mtunda wa makilomita pafupifupi 32,000 pa ulendo wawo wa chaka n’chaka.

Ngakhale kuti pa maulendo ena mbalamezi zimafunika kuwoloka nyanja zamchere, sizitha kusambira ndipo siziima pamadzi. Choncho zimafunika kukhala ndi mafuta ambiri m’thupi, ochuluka kuposa amene ndege yaikulu imanyamula tikayerekezera kukula kwake ndi kukula kwa mbalameyi. Ndegeyi ponyamuka, 40 peresenti ya kulemera kwake konse kumakhala kulemera kwa mafuta. Kodi mbalamezi zimatani kuti zikhale ndi mafuta ochuluka chonchi?

David Attenborough anafotokoza m’buku lake lakuti The Life of Birds kuti: “Zimasunga mafuta m’thupi mwawo mwa kudya kwambiri pamalo amatope a m’mphepete mwa nyanja, omwe kale anali m’madzi, moti m’milungu yochepa kulemera kwawo m’nyengo yachilimwe kumakhala kutawirikiza pafupifupi kawiri kulemera kwawo kwakale. Mafuta amene zimasungirawa amachuluka kuposa kuwirikiza kawiri amene analipo kale, chifukwa ziwalo zawo zambiri za m’kati, kuphatikizapo ubongo ndi matumbo awo, zimakhwinyata kuti papezeke malo oika mafuta onsewa ndi kutinso mbalameyo isamalemere kwambiri.”

Pali mbalame zina zodziwa kuuluka maulendo ataliatali zomwe zimachokera ku Alaska kupita ku zilumba za ku Hawaii. N’zodabwitsa kuti mbalamezi zimatha kupirira n’kuuluka osapuma kwa makilomita 4,500. Koma zodabwitsa kuposa pamenepa n’zoti zimatha kudziwa pomwe pali Hawaii pakati pa nyanja yamchere. Chimenechi n’chitsanzo cha luso lozizwitsa la mbalame lotha kupeza malo amene zikufuna. Mbalame ina imene ankaiona ikuuluka inayenda ulendo umenewu m’masiku osakwana anayi. Ndipo mbalame ina yokalamba yayenda ulendo umenewu maulendo 20!

Mbalame zouluka ulendo wautalizi zikafika kumpoto kwa dziko lapansi, zimakhala zotanganidwa kwambiri. M’milungu iwiri, ziyenera kupeza mkazi kapena mwamuna, kupeza pokhala, ndi kumanga chisa. Kenaka zimakhala ndi milungu pafupifupi itatu yoti zikhalire mazira ndi milungu ina itatu yoti zilere anapiye awo. Pomafika kumapeto kwa July, zimakhala zitanyamuka ulendo wopita kum’mwera kachiwirinso.

Zoopsa za Maulendo Ataliatali

Pa maulendo ataliatali amene mbalame za m’mphepete mwa nyanja zimauluka, zimakumana ndi zoopsa zambiri. Vuto limodzi lalikulu ndi anthu. M’zaka za m’ma 1800, katswiri wina wa zachilengedwe dzina lake John James Audubon anati gulu linalake la alenje linapha mbalame za mtundu winawake za ku America zokwana 48,000 tsiku limodzi. Masiku ano, mbalame za mtundu umenewo zawonjezekako padziko lonse lapansi, komabe mwina n’zosakwana mbalame zimene zinaphedwa tsiku limenelo kuchuluka kwake.

Vuto lina lalikulu kuposa pamenepa la mbalame za m’mphepete mwa nyanja ndilo kutha kwa madambo. Mbalamezi zimavutika kuti zisinthe moyo wawo madambo akamatha chonchi. Buku lakuti Shorebirds—An Identification Guide to the Waders of the World limati: “Chizolowezi cha mbalame za m’mphepete mwa nyanja choswana, kuulukira ku madera akutali, ndi kupeza malo enaake m’nyengo yozizira chakhala chikuchitika kwa zaka masauzande ambiri, koma n’zosavuta kuti anthu asinthe kapena awononge zimenezi.” Kuti mbalame zambiri za m’mphepete mwa nyanja zipulumuke zikudalira pa kusunga malo ochepa ofunika omwe mbalamezi zimaimapo pamaulendo awo.

Chitsanzo chabwino cha malo oterewa ndi Delaware Bay, kugombe lakum’mwera chakumadzulo kwa mzinda wa New Jersey ku United States. Kumalo amenewa, mbalame zamtundu winawake zokwana pafupifupi 100,000 zimasonkhana nyengo yachisanu ikatha kuti zidye mazira a nkhanu. Mbalamezo zimakhala ndi njala, poti zimakhala zitangomaliza kumene ulendo umene ndi “umodzi mwa maulendo aatali kwambiri osapumira a mbalame.” M’milungu iwiri zimakhala zitauluka ulendo wa makilomita 8,000 kufika kumalowa kuchokera kum’mwera chakum’mawa kwa Brazil, ndipo panthawi imeneyi zimakhala zitawonda mpaka kumalemera theka la kulemera kwawo kwakale.

Zoyesayesa za anthu osunga malo achilengedwe zingathandize kuti malo amene mbalame zimakonda kuimako ngati amenewa akhalepobe. Mwina chakwanuko kuli malo ngati amenewa. Ngati munaonapo gulu la mbalame za m’mphepete mwa nyanja zikuuluka mokhotakhota ndiponso mothamanga pamwamba pa madzi kapena ngati munamvetserapo nyimbo zawo zomvetsa chisoni, simungaziiwale.

Mogwirizana ndi zomwe katswiri wina wa zachilengedwe dzina lake Arthur Morris anafotokoza, “anthu onse amene amakonda kuyang’ana mbalame za m’mphepete mwa nyanja ali ndi maganizo ofanana: aliyense wa ife anaimapo nthawi zosawerengeka pa magombe opanda anthu kapena pa malo a matope a m’mphepete mwa nyanja ndipo anaonapo gulu la mbalamezi zikuuluka moonetsa nthenga zawo zakuda ndi zoyera, ndiponso mokhotakhota ndi mogwirizana. Ndipo nthawi iliyonse zimenezi zikachitika, zimatichititsa chidwi ndipo timasowa chonena.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Mbalame za m’gulu limeneli zilipo za mitundu yoposa 200.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 18]

Mbalame Zotha Kuulukira ku Madera Akutali

Mbalame iyi mwina ndi imene imauluka ulendo wautali kwambiri kuposa zonse. Mbalame za mtunduwu zimene zimaswana kumpoto kwa Canada, nthawi zambiri m’nyengo yozizira zimakhala kumadzulo kwa Ulaya kapena kum’mwera kwa South America (zimauluka mtunda wotalika makilomita oposa 10,000 kuti zifike kumeneku)

[Mawu a Chithunzi]

KK Hui

Gulu la mbalame izi zokwana pafupifupi wani miliyoni zinaonedwapo ku Netherlands ndi ku Mauretania

Mbalame izi zimapita kutali ndi kumene zimaswera ku Siberia, ndipo zimakafika ku British Isles, ku South Africa, ku Middle East, ku Australia, kapena ku New Zealand

Mbalame izi zikhoza kupezeka zikuyenda pa magombe pafupifupi kulikonse pa dziko lapansi. Zina zimakaswanira makilomita 950 okha kufupi ndi dera la kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi

[Zithunzi pamasamba 16, 17]

Kuti ziwoloke nyanja zamchere zikuluzikulu, mbalame za m’mphepete mwa nyanja ziyenera kukhala ndi mafuta ambiri m’thupi, popeza siziima pa madzi

[Chithunzi pamasamba 16, 17]

Mbalame izi zimatetezeka chifukwa chokhala m’magulu

[Chithunzi patsamba 17]

Mtundu umodzi wa mbalame za m’mphepete mwa nyanja

[Chithunzi patsamba 17]

Mbalame iyi ikufunafuna chakudya m’dambo

[Mawu a Chithunzi patsamba 16]

Top and bottom panoramic photos: © Richard Crossley/​VIREO