Kodi Ndizichita Masewera a Pakompyuta?
Zimene Achinyamata Amadzifunsa
Kodi Ndizichita Masewera a Pakompyuta?
MASEWERA a pakompyuta si masewera a pamwamba chabe. Masewerawa amafuna luso ndipo amathandiza munthu kuti asasungulumwe. Komatu sizokhazi. Masewera a pakompyuta amathandiza munthu kuti azichita zinthu mochangamuka, ndipo kafukufuku amasonyeza kuti kuchita masewera amenewa kumathandiza munthu kuti maso ake aziona bwino. Ena mwa masewera amenewa angathandize munthu kudziwa masamu ndiponso kuwerenga bwino. Kuwonjezera pamenepo, anthu ambiri kusukulu amakonda kukambirana za masewera a pakompyuta amene angotuluka kumene. Ngati wina wachitapo masewera atsopanowo, ndiye kuti amakhala ndi zokamba kwa anzake.
Makolo anu ndi amene angakhale ndi udindo wokuvomerezani kuchita masewera a pakompyuta. (Akolose 3:20) Ngati atakulolani kuti muzichita masewerawa, muyenera kusankha masewera osangalatsa ndiponso abwino. Komabe, n’chifukwa chiyani muyenera kusamala kwambiri posankha masewerawo?
Kuopsa Kwa Masewera a Pakompyuta
Brian, yemwe ndi wa zaka 16 anati: “Masewera a pakompyuta ndi osangalatsa kwambiri.” Koma mwina mungavomereze kuti, si masewera onse omwe ndi abwino. Brian ananenanso kuti: “Ukamachita masewerawa umapanga zinthu zomwe zitakhala kuti ndi zenizeni,
zingakubweretsere mavuto aakulu.” Kodi masewerawa amalimbikitsa khalidwe lotani?Masewera ambiri amalimbikitsa chiwerewere, mawu achipongwe ndiponso chiwawa. Koma Baibulo limatsutsa makhalidwe onsewa. (Salmo 11:5; Agalatiya 5:19-21; Akolose 3:8) Masewera ena amatamanda zamizimu. Pofotokoza masewera ena otchuka, Adrian wa zaka 18 anati: “Masewerawa amaonetsa kumenyana kwa magulu a anthu, kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, kuchita chiwerewere poyerayera, kutukwana, chiwawa chosaneneka ndi kukhetsa magazi.” Ndipo pakatuluka masewera atsopano, akale aja amakhala osasangalatsa. James, wa zaka 19 anati, ena mwa masewera otchuka kwambiri amenewa ndi oti ungathe kusewera ndi anthu ena pa Intaneti. Zimenezi zapangitsa kuti masewera a pakompyuta apite patsogolo kwambiri. James ananenanso kuti: “Pakompyuta yanu mutha kumapikisana ndi anthu amene a ku mayiko ena.”
Masewera omwe atchuka kwambiri masiku ano ndi akuti munthu umasankha kudziyerekezera ndi winawake kapena chinachake chotchuka. Munthu akamachita masewerawa, amasankha kuti akhale munthu, nyama, kapena zonse ziwiri. Pakompyutapo pamakhala anthu ena ambirimbiri omwenso akusewera. Ndipo pamakhalanso masitolo, magalimoto, nyumba, malo a zisangalalo, ndi nyumba zosungiramo mahule. Zimenezi zimakhaladi ngati zenizeni. Zidole za pakompyuta zikamalankhulana kapena kuchita zinthu zina, anthu amene akusewerawo amakhala akutumizirana mauthenga.
Kodi chimachitika n’chiyani? Mtolankhani wina anati: “ Anthu amachita zinthu zomwe sangazichite n’komwe pa moyo wawo.” Iye anapitiriza kuti: “Pamasewerawo, chiwerewere ndi uhule n’zofala kwambiri.” Kungothabwanya mabatani ochepa, anthu osewerawa angachititse zidole zawozo kuti zigonane, uku iwo akutumizirana mauthenga onena za kugonana. Kuwonjezera pamenepo, magazini ina (ya New Scientist) inati: “M’masewerawa mumakhala zachiwawa, zigawenga, anthu omwe amafufuza amuna oti agone ndi mahule, anthu olanda, achinyengo, ndi akupha anzawo.” Magazini inanso inati: “Anthu ambiri akudandaula chifukwa cha zinthu zosaloleka zimene zimachitika m’masewerawa, monga nyumba ya mahule imene mumaoneka osewera akugwirira hule, kapena anthu amene amachita zachiwerewere pogwiritsira ntchito tizidole tooneka ngati ana.”
N’chifukwa Chiyani Muyenera Kusankha Mwanzeru?
Anthu amene amachita masewera osonyeza zachiwawa kapena zachiwerewere amanena kuti “Palibe cholakwika, chifukwa si zenizeni. Ndimasewera chabe basi.” Koma musapusitsidwe ndi maganizo amenewa.
Baibulo limanena kuti: “Ngakhale mwana adziwika ndi ntchito zake; ngati ntchito yake ili yoyera ngakhale yolungama.” (Miyambo 20:11) Kodi mungatchedwe oyera ndi olungama ngati muli ndi chizolowezi chochita masewera a pakompyuta olimbikitsa chiwawa ndi chiwerewere? Kawirikawiri, kafukufuku amasonyeza kuti anthu amene amaonerera zinthu zachiwawa amakhala olusa. Magazini ya New Scientist posachedwapa inati: “Masewera a pakompyuta amasintha kwambiri khalidwe la munthu kusiyana ndi TV chifukwa choti munthu amachita nawo masewerawo osati kungoonerera chabe.”
Kuchita masewera osonyeza chiwawa ndi chiwerewere kuli ngati kusewera ndi zinyalala zotsalira popanga mabomba zomwe ndi za poizoni. Kuopsa kwa zinthu zimenezi sikuonekera msanga koma ndi kosapeweka. Chifukwa chiyani tikutero? Chifukwa poizoni wa muzinyalalazi amalowa m’mimba ndi kuwononga matumbo, kenako mabakiteriya ochokera m’matumbo amalowa m’magazi ndipo m’kupita kwa nthawi munthu amayamba kudwala. Mofanana ndi zimenezi, kuonera zinthu zachiwerewere ndi chiwawa kungawononge ‘makhalidwe anu abwino’ ndipo mungayambe kuganiza ndi kuchita zinthu zimene thupi limalakalaka.—Aefeso 4:19; Agalatiya 6:7, 8.
Kodi Ndisankhe Masewera a Mtundu Wanji?
Ngati makolo anu akulolani kuchita masewera a pakompyuta, kodi mungadziwe bwanji masewera oyenera kusankha ndiponso nthawi imene mungathere posewera? Dzifunseni mafunso otsatirawa:
▪ Kodi zimene ndasankha zingakwiyitse Yehova? Masewera amene mungasankhe angakhudze ubwenzi wanu ndi Mulungu. Lemba la Salmo 11:5 limati: “Yehova ayesa wolungama mtima: Koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.” Ponena za anthu amene amachita zamizimu, Mawu a Mulungu amati: “Aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.” (Deuteronomo 18:10-12) Ngati tikufuna kukhala mabwenzi a Mulungu, tiyenera kutsatira malangizo a pa Salmo 97:10 akuti: “Inu okonda Yehova, danani nacho choipa.”
▪ Kodi masewerawa angakhudze bwanji mmene ndimaganizira? Dzifunseni kuti, “Kodi kuchita masewera amenewa kungachititse kuti ndivutike ‘kuthawa dama’?” (1 Akorinto 6:18) Masewera amene amaonetsa zithunzi kapena mawu oyambitsa chilakolako cha kugonana, sangakuthandizeni kuganizira zinthu zolungama, zoyera, ndi zabwino. (Afilipi 4:8) Amy wa zaka 22 anati: “Masewera ambiri amachititsa munthu kuona zinthu monga chiwawa, kutukwana, ndi chiwerewere kuti sizoipa kwenikweni. Ndiponso angachititse munthu kugonja pa ziyeso zosiyanasiyana. Choncho tiyenera kukhala osamala kwambiri ndi masewera amene tasankha kuchita.”
▪ Kodi ndingasewere kwa nthawi yaitali bwanji? Deborah wa zaka 18 anati: “Ndimaona kuti si masewera onse a pakompyuta omwe ndi oipa. Koma angakhale odya nthawi kwambiri, ndipo ukayamba kusewera sufuna kusiya.” Ngakhale masewera omwe ndi abwino, angadye nthawi yambiri. Choncho, lembani nthawi imene mumathera posewera ndipo yerekezerani ndi nthawi imene mumathera kuchita zinthu zina zofunika kwambiri. Zimenezi zidzakuthandizani kuchita zinthu zofunika panthawi yake.—Aefeso 5:15, 16.
Baibulo silimanena kuti tizingokhalira kuphunzira kapena kugwira ntchito nthawi zonse. Limatikumbutsa tonsefe kuti pali “mphindi yakuseka. . . ndi mphindi yakuvina.” (Mlaliki 3:4) Dziwani kuti mawu akuti ‘kuvina’ sakutanthauza kungosewera, koma kuchitanso zinthu zina zolimbitsa thupi. Choncho, bwanji osapatula nthawi yochita masewera ena olimbitsa thupi m’malo mongokhala muli dwii pa kompyuta?
Sankhani Mwanzeru
Mosakayikira, masewera a pakompyuta amakhala osangalatsa kwambiri, makamaka ngati mukuwadziwa bwino. N’chifukwa chake muyenera kusankha masewera mwanzeru. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimakhoza bwino maphunziro ati kusukulu?’ Kodi maphunziro amenewo si amene mumawakonda? Umu ndi mmene zimakhalira kuti mukamakonda kwambiri phunziro linalake m’pamene mumalidziwa bwino kwambiri. Tsopano dzifunseni kuti: ‘Kodi ndi masewera ati a pakompyuta amene ndimawakonda kwambiri? Ndipo amandiphunzitsa makhalidwe otani?’
Kuti muthe kusankha bwino, lembani mwachidule masewera aliwonse omwe mukufuna kuchita, fotokozani cholinga cha masewerawo ndiponso njira zomwe mugwiritse ntchito kuti mukwanitse cholingacho. Onani ngati zimene mwapezazo zikugwirizana ndi mfundo za m’Baibulo zimene zafotokozedwa mu nkhani ino, ndipo kenako dzifunseni ngati masewerawo ali oyenerera.
M’malo mongochita masewera chifukwa chokopeka ndi anzanu, limbani mtima kusankha nokha zochita. Chofunika kwambiri ndicho kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Nthawi zonse muzitsimikiza kuti cholandirika kwa Ambuye n’chiti.”—Aefeso 5:10.
Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.dan124.com.
ZOTI MUGANIZIRE
▪ Kodi mungatani mnzanu atakuuzani kuti mukachite masewera a pakompyuta osonyeza zachiwawa kapena zachiwerewere?
▪ Kodi mungatsimikize bwanji kuti kuchita masewera a pakompyuta sikukusokoneza zinthu zofunika kwambiri?
[Mawu Otsindika patsamba 19]
Kuchita masewera osonyeza chiwawa ndi chiwerewere kuli ngati kusewera ndi zinyalala zotsalira popanga mabomba zomwe ndi za poizoni. Kuopsa kwa zinthu zimenezi sikuonekera msanga koma ndi kosapeweka
[Bokosi patsamba 18]
Kodi mumachita kangati masewera a pakompyuta?
□ Si kawirikawiri
□ Kamodzi pa mlungu
□ Tsiku lililonse
Kodi mumachita masewerawa kwa nthawi yaitali bwanji?
□ Mphindi zowerengeka
□ Ola limodzi kapena osakwana
□ Kupitirira maola awiri
Kodi mumakonda kwambiri masewera ati?
□ Mpikisano wa magalimoto
□ Masewera monga mpira
□ Masewera owombera anthu
□ Ena aliwonse
Lembani apa masewera a pakompyuta amene mukuona kuti si abwino
․․․․․
[Bokosi/Chithunzi patsamba 21]
MAWU KWA MAKOLO
Monga momwe mwaonera mu nkhani yapitayi, masewera a pa kompyuta asintha kwambiri kuchokera panthawi imene inu munali wachinyamata. Popeza ndinu kholo, kodi mungathandize bwanji mwana wanu kuti athe kuzindikira zoopsa zomwe zingabwere chifukwa cha masewerawa ndiponso m’mene angazipewere?
Sizingakhale zothandiza kunena kuti masewera onse ndi oipa kapena kuti kuchita masewera a pakompyuta ndi kutaya nthawi. Kumbukirani kuti, si masewera onse omwe ndi oipa. Komabe, kuchita masewerawa kumadya nthawi ndiponso ukayamba kusewera sufuna kusiya. Motero pezani nthawi yofufuza kuti mudziwe kuchuluka kwa nthawi imene mwana wanu amathera pochita masewerawa. Fufuzani mtundu wamasewera omwe mwana wanu amakonda. Ndiponso mungathe kufunsa mwana wanu mafunso ngati awa:
▪ Kodi anzako akusukulu amakonda masewera otani?
▪ Kodi chimachitika n’chiyani pochita masewerawo?
▪ Kodi ukuganiza kuti n’chifukwa chiyani anzako amakonda kwambiri masewerawo?
Mudzaona kuti mwana wanu amadziwa zambiri zokhudza masewera a pakompyuta kuposa mmene mukuganizira. Mwina n’kutheka kuti iye wachitapo masewera ena amene inuyo mumaona kuti si oyenera. Ngati zili choncho, upezeni mtima. Umenewu ndi mwayi wanu kuti muthandize mwana wanu kukhala ndi luntha la kuzindikira.—Aheberi 5:14.
Funsani mafunso amene angathandize mwana wanu kuzindikira chifukwa chake anthu ambiri amakonda masewera osayenera. Mwachitsanzo mungafunse mafunso ngati awa:
▪ Kodi umaona kuti ndiwe wotsalira chifukwa chakuti suloledwa kuchita masewera ena?
Monga tafotokozera pa tsamba loyamba la nkhani yapitayi, achinyamata ambiri amachita masewera a pakompyuta n’cholinga chakuti akhale ndi zokamba akakumana ndi anzawo. Ngati zili choncho ndi mwana wanu, nkhani imeneyi mungaisamalire mosiyana ndi mmene mungachitire ngati mwadziwa kuti mwanayo amakonda masewera osonyeza zachiwawa kapena zachiwerewere.—Akolose 4:6.
Bwanji ngati mwana wanu amakonda masewera oipa? Achinyamata ena anganene mwamsanga kuti masewera achiwawa chosaneneka sasintha maganizo awo. Iwo anganene kuti, ‘Ndikamachita zimenezi pakompyuta sizitanthauza kuti ndingazichitedi.’ Ngati mwana wanu ali ndi maganizo amenewa, mungakambirane naye lemba la Salmo 11:5, limene lagwidwa mawu pa tsamba 20. Mawu a palembali akusonyeza momveka bwino kuti Mulungu samangodana ndi anthu ochita chiwawa okha, koma amadananso ndi anthu okonda chiwawa. Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito pa nkhani ya chiwerewere ndi makhalidwe ena oipa amene Mawu a Mulungu amaletsa.—Salmo 97:10.
Akatswiri ena amapereka malangizo otsatirawa:
▪ Musalole ana anu kuchita masewera a pakompyuta ali kwaokha monga kuchipinda chogona.
▪ Khazikitsani malamulo (monga akuti, osasewera musanamalize ntchito ya kusukulu, musanadye chakudya chamadzulo kapena musanachite zinthu zina zofunika kwambiri).
▪ Auzeni ubwino wochita masewera ena olimbitsa thupi.
▪ Khalani pomwepo ana anu akamachita masewera a pakompyuta. Ndipo nthawi zina mungachite bwino kusewera nawo limodzi.
Ndipotu, kuti muthandize ana anu pa nkhani ya zosangalatsa, muyenera kulankhula nawo momasuka. Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Kodi ineyo ndimakonda kuwonerera masewera ndi mapulogalamu otani a pa TV?’ Musadzinamize, ana anu angadziwe ngati inu simuchita zimene mumawauza.