Zidole Zochita Zisudzo
Zidole Zochita Zisudzo
YOLEMBEDWA KU AUSTRIA
“III! Nyimbo zija zinali zokoma, koma zidole zija n’zimene zandigometsa kwambiri. Zaposa zidole zina zonse zomwe ndaonererapo m’zisudzo zoterezi chifukwa zimatha kuchita chilichonse.”
Kodi munthuyu akufotokoza za zisudzo zoonera ana? Ayi. Simungamvetse kuti munthu wamkulu ndi amene anafotokoza mawu amenewa, atakaonera zisudzo zochitidwa motsatira nyimbo. Kodi n’kuti kumene zisudzo zochititsa chidwizi zimachitikira? Zimachitikira m’chinyumba china chokongola kwambiri mu mzinda wa Salzburg, m’dziko la Austria. Mzindawu ndi kwawo kwa katswiri wotchuka kwambiri wopeka nyimbo dzina lake Mozart.
Komano kodi munamvapo za zidole zochita zisudzo? Izi ndi zimene zidole za gulu la zisudzo la Salzburg Marionette Theatre zimachita. Zidolezi zikalowa m’bwalo, anthu oonerera amasangalala kwambiri. Amafika mpaka poiwala zochitika kunja kuno, n’kuyamba kuganiza zoti ali m’dziko lina labwino kwambiri ndiponso lanyimbo zokoma kwabasi.
Zisudzo za Zochitika Zenizeni ndi Zongoganizira
Poyamba kuonetsa zisudzuzo, amayamba ndi nyimbo kenaka amachotsa chinsalu chotchinga bwalo lasewero, ndipo akatero nthawi zina anthu oonerera samvetsa zinthu zimene akuona. Iwo amadabwa kwambiri kuona zidole zikuyendayenda pa bwalopo n’kumayendetsayendetsa manja ngati kuti zikuimbadi. Samvetsanso kuona tizingwe tambirimbiri pamitu ya zidolezo. Ena mwa iwo angathe kukhumudwa n’kumati, ‘Tizingwe toyendetsera zidolezi tikuchita
kuonekeratu.’ Komanso m’nyumbamo simuoneka anthu oimba. Poyamba, anthu ena oonera sasangalala ndi zoti pazisudzozi azikhala ndi nyimbo zojambuliratu. Munthu wokonda kuonera zisudzo za nyimbo angathe kukhumudwa n’kumati, ‘Ndangotaya nthawi yanga pano.’ Koma ndi bwino kufatsa kaye! Oonerawo amayamba kukopeka pang’ono ndi pang’ono.Zikatero, zidole zija zimayamba kuwasangalatsa. Zimachita zinthu zomwe zimachitikadi m’moyo ndi zina zoti sizingachitike n’komwe. Munthu saganiziranso za tizingwe toyendetsera zidole tija. Kuwonjezera pa kuchita chidwi ndi zochita za zidolezo, oonererawo amachitanso chidwi ndi nzeru imeneyi. Pasanapite nthawi yaitali, amaona kuti imeneyi ndi nzeru yabwino kwambiri, ndipo amaiwalako zoti akuonerera zidole. Zoonadi, zidolezi zimatha kusangalatsa ngakhale anthu omwe poyamba amazikayikira, mpaka kufika poiwalako zochitika kunja kuno.
Zochitika pa Bwalo Lasewero Ndiponso M’mwamba Mwake
M’mwamba mwa bwalo lasewerolo mumachitika zinthu zosangalatsanso kwambiri ngati zomwe zikuchitika pabwalopo. Anthu omwe amavinitsa zidolezo, omwe amakhala m’mwamba mwa bwalolo ndiwo kwenikweni ali akatswiri a zisudzozo. Iwo amachititsa zidole zija kuti zizikhala ngati zikuimba, kulira, kumenyana ndi mfuti kapena malupanga, kapenanso kuchitirana ulemu. Izitu n’zofanana kwambiri ndi zimene anthu enieni ochita zisudzo zimenezi amachita.
Nyuzipepala ina inafotokozapo zimene zimachititsa kuti luso limeneli likhale losangalatsa kwambiri. Inati: “M’mwamba mwa bwalolo, anthu amatha kuchita mbali iliyonse m’sewerolo mosaganizira misinkhu yawo, kayanso kuti ndi amuna kapena akazi. Amangofunika kukhala ndi luso lapadera kwambiri.” (The New York Times) Ndipo anthu omwe amavinitsa zidole ku Salzburg, mpaka kufika pochita zinthu ngati anthu enieni, n’ngaluso lapamwamba kwambiri.
Anasankha Zidole M’malo mwa Ziboliboli
Gulu la Salzburg Marionette Theatre lakhala likuyenda bwino kwambiri kwazaka zoposa 90 tsopano. Gululi linaonetsa sewero lake koyamba
mu 1913 potengera sewero lina la Mozart. Anton Aicher, katswiri wosema ziboliboli, ndiye anayambitsa gululi. Aicher anakaphunzira ku Munich ndipo kenako anasema zidole zotha kupanga zinthu zimene anthu angapange. Sipanatenge nthawi yaitali kuti ayambe kusangalala ndi ntchito imeneyi kusiyana ndi kusema ziboliboli zoti anthu azigwiritsa ntchito paguwa, zomwe sizingachite chilichonse.Patatha nthawi yochepa chiyambire zimenezi, banja lonse la Aicher linatengeka ndi sewerolo. Abale akewo anam’thandiza kusoka zovala za zidolezo ndiponso kuimba nyimbo ndi kuchita mbali zina zolankhula zomwe zinkafunika pa sewerolo. Zinthu zinawayendera bwino kwambiri moti patangotha nthawi pang’ono iwo anayamba kukonza ndi kuonetsa zisudzo za nyimbo zinanso. Ndipo kuchokera mu 1927 mpaka pano, gululi lakhala likuitanidwa kuti likaonetse zisudzo zake m’mayiko ena. Masiku ano, m’mayiko angapo monga Japan ndi United States, sizachilendo kuona zidolezi. Anthu azikhalidwe zonse amasangalala nazo kwambiri.
Kodi Mungakonde Kuonera Zimenezi?
Buku lina lotanthauzira mawu limati zisudzo zoterezi kwenikweni ndi “masewero omwe amachitika motsatira nyimbo zazing’wenyeng’wenye zimene oimba ake nthawi zambiri amavala zovala zapadera.” (The Concise Oxford Dictionary of Music) Mawu a nyimbo za m’zisudzozi amawatenga m’nthano, zochitika m’mbiri yakale, nkhani za m’Baibulo ndipo ena amangopeka. Nthawi zina angakhale ofotokoza zochitika zomvetsa chisoni, zachikondi kapena zinthu zongofuna kuseketsa anthu. Zisudzo za gulu la Salzburg Marionette Theatre nthawi zambiri zimakhala m’Chijeremani kapena Chitaliyana. Motero ndi bwino kuyamba mwawerenga mawu omasuliridwa ofotokozera sewerolo, kuti mudziwe ngati n’labwino kapena ayi.
Kodi n’chiyani chingathandize Mkhristu kudziwa ngati ndi bwino kuonera sewero linalake lotereli? Kodi ndi bwino kungoganizira za kutchuka kwa oimba ake? Kapena potengera kukoma kwa nyimbo zawo? Kapenanso nkhani ya m’sewerolo?
N’zodziwikiratu kuti monga momwe timachitira ndi zosangalutsa zonse, njira yabwino imene Mkhristu angadziwire kuti ndi bwino kuti amvere kapena kuonera zisudzo zoterezi ndiyo kuona ngati mawu ofotokozera zisudzozo akugwirizana ndi zimene mtumwi Paulo ananena. Iye anati: “Chomalizira abale, zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse za chikondi, zilizonse zoneneredwa zabwino, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi.”—Afilipi 4:8.
[Mapu patsamba 8]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
AUSTRIA
VIENNA
Salzburg
[Chithunzi patsamba 8]
Zidole zili chire kuti zichite zisudzo zosiyanasiyana
[Chithunzi patsamba 9]
Nyumba ya Zisudzo ya Salzburg Marionette Theatre
[Chithunzi patsamba 10]
Anton Aicher, yemwe anayambitsa zimenezi
[Mawu a Chithunzi]
By courtesy of the Salzburg Marionette Theatre
[Mawu a Chithunzi patsamba 8]
All photos on pages 8 and 9: By courtesy of the Salzburg Marionette Theatre