Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Svalbard Dera Lozizira la M’mphepete mwa Nyanja

Svalbard Dera Lozizira la M’mphepete mwa Nyanja

Svalbard Dera Lozizira la M’mphepete mwa Nyanja

YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU NORWAY

TILI m’ndege imene ikuuluka m’katikati mwa mitambo yambiri, ndipo sitikutha kuona kanthu. Mosayembekezereka, ndege yathu ikutuluka m’mitambomo ndipo tikayang’ana pansi, tikuona dera lokutidwa ndi chipale chofewa. Deralo n’looneka mosangalatsa kwambiri. Ndiyeno tikuona zinthu zina zochititsa chidwi kwambiri monga madzi okongola abuluu pang’ono amene akuoneka m’zigwembe za m’mphepete mwa nyanja, matanthwe a madzi oundana, ndi mapiri okutidwa ndi chipale chofewa. Ndipo dera lokutidwa ndi chipale chofewa ndiponso lokhala ndi madzi oundanali n’lalikulu kwambiri moti sitikuona pamene lathera. Limeneli ndi dera lotchedwa Svalbard, ndipo tabwera kuno kudzaliona. Lili kufupi kwambiri ndi kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi, ndipo lili ndi zilumba zingapo.

Dzina loti Svalbard, lomwe limatanthauza “Dera Lozizira la M’mphepete mwa Nyanja,” linalembedwa koyamba m’mabuku a mbiri yakale a ku Iceland m’chaka cha 1194. Komano derali “linatulukiridwa” m’chaka cha 1595, patadutsa zaka 400 chilembedwere m’mabukuwo, ndipo zimenezi n’zimene zinatchukitsa derali padziko lonse. M’chaka chimenecho, gulu la anthu a ku Netherlands lofufuza malo atsopano lotsogoleredwa ndi Willem Barents linali pa ulendo wapanyanja wolowera kumpoto ndipo munthu wina yemwe ankayang’ana kutsogolo anaona kuti chapatali kwambiri pali mapiri osongoka. Anthu ofufuza malo atsopanowa anali atabwera ku dera lina la kumpoto chakumadzulo kwa Svalbard, lomwe Barents analitcha “Spitsbergen,” kutanthauza “Mapiri Osongoka.” Limeneli tsopano ndi dzina la chilumba chachikulu padera la zilumbali. Kutulukiridwa kwa derali, kunayambitsa ntchito zosiyanasiyana ku Svalbard, monga kupha anamgumi ndi nyama zina za m’madzi, kusaka, kufufuza malo atsopano komanso patapita nthawi, kunayambitsa ntchito za migodi ya malasha, kufufuza zasayansi, ndiponso zokopa alendo. Kwa zaka zambiri m’mbuyomo, mayiko ambiri agwirapo nawo ntchitozi kuderali, koma kuyambira mu 1925, derali lakhala m’manja mwa dziko la Norway.

Dziko Lozizira Kwambiri Ndiponso Kuwala Kochititsa Chidwi

Ndege yathuyo ikutsika m’dera la madzi oundana a m’zigwembe zakuya za m’mphepete mwa nyanja, kenako n’kutera pa bwalo la ndege la Svalbard. Ndiyeno tikukwera galimoto yomwe tachita hayala n’kuyamba ulendo wopita kutawuni ya Longyearbyen, yomwe inatenga dzina lake kwa munthu wa ku America wotchedwa John M. Longyear, amene anayambitsa ntchito za migodi ya malasha m’derali, m’chaka cha 1906. Tawuni ya Longyearbyen n’njaikulu kwambiri ku Svalbard konse, ndipo ili ndi anthu pafupifupi 2,000. Indedi, dera lalikulu la zinthu zachilengedwe lomwe likuoneka losasokonezedwali, tapezako tawuni yamakono yokhala ndi zinthu zodziwika monga sitolo, positi ofesi, banki, laibulale, masukulu amkaka ndi masukulu ena, mahotela, malesitilanti, chipatala, ndi nyuzipepala yakeyake. Tawuni ya Longyearbyen yayandikira kwambiri kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi kuposa tawuni ina iliyonse yaikulu ngati imeneyi.

Tapeza malo ogona panyumba yogona alendo imene kale inali gawo la nyumba ya anthu ogwira ntchito m’migodi ya malasha. Mukakhala pa nyumba imeneyi, mungathe kuona bwinobwino tawuni ya Longyearbyen ndiponso phiri lalikulu lochititsa chidwi kwambiri la Hiorthfjellet. Tili m’mwezi wa October, ndipo mapiri n’ngokutidwa ndi chipale chofewa. M’munsi mwa zigwa za mapiri amenewa mulibe chipale chofewa, koma nthaka yake ndi yogwirana chifukwa cha kuzizira kwambiri. Inde, amenewa ndi malo ozizira kwambiri. Dothi la pamwamba panthaka limamasuka kwa nthawi yochepa chabe m’chilimwe. Komabe, chifukwa cha mphepo yabwino imene imaomba kuderali ndiponso mafunde a m’nyanja, nyengo ya kudera limeneli n’njotentherapo kusiyana ndi malo ena a m’chigawo chomwechi cha kumpoto kwa dziko. Kuchokera ku malo athu ogonawo, tikutha kuona kuwala kwa dzuwa kumapiri, koma chigwa chili mu mthunzi wooneka wa buluu. Kuyambira pa October 26 mpaka pa February 16, dzuwa silimatuluka n’komwe kumadera ozungulira tawuni ya Longyearbyen. Koma kuwala kochititsa chidwi komwe kumaoneka kuchokera chakumpoto, n’kumene kawirikawiri kumathamangitsa mdima m’nyengo imeneyi. Komano m’nthawi ina, dzuwa silimalowa n’komwe m’dera limeneli la Svalbard, ndipo m’tawuni ya Longyearbyen, zimenezi zimachitika kuyambira pa April 20 mpaka pa August 23.

Zomera Ndiponso Zinyama

Kunja kwazizira madigiri 8 kuposa mmene kumazizirira kuti madzi afike poundana, ndipo mphepo yamphamvu ikuwomba, komabe kumwamba kulibe mitambo. Takonzeka kuti tiyambe ulendo. Munthu wotiperekeza yemwe akutionetsa malo osiyanasiyana akukwera nafe pamwamba pa phiri la Sarkofagen, ndiponso akutsetsereka nafe kumalo otchedwa Longyearbreen komwe kuli matanthwe a madzi oundana. Pamene tikukwera m’mapiri ozizira kwambiriwa, munthu wotiperekezayo akutiuza kuti m’miyezi yotentherapo, kunoko kumamera maluwa okongola osiyanasiyana. Kunena zoona, n’zodabwitsa kuti ku Svalbard kuno kuli zomera zambiri, ndipo kuli mitundu yoposa 170 ya maluwa. Mitundu iwiri ya maluwa ofala kuderali ndi maluwa enaake omwe amaoneka oyera kapena achikasu, ndi ena onunkhira kwambiri ooneka mofiirira.

Pamene tikukwera pamwamba paphiri lokutidwa ndi chipale chofewali, tikuona mapazi a mbalame inayake ya kuderali yonga nkhuku. Mbalame za mtundu umenewu n’zokhazi zimene zinakhazikika kuno ku Svalbard. Mitundu ina yonse ya mbalame, monga mbalame zosiyanasiyana za kunyanja, mbalame zooneka ngati abakha oyera, ndiponso mbalame zofiirira za mlomo wautali, sizimakhazikika kuderali. Mtundu wa mbalame zinazake za kunyanja n’ngochititsa chidwi kwambiri. Mbalame zambiri za mtundu umenewu zimauluka ulendo wautali kwambiri, kuchoka kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansili kukafika kum’mwera kwenikweni.

Tikuonanso mapazi a nkhandwe za kuderali. Nyama yochenjerayi imadya nyama zina zakufa zimene yapeza, koma zikasowa, imadya ana a mbalame ndi mazira. Nkhandwe ndi imodzi mwa mitundu iwiri ya zinyama zapamtunda za kuno ku Svalbard, zomwe sizinachokere kwina. Nyama inayo ndi yokhala ngati mphalapala. Panthawi yomwe takhala ku Svalbard, taona nyama imeneyi kangapo konse titaiyandikira ndithu. Nyamayi imangotiyang’ana mofatsa tikamaiyandikira n’kumaitola zithunzi, koma kenaka imathawa. Nyama yooneka ngati mphalapalayi n’njaifupi miyendo, yokhala ndi ubweya wambiri komanso wothithikana. M’nyengo yozizira ino, nyamayi imakhala yonenepa ndipo mafuta a m’thupi lakewo amaithandiza kuti isamazizidwe kwambiri m’chisanu.

Anthu ambiri amati chimbalangondo choyera, chomwe ndi mfumu ya zinyama zonse za kumpoto kwenikweni kwa dziko lapansi, ndi nyama ya m’madzi. Anthuwo amatero chifukwa chimbalangondochi chimathera nthawi yaitali kunyanja chikuyenda pa madzi oundana posaka nyama zinazake za m’madzi. Koma mukhoza kukumana ndi zimbalangondo zoyenda pazokhapazokha zomwe zimayendayenda pafupifupi m’dera lililonse ku Svalbard. Koma munthu amene akutiperekezayo sakufuna ku kumana nazo. Zimbalangondozi nthawi zina zimalusa kwambiri, choncho munthu wotiperekezayo watenga mfuti n’cholinga chotiteteza. Kuyambira m’chaka cha 1973, kusaka ndi kupha zimbalangondo kunaletsedwa ndipo munthu wina aliyense akapha chimbalangondo, amafufuzidwa ndi kufunsidwa mafunso. Ngakhale kuti masiku ano zimbalangondozi n’zochuluka ndithu ku Svalbard, tsogolo la zinyama za mphamvuzi likudetsa nkhawa kwambiri. Dera la kumpoto kwenikwenili, limaoneka ngati loyera, labwino, ndiponso losawonongeka. Koma lili ndi mankhwala owononga zamoyo amene akhudza kwambiri chilengedwe cha kumeneko. Mankhwala owononga zamoyowa amaunjikana m’thupi mwa zimbalangondo chifukwa n’zimene zimadya kwambiri zinyama zinzake. Ndipo mankhwala amenewa akuoneka kuti akulepheretsa zimbalangondozi kuberekana bwino.

Tafika pamwamba penipeni paphiri la Sarkofagen ndipo titaponya maso tikuchita chidwi kwambiri kuona nsonga zambirimbiri za mapiri osongoka, zimene zakutidwa ndi chipale chofewa. Kum’mwera chakumadzulo kuli phiri lochititsa chidwi la Nordenskiöldfjellet, lomwe n’lozungulira ndipo dzuwa likuwala m’phiri limeneli. Cham’munsi mwathu kwambiri muli tawuni ya Longyearbyen, ndipo m’mwamba mwathu, mukuoneka thambo la buluu. Tikuchita kumva kuti taimiriradi pamwamba penipeni padziko. Ndiyeno tikutsitsimulidwa pamene tikudya buledi ndiponso kukonkha kukhosi ndi chakumwa chinachake cha madzi otentha, chothira shuga chomwe chimachokera ku zipatso. Kenako takonzeka kuyamba ulendo wotsetsereka phirilo kulowera kudera la madzi oundana la Longyearbreen.

Migodi ya Malasha Ndiponso Kupha Nyama Mosakaza

Chinthu china chosangalatsa kwambiri ndi ulendowu, n’kucheza kwathu ku mgodi wakale wa malasha. Mwamuna wa dzitho wotilondolerayo, yemwe ndi katswiri pantchito yokumba malasha, akutionetsa Mgodi Wachitatu, womwe uli kunja kwa tawuni ya Longyearbyen. Titavala maovololo ndi zisoti zoteteza mitu zokhala ndi matochi pamphumi, tikum’tsatira munthu wotilondolerayo kulowa mu mgodi wakuya wam’kati mwa phiri. Tauzidwa kuti, kuyambira chakumayambiriro kwa m’ma 1900, ku Svalbard kuno, akhala akudalira kwambiri ntchito za m’migodi ya malasha. Kwa zaka zambiri, anthu a m’migodi ankavutika kwambiri. Kawirikawiri, iwo ankakwawa ndi maondo ndiponso manja m’ngalande zoyenda mtunda wautali za m’migodi ya malasha, ndipo malo ena m’ngalandezi anali aatali masentimita 70 okha basi kupita m’mwamba. Tili ndi mpata woyeserera kukwawa ngati mmene anthu ogwira ntchito m’migodiwo ankachitira ndipo taona kuti anthuwo ankavutika zedi. Ntchito yawo inali yovuta, mpweya unali wodzadza ndi fumbi la malasha ndiponso la miyala, kunali phokoso lalikulu, ndipo nthawi ina iliyonse migodi ikanatha kuphulika ndiponso kugumukira. Koma masiku ano, kuli njira zamakono zomwe zikugwiritsidwa ntchito. Ntchito za m’migodi ya malasha n’zimene amadalirabe kwabasi pachuma cha ku Svalbard, koma kuyambira zaka makumi angapo zapitazo, ayambanso kudalira kwambiri ntchito zokopa alendo.

Sikuti anthu nthawi zonse akhala akusamala zoti zinyama za kudera limeneli zingasakazike ayi. Panthawi inayake ku Svalbard kuno, anthu ankasaka ndi kupha anamgumi, nyama zinazake za m’madzi, nyama zooneka ngati mphalapala, zimbalangondo, ndi nyama zina zambiri, moti mitundu ina ya zinyamazi inatsala pang’ono kutheratu. Komano, zinyamazi zayamba kuchulukananso chifukwa cha malamulo okhwima omwe aikidwa poteteza zinyamazi.

Malo Abwino Kwambiri kwa Akatswiri a za M’matanthwe

Dera la Svalbard lakhala likutchulidwa kuti “n’labwino kwambiri kwa akatswiri a za m’matanthwe.” Popeza zomera zili patalipatali kwambiri, derali limaoneka ngati buku la zithunzi zokhazokha za matanthwe. Tikuona matanthwe a m’mapiri amene ali ndi zigawozigawo za miyala yosiyanasiyana zimene zayalana mooneka ngati mapisi a buledi wopaka majalini. Kuno kumapezeka miyala ya m’nthawi zosiyanasiyana chilengedwere dziko lapansi. Ina mwa miyalayi ndi ya mchenga wosakanikirana ndi dothi, ndipo ina inapangidwa ndi zinyama ndi zomera zimene zinafa. Kwa zaka mazanamazana, zomera ndi zinyama zambiri zakufa zinakwiririka ndi dothi ndipo zinawolerana. Ndipotu, zowolerana zimenezi zimapezeka m’miyala imene inapangidwa m’nyengo zakale zosiyanasiyana.

Titapita ku malo osungirako zinthu zakale ku Svalbard, tikuyang’anitsitsa zinyama ndiponso zomera zosiyanasiyana zimene zinafa kalekale n’kuwolerana ndipo tikuona kuti zina n’za kumadera otentha. Zimenezi zikusonyeza kuti dera la zilumbali linali lotentherapo m’masiku akale kusiyana ndi masiku ano. M’malo ena a ku Svalbard, miyala ya malasha imapanga zigawozigawo zomwe zimachindikala mpaka mamita asanu. M’miyala ya malasha imeneyi mwapezeka zowolerana za yomwe masamba ake amayoyoka ndi ina yomwe masamba ake sayoyoka. M’zinthu zowoleranazi mwapezeka zidindo za mapazi a zinyama zikuluzikulu zakale kwambiri zotchedwa dinosaur, ndipo zimenezi zikupereka umboni wina wakuti kale derali linali lotentherapo ndipo linali ndi zomera zambiri.

Kodi kusintha kwakukulu kwa nyengoku kukuchitika chifukwa chiyani? Tikufunsa katswiri wa za matanthwe, Torfinn Kjaernet, yemwenso ndi woimira bungwe la za migodi la Directorate of Mining ku Longyearbyen. Iye akutiuza kuti akatswiri ambiri akuganiza kuti chifukwa chachikulu chimene chikuchititsa zimenezi ndicho kusuntha kwa matanthwe a pansi padziko. Akatswiriwa amati pansi pa chilumbachi pali thanthwe limene lakhala likusuntha kwa nthawi yaitali molowera chakumpoto, ndipo n’kutheka kuti linachokera kutali kwambiri cha kum’mwera pafupi ndi pakati penipeni padziko lapansi. Malingana ndi zimene asayansi akuona akamaunika ali mlengalenga, chaka chilichonse chilumba cha Svalbard chikusunthabe masentimita angapo molowera kumpoto chakum’mawa.

Pamene ndege yathu ikunyamuka kuchoka ku Svalbard, tikuona kuti ulendo wathuwu watipatsa zinthu zambiri zoti tiziganizire mwakuya. Nthaka yaikulu yopanda zomera zambiri, zinyama zomwe zimatha kukhala bwinobwino kuderali, ndiponso mitundu yosiyanasiyana ya zomera, zatichititsa kuti tiganizire za kuchuluka kwa zinthu zachilengedwe, ndiponso kuchepa kwa munthu pomuyerekezera ndi zinthu zimenezi. Komansotu taganizira mwakuya mmene anthufe timakwaniritsira udindo wathu wosamalira dziko lapansi. Pamene ndege yomwe takwera ikuuluka n’kulowera kum’mwera, tikuyang’ana komaliza dera lozizira kwambiri la m’mphepete mwa nyanjali, ndipo tikuona nsonga za mapiri zikutulukira m’mitambo. Nsongazi n’zokutidwa ndi chipale chofewa ndipo zikuoneka zonyezimira mofiira pang’ono chifukwa cha kuwala kwa dzuwa.

[Mapu patsamba 24]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Kumpoto Kwenikweni kwa Dziko Lapansi

GREENLAND

SVALBARD

Longyearbyen

ICELAND

NORWAY

RUSSIA

[Chithunzi patsamba 25]

Tawuni ya Longyearbyen

[Chithunzi patsamba 25]

Maluwa ambiri, monga awawa, amapirira nyengo yozizira kwambiri ya kuderali

[Mawu a Chithunzi]

Knut Erik Weman

[Zithunzi patsamba 26]

Mbalame ya kuderali yooneka ngati nkhuku, ndiponso nyama yangati mphalapala

[Mawu a Chithunzi]

Knut Erik Weman