Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ Zipangizo zoyendera magetsi zimene amangozisiya osazizimitsiratu, zimachititsa kuti mabilu a magetsi akwere ndi 5 peresenti m’mabanja ambiri a ku Canada.—ZACHOKERA MU NYUZI YA NATIONAL POST, KU CANADA.
▪ Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu ambiri a ku Russia amakhulupirira kuti zinthu zofunika kwambiri zoti boma lilimbane nazo ndi “katangale ndi ziphuphu” ndiponso “kukwera mitengo kwa zinthu.”—ZACHOKERA MU NYUZI YA PRAVDA, KU RUSSIA.
▪ Malinga ndi zotsatira za kafukufuku wina, ana asukulu opitirira 26 pa 100 aliwonse, osakwana zaka 13 a ku Taiwan “anaganizapo zodzipha.”—ZACHOKERA MU NYUZI YA THE CHINA POST, KU TAIWAN.
▪ “Luso lamakono lathandiza kuchepetsa kwambiri nthawi yomwe anthu ankagwira ntchito ku United States. Komabe anthu ogwira ntchitoyo tsopano sakupezanso nthawi yopuma chifukwa cha maulendo aatali opita ndi kubwera kuntchito, anthu akuluakulu akupitirizabe sukulu, ndiponso ntchito zapakhomo zikuchuluka.”—ZACHOKERA MU MAGAZINI YA FORBES, UNITED STATES.
▪ Kuchokera mu 2003 mpaka 2004, mpweya woononga chilengedwe wochekera m’makampani a m’mayiko olemera unawonjezereka ndi 1.6 peresenti, ndipo kuwonjezeka kumeneku “n’kwakukulu kwambiri kuposa kumene kunachitikapo m’zaka khumi zapitazo.”—ZACHOKERA KU REUTERS, OSLO, NORWAY.
Vuto la Madzi M’dziko la China
M’dziko la China muli vuto la “kuwonongedwa ndiponso kuchepa kwa madzi.” M’mizinda yambiri muli madamu ndi mathanki oyeretsera madzi oipa, koma mizinda yochuluka ilibe ndalama zoyendetsera ntchitoyi. Magazini ina (The Wall Street Journal) inati: “Mitsinje yambiri ya m’dzikoli, nyanja ndiponso ngalande n’zoipitsidwa chifukwa cha zonyansa zochokera m’makampani ndi m’zinyumba komanso mankhwala ophera tizilombo ochokera m’mafamu osiyanasiyana.” Ndipotu “anthu pafupifupi 300 miliyoni sakwanitsa kupeza madzi abwino.” Magaziniyo inati zinthu “sizili bwino ngakhale pang’ono,” ndipo zikuipiraipira.
“Kodi Mukufuna Mukhale Ngati Amboni?”
Chaka chatha, kunyanja ya pachilumba cha Elba ku Italy, achinyamata ena achikatolika ankayesa kulankhula ndi alendo odzaona nyanja pomvera pempho la bishopu wa dayosisi ya Massa Marittima-Piombino. Bishopuyo anawauza kuti ngati akufuna kukhalabe Akhristu, ayenera kulalikira chikhulupiriro chawo. Zimenezi zinadabwitsa alendowo. Nyuzipepala ina (Il Tempo) inati, anthu ambiri ankauza achinyamatawo kuti, “Kodi mukufuna mukhale ngati Amboni?”
Nyimbo Zolimbikitsa Chiwerewere
Bungwe lina (Associated Press) linati pa kafukufuku wina anapeza kuti achinyamata amene amamvetsera nyimbo “zokhala ndi mawu otukwana” amayamba “mwamsanga kuchita zachiwerewere kusiyana ndi amene amakonda nyimbo zina. “M’posavuta kuti achinyamata ayambe msanga zachiwerewere chifukwa chomvera nyimbo zomwe zimatama amuna pankhani ya kugonana, n’kumachemerera akazi chifukwa cha mmene amaimitsira mitu amuna, komanso n’kumatchula nkhani za kugonana mosabisa mawu. Koma nyimbo zomwe zimatchula nkhanizi mophiphiritsa komanso mokhala ngati kuti zikuchitika pakati pa anthu amene ali paubwenzi wa moyo wawo wonse sizitero.” Maganiziyo inati “Makolo, aphunzitsi ngakhalenso achinyamatawo ayenera kusamala ndi nyimbo zimene amamvetsera.”
Anthu Akusakaza Zakudya
M’chaka cha 2004, anthu a ku Australia anataya zakudya za ndalama zopitirira madola 4 biliyoni, linatero bungwe lina la zofufuzafufuza (The Australia Institute). Zakudya zimene anatayazi ndalama zake n’zowirikiza nthawi 13 poziyerekezera ndi ndalama zimene dzikoli linatumiza kunja pothandiza mayiko osauka m’chaka cha 2003. Chaka chilichonse, ndalama zonse zimene dzikoli limawononga pa zinthu zomwe sazigwiritsa ntchito n’komwe, n’zoposa madola 8.1 biliyoni. Ndalamazitu n’zochuluka zedi kuposa zimene dzikoli limagwiritsa ntchito posamalira mayunivesite ndi pokonzetsera misewu.