Mkokomo wa “Mzinda Wamuyaya”
Mkokomo wa “Mzinda Wamuyaya”
YOLEMBEDWA KU ITALY
Munthu wina wa ku Italy, dzina lake Ottorino Respighi, anafika popeka nyimbo yakuti “Akasupe a ku Rome,” chifukwa choona ndiponso kumva mkokomo wa akasupe ochititsa kaso ambirimbiri a mumzindawo. Tiyeni tikaone kasupe mmodzi wochititsa chidwi kwambiri ku Rome, wotchedwa Trevi.
Tikuyenda mumsewu waung’ono wolowera kumene kuli kasupeyu ndipo tikukhota, kenaka tikuona chinthu chonyamula mtima zedi. Chinthu chake ndi kasupe wamkulu wotchedwa Trevi, yemwe ndi wamkulu mamita 20 mlifupi ndipo ndi wamtali mamita 26. Kasupeyu ndiye chinthu chochititsa kaso kwambiri m’kachigawo konseko ka mzindawu.
Papa Kilementi wa chi 12 ndiye analamula kuti amange kasupe wa Trevi ndipo Mtaliyana wina, dzina lake Niccolò Salvi, ndiye anajambula mapulani a kasupeyu. Ntchito imeneyi inayamba mu 1732 ndipo inatha mu 1762. Madzi a kasupeyu amachokera mu ngalande yomwe inakumbidwa m’zaka 100 nthawi ya atumwi isanafike, yotchedwa Aqua Virgo, imene ili yotalika makilomita 13.
Kasupeyu ali kumaso kwa nyumba yakale ya mafumu ndipo anam’panga mofanizira nyanja. Pakhoma la nyumbayo pali chiboliboli chachikulu cha mulungu wa Aroma wotchedwa Oceanus, (amene ena amamutcha kuti Neptune). Chibolibolichi chili pa galeta lopangidwa ngati chigoba cha nkhono, ndipo chimasonyeza mulunguyo akulamulira mathithiwo. Madzi akamayenderera m’ziboliboli ndiponso m’miyala yomwe ili pa kasupeyu, amachita mkokomo ngati wa mafunde a mphepete mwa nyanja. Damu limene mumalowa madzi a kasupeyu n’lalikulu kwambiri, moti nyumba zonse za m’kachigawo kameneka, zimaoneka ngati kuti zinagundizana ndi kasupeyo.
Tsiku lililonse, ku malo amenewa kumabwera alendo ankhaninkhani kuposa malo ambiri mumzinda wa Rome, ndipo amaponya ndalama zachitsulo m’damulo. Kamodzi pamlungu uliwonse, madzi onse a m’damulo amatulutsidwa. Zikatero, amatolera ndalama zonse zimene alendowa anaponyamo n’kukazipereka ku bungwe linalake lachipembedzo, lothandiza osowa. Mlungu uliwonse amapeza ndalama zokwana madola pafupifupi 11,000.
Respighi, amene anapeka nyimbo uja ananena kuti mkokomo wa kasupeyu umamveka ngati mawu a oyimba. Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti kasupe wa ku Trevi ndiye woimba yemwe ali ndi mawu amphamvu kwambiri mumzindawo. Chifukwatu alendo ambiri amakonda kwambiri kukaona kasupe ameneyu akafika ku Rome, womwe amati ndi Mzinda Wamuyaya.