Makhalidwe Akulowa Pansi Padziko Lonse
Makhalidwe Akulowa Pansi Padziko Lonse
“KUBA ndi chinyengo zili paliponse,” anatero David Callahan m’buku lake lofotokoza za chinyengo laposachedwapa. Anatchula zinthu zimene zikuchitika ku United States ngati “kubera mayeso kwa ana a sukulu, kujambula nyimbo ndi mavidiyo popanda chilolezo, kuba ku ntchito, chinyengo popereka thandizo la zamankhwala,” ndiponso kumwa mankhwala owonjezera mphamvu pochita mpikisano wa zamasewera. Anamaliza ndi kunena kuti: “Mukaphatikiza zinthu zonse zimene anthu akuchita posatsatira khalidwe labwino kapena malamulo, muona kuti makhalidwe akulowa pansi kwambiri.”
Nyuzipepala ya The New York Times inati mphepo yamkuntho ya Katrina, itawomba ku United States kumapeto kwa chaka cha 2005, “kunali chinyengo chachikulu ndipo boma linalephereratu kuyendetsa zinthu. Zinthu zimenezi zinali zisanachitikepo m’nthawi yathu ino.” Phungu wina ku United States anasimba kuti: “N’zodabwitsa kwambiri kuti anthu ankachita chinyengo mosabisa ndi mopanda manyazi, ndiponso anthu anawononga chuma chosaneneka.”
N’zoona kuti alipo anthu ena amene amadzipereka posonyeza ena chikondi. (Machitidwe 27:3; 28:2) Koma nthawi zambiri timamva anthu ena akufunsa kuti: “Kodi ineyo ndipeza chiyani pamenepa? Kodi ndipindulapo chiyani?” Anthu ambiri ayamba kudzikonda kwambiri ndi kumangofuna zawo zokha.
M’mbuyomo, akuti kudzikonda ndi makhalidwe oipa kunathandizira kwambiri kugwetsa maufumu ena akuluakulu, monga ufumu wa Roma. Kodi n’kuthekanso kuti zinthu zimene zikuchitika masiku ano, zikulosera chinthu china chachikulu m’tsogolo? Kodi “kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo,” kumene Baibulo linalosera kukhala chizindikiro cha mapeto a dzikoli, kukuchitikadi kulikonse?—Mateyo 24:3-8, 12-14; 2 Timoteyo 3:1-5.
Makhalidwe Akuipa pa Dziko Lonse
Mu Africa News ya June 22, 2006, munali nkhani yonena za “msonkhano wokambirana za kugwiriridwa ndi kuonera zithunzi zolaula” zimene zikuchitika ku dera lina losauka ku Uganda. Inati “uhule ndi mankhwala osokoneza bongo zikuchuluka chifukwa chakuti makolo sakusamaliranso ana awo.” Nkhani yomweyi inanenanso kuti: “Mkulu wa polisi woyang’anira chitetezo cha ana ndi mabanja papolisi ya Kawempe, a Dhabangi Salongo, anati kuchitira nkhanza ana ndi nkhanza m’banja zachuluka kwambiri.”
Dokotala wina ku India ananena kuti, “anthu akutaya chikhalidwe chawo.” Mkulu wina woyang’anira ntchito yokonza mafilimu ku India komweko ananenanso kuti, “mankhwala osokoneza bongo ndi chiwerewere zimene zachulukazi ndi umboni winanso wakuti dziko la India likutaya chikhalidwe chake potengera makhalidwe oipa a mayiko a ku Ulaya ndi ku North America.”
Mlembi wamkulu wa bungwe loona za mgwirizano pakati pa amuna ndi akazi, ku Beijing m’dziko la China, dzina lake Hu Peicheng, ananena kuti: “Kale anthufe tinkadziwa chabwino ndi choipa. Koma masiku ano, timangochita chilichonse chimene tikufuna.” Nkhani ina m’magazini ya China Today inati: “Anthu sakuonanso cholakwika ngati munthu amene ali pabanja agonana ndi munthu wina.”
Nyuzipepala ina ku England posachedwapa inati: “Zikuoneka kuti anthu alibenso manyazi ndi kudzivula akamasatsa malonda. Kale
zimenezi zikanakwiyitsa anthu. Masiku anu tikuona zinthu zolaula paliponse ndipo anthu sakuchitanso manyazi ndi zithunzi zolaula.” Nyuzipepala yomweyi inanenanso kuti: “Mabuku ndi mafilimu omwe kale ankapangidwira anthu opitirira zaka 18, tsopano akutengedwa kukhala a banja lonse. Ndipo anthu otsutsa khalidwe loonera zithunzi zolaula akuti, mabuku ndi mafilimu amenewa nthawi zambiri akupangira ana.”Magazini ya The New York Times inanena kuti: “[Achinyamata ena] amakambirana za [kugonana kwawo] ngati kuti akukambirana za zimene adya tsiku limenelo.” Magazini inanso yothandiza makolo a ana a zaka 8 mpaka 12 inati: “Mtsikana wina, polemba uthenga womvetsa chisoni ndi zilembo zosonyeza kuti walemba ndi mwana, anati: ‘Amayi anga akundikakamiza kukhala ndi zibwenzi ndi kugonana ndi anyamata. Koma ndili ndi zaka 12 zokha . . . ndithandizeni!’”
Zinthu zasinthadi! Nyuzipepala ina ku Canada ya Toronto Star inati osati kale kwambiri “anthu ankaona kukwatirana kwa amuna ndi akazi okhaokha kukhala khalidwe loipa kwambiri.” Koma mphunzitsi wa chikhalidwe cha anthu pa yunivesite ya Carleton ku Canada, dzina lake Barbara Freemen, anati: “Masiku ano anthu amati, ‘Tili ndi ufulu wochita zimene tikufuna. Sitikufuna anthu ena kulowerera.’”
N’zosachita kufunsa kuti kumadera ambiri pazaka makumi angapo zapitazo, makhalidwe a anthu alowa pansi kwambiri. N’chifukwa chiyani zinthu zasintha kwambiri chonchi? Kodi inuyo mumati bwanji mukaona kusintha kotere? Ndipo kodi kusintha kumeneku kukulosera chiyani m’tsogolo?