Nyimbo ndi Mphatso ya Mulungu Yotitsitsimula
Nyimbo ndi Mphatso ya Mulungu Yotitsitsimula
YOLEMBEDWA KU SPAIN
NYIMBO zimatikhudza m’njira zambiri. Zingatikhazike mtima m’malo, kutitsitsimula, ndi kutithandiza kukhala osangalala. Nyimbo zingatithandize kusonyeza chimwemwe chathu ndiponso chisoni chathu. Kale komanso masiku ano, palibe mtundu wa anthu umene unakhalapo wopanda nyimbo. Inde, nyimbo ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.—Genesis 4:21.
Takhala tikumva nyimbo mwina kungoyambira tili makanda. N’kutheka kuti tili ana mayi athu ankatiimbira kanyimbo pofuna kuti tigone. Ndipo achinyamata, amakondanso kwambiri nyimbo zimene zimawatenga mtima. Nawonso akuluakulu amakonda kumvetsera nyimbo zotsitsimula akamayendetsa galimoto kapena akakhala kunyumba ataweruka ku ntchito.
Mawu a nyimbo inayake amatha kutchula zinthu zina zokhudza chikhalidwe komanso mbiri ya dziko. Kale Aisiraeli ankaimba nyimbo pokumbukira zochitika zofunika kwambiri. (Eksodo 15:1-21; Oweruza 5:1-31) Mneneri Mose anapeka nyimbo yofotokoza mbiri ya Aisiraeli ndiponso yowapatsa malangizo olimbikitsa kwambiri. (Deuteronomo 32:1-43) N’zosakayikitsa kuti nyimbo zoterezi zinkawathandiza anthuwo kukumbukira zinthu.
Mungathe Kuimba
Mwina mumaganiza kuti, ‘Ine kuimba kunandipita kumanzere.’ Komano taganizirani pang’ono za mawu amene muli nawo. Pafupifupi aliyense angathe kuimba nyimbo pogwiritsa ntchito chida chinachake, ngakhalenso popanda kugwiritsira ntchito chida chilichonse. Pamangofunikira kutsegula pakamwa n’kuyamba kuimba basi. Ngakhale anthu atapanda kukutamani, zilibe kanthu. Ndipo ngati muchita khama mawu anu adzayamba kumveka bwino.
Magazini ina ya ku Spain inati: “Poimba nyimbo, mtima wathu wonse umakhudzidwa, ndipo palibe chinthu chimene chingapose nyimbo pankhani yotithandiza kusonyeza zimene zili mumtima mwathu.” Katswiri wina woimba nyimbo mwaluso, dzina lake Ainhoa Arteta anati: “[Kuimba nyimbo] n’kosangalatsa. Ndibwino kuti aliyense amene akufuna kusonyeza mmene akumvera mumtima mwake, azimasuka kuimba nyimbo panthawi imene wafuna.”—Psychologies.
Chifukwa chakuti nyimbo zimakhudza kwambiri mtima, tiyenera kusankha bwino nyimbo zimene timamvera. Chuni chabwino cha nyimbo chingakometse mawu oipa amene amalimbikitsa udani, chiwerewere kapena chiwawa. Munthu wofuna kusangalatsa Mulungu sangasangalale ndi zinthu zotere. (Aefeso 4:17-19; 5:3, 4) Mawu a Mulungu amati: “Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.” (Miyambo 4:23) Inde, kusankha nyimbo sinkhani yamasewera. *
Nyimbo Zabwino Ndi Mankhwala
Buku lina linati: “Mtundu uliwonse wa anthu uli ndi nyimbo [chifukwa] nyimbo zimathandiza munthu kukhala ndi thanzi labwino.” Mabuku ena amavomerezanso kuti kuimba kumathandiza kuti minyewa izitakasuka bwinobwino ndipo zimenezi zimachepetsa ululu.—Principles and Practice of Stress Management.
N’chifukwa chake madokotala ena amalimbikitsa anthu amene ali ndi nkhawa kuti azimvetsera nyimbo zokhazika mtima pansi. M’zipatala zina amaika nyimbo m’zipinda zofikira matenda akayakaya. Ana obadwa masiku asanakwane, ndiponso anthu ochitidwa opaleshoni sachedwa kupeza bwino akamamvetseranso nyimbo zabwino. Malinga ndi buku lija, ofufuza
apeza kuti kumvetsera nyimbo zokhazika mtima pansi “kumathandiza kuchepetsa nkhawa pamene munthu akuchitidwa opaleshoni.”Nyimbo zimathandizanso kukhazika mtima pansi azimayi panthawi yobereka. Madokotala a mano amaika nyimbo zokhazika mtima pansi pothandiza odwala amantha kuti aupeze mtima. Komatu nyimbo zimatithandiza m’njira zambiri. Zingatithandizenso mwauzimu.
‘Ndidzam’yamika Mulungu ndi Nyimbo Yanga’
Kodi mukudziwa kuti gawo limodzi pamagawo 10 alionse a Baibulo ndi nyimbo? Chitsanzo chabwino ndi mabuku a Salmo, Nyimbo ya Solomo ndi Maliro. N’chifukwa chake pa nyimbo pafupifupi 300 zotchulidwa m’Baibulo, zambiri n’zokhudza kulambira Mulungu. Mfumu Davide, yemwe anali katswiri poimba ndi kupeka nyimbo, anati: “Yehova ndiye mphamvu yanga . . . , ndipo ndidzam’yamika nayo nyimbo yanga.”—Salmo 28:7.
Ndipotu Davide analinganiza amuna 4,000 a fuko la Levi kuti akhale oimba zida komanso mawu ku Yerusalemu. Pa anthu amenewa amuna 288 anali ‘ophunzitsidwa kuimbira Yehova, mwa nthetemya.’ (1 Mbiri 23:4, 5; 25:7) N’zachionekere kuti amuna amenewa ankakonzekera mwakhama ntchito yawo yoimbayi. Nyimbo zinali zofunika kwambiri pa kulambira Yehova. Motero oimbawo ankaletsedwa kugwira ntchito zina zapakachisi kuti azingoika maganizo pantchito yawo basi.—1 Mbiri 9:33.
Usiku womaliza pamoyo wa Yesu, iye ndi ophunzira ake anaimba nyimbo zotamanda Mulungu. Mwina ankaimba Salmo 113 mpaka 118. Panthawiyo nyimbo za m’machaputala amenewa zinkatchedwa Masalimo a Aleluya ndipo zinkaimbidwa pa mwambo wa Pasika. (Mateyo 26:26-30) Zinkatchedwa Masalimo a Aleluya chifukwa chakuti mawu oti Aleluya, amene amatanthauza kuti “Tamandani Ya,” anatchulidwa kwambiri m’nyimbo zimenezi. Mawu akuti “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova, yemwe ndi Mulungu Wam’mwambamwamba.—Salmo 83:18.
Kuimba kunalinso mbali ya kulambira kwa Akhristu. Buku lina linati: “Akhristu oyambirira ankaimba pagulu komanso paokhapaokha. Ayuda ankaimba m’masunagoge awo ndipo akatembenuka n’kukhala Akhristu, ankangopitiriza zomwezo. . . . Kuwonjezera pa Masalimo a Chiheberi . . . , panali nyimbo zatsopano zogwirizana ndi chikhulupiriro chatsopanocho.” Masiku ano Akhristu a Mboni za Yehova amasangalala kutamanda Mulungu poimba nyimbo m’nyumba zawo kapena pamisonkhano yachikhristu.
Monga taonera, nyimbo zimatithandiza kusonyeza mmene tikumvera, zimakhudza kwambiri mtima, maganizo, ndi thupi. N’chifukwa chake tiyenera kulemekeza ‘mtulo . . . wangwiro wochokera kumwamba’ umenewu. (Yakobe 1:17) Choncho, tiyeni tiugwiritse ntchito mokwanira ndiponso mwanzeru.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 9 Anthu amene amakonda Mulungu ndi anthu anzawo samvera nyimbo zolimbikitsa udani, chiwerewere kapena chiwawa. Iwo samvetseranso nyimbo zolimbikitsa ndale kapena kupembedza konyenga.—Yesaya 2:4; 2 Akorinto 6:14-18; 1 Yohane 5:21.