Anyani Odabwitsa a M’matanthwe
Anyani Odabwitsa a M’matanthwe
ANTHU ambiri akamva za anyani amaganiza za nkhalango za m’mayiko otentha. Pali mitundu ya anyani yochepa chabe imene imapezeka m’mayiko osatentha kwambiri. Komabe, pali mitundu iwiri yomwe ili yosiyana kwambiri ndi mitundu ina yonse ya anyani.
Pali anyani ena amene amayenda m’timagulu ting’onoting’ono m’nkhalango za mitengo ya mkungudza ndi mitengo ina, m’mapiri aatali otchedwa Atlas a kumpoto kwa Africa, omwe kumagwa chipale chofewa. * M’dera lina la matanthwe ku Gibraltar, mumapezeka gulu la anyani amenewa, pamtunda wa makilomita 300 cha kumpoto kwake. Dera limeneli lili kum’mwera kwenikweni kwa Ulaya.
Kodi asayansi amati zinatheka bwanji kuti anyaniwa apezeke kumeneko? Ena amati kale ku Ulaya kunali anyani ambirimbiri, motero anyani amenewa ndi otsala. Enanso amati atsamunda a ku Arabia ndi a ku Britain ndi amene anabweretsa anyaniwa. Palinso nthano zina zimene zimati anyaniwa anafika ku Ulaya kuchokera ku Africa kudzera m’ngalande ya pansi panthaka yomwe masiku ano akuti inaiwalika. Ngakhale sizikudziwika bwinobwino kuti anyaniwa anachokera kuti, mfundo ndi yakuti ndi anyani okhawo a m’tchire ku Ulaya konse.
Anyaniwa amakhala m’nkhalango ya mitengo ya mkungudza yomwe ili kumtunda kwa matanthwewa. Ngakhale kuti aliko ochepa chabe, mwina 100 basi, bungwe lina linati anyaniwa ndiwo “nyama zodziwika kwambiri pa chilumbachi.”—International Primate Protection League. *
Popeza kuti chaka chilichonse ku Gibraltar kumafika alendo 7 miliyoni okaona malo, nthawi zonse anyaniwa amapatsidwa chakudya ndi alendowa, ndipo amachita zinthu zosiyanasiyana zoseketsa. Ngakhale kuti amatolatola tizipatso tosiyanasiyana ta m’tchire, anyaniwa ali ndi luso lopemphapempha ndipo nthawi zina amangosomphola chakudya kwa alendowo. Aboma amawapatsanso zipatso zosiyanasiyana.
Anyaniwa samangokhalira kudya basi, komanso amachotsana nthata ndi kukonzanakonzana kuti azioneka bwino. Anyani aakazi ndi aamuna omwe amasamalira ndiponso kusewera ndi ana awo. Anyaniwa amakonda kukhala m’magulu, motero nthawi zina amakangana ndiponso kumenyana. Pofuna kuthamangitsa anyani ang’onoang’ono, anyani akuluakulu amawaopseza kapena kuwakuwiza. Komanso amachita phokoso lina lake lodabwitsa pogwiritsa ntchito mano awo. Zikuoneka kuti amachita zimenezi pofuna kukhazika mitima yawo pansi.
Inde, mpaka pano palibe akudziwa bwinobwino kuti anyaniwa anafika bwanji ku Gibraltar. Komabe anyani okonda anthuwa amakongoletsa dera la matanthwe limeneli, lomwe lili kufupi kwambiri ndi nyanja ya Mediterranean. Kunena zoona, pakanapanda anyaniwa dera la Gibraltar silikanakhala lochititsa chidwi chonchi.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 3 Anyaniwa alibe michira.
^ ndime 5 Anyaniwa ndi ofanana ndi anyani ena a ku Japan, omwe m’nyengo yozizira amakonda kusonkhana kumene kuli akasupe amadzi otentha. Anthu okaona akasupewa ku Japan amachita chidwi kwambiri ndi anyaniwa.