Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chakudya cha ku Thailand

Chakudya cha ku Thailand

Chakudya cha ku Thailand

YOLEMBEDWA KU MALAYSIA

MUKAMAYENDA mu mzinda wa Bangkok ku Thailand, anthu ali pikitipikiti, mumamva kafungo koutsa mudyo. Kafungoka kamachokera m’mbali mwa msewu momwe mumakhala anthu odziwa kuphika zakudya mwaluso. Chifukwa cha kafungo kokomako komanso maonekedwe okopa a chakudyacho, mungakopeke ndi kuima kuti mulaweko chakudya chokomacho.

Chakudya cha ku Thailand n’chokopa chifukwa choti amathiramo tokometsera tambirimbiri, monga timitsitsi, timasamba, ndiponso timbewu tosiyanasiyana. Choncho chakudyacho chimatha kumveka chotsekemera, chowawasa, chamchere, chowawira ngati luni, ndiponso chatsabola. Moti zimakhala zovuta kwambiri kupitiriza ulendo wako popanda kuima pang’ono n’kulawako chakudyacho. Kodi anthu a ku Thailand anayamba bwanji kuphika chakudya chotere?

Anatengera Kaphikidwe ka M’mayiko Osiyanasiyana

Dziko la Thailand lili pa nkhumano pa anthu a m’mayiko a ku Asia. Kwa zaka zambiri, anthu a ku China, ku Lao, ku Cambodia, ku Indonesia ndi ku Ulaya ankadutsadutsa m’dziko la Thailand ndipo ambiri anaganiza zomakhala komweko. Anthu amenewa anabweretsa zakudya zamitundumitundu za kwawoko ndipo zakudya zonsezi zidakalipobe mpaka pano.

Kalekale anthu oyendayenda ochokera ku India anaphunzitsa anthu a ku Thailand kukometsera zakudya zawo pothiramo kale. M’zaka za m’ma 1500, Apwitikizi anabweretsa tsabola ndipo mwinanso tomato. Panopo, zakudya za ku Thailand amathirako zokometsera zosiyanasiyana, koma zambiri amathirako tsabola wofiira, wobiriwira, ndipo amathirakonso kale wa mitundu yosiyanasiyana. Chifukwa chothira tsabola ndiponso kale, zakudya zimenezi zimakoma kuti tsoo, monga zimachitira zakudya zambiri za amwenye.

Zakudya Zokoma Mosiyanasiyana

Ku Thailand, panthawi ya chakudya pamakhala zakudya zosiyanasiyana monga supu, saladi, ndiwo zokazingira, nyama kapena masamba ophika, ndiponso msuzi. Nthawi zonse pambalipa pamakhalanso mpunga woyera. Pamakhalanso tizakudya tina totsekemera totsitsira, tothira shuga ndi mazira. Nthawi zina amathanso kuphika tizakudya totere pogwiritsira ntchito kokonati ndi madzi ake.

Zakudya zimakhala bwino ngati zaphikidwa zisanakhale nthawi yaitali, ndipotu ku Thailand zakudya zotere sizovuta kupeza. M’misika yambiri ya m’mizinda ndi m’matauni mumapezeka zakudya zongobwera kumene, monga zipatso, masamba, nsomba, adyo, jinja ndi chitowe. M’misika ngati imeneyi mumapezekanso tsabola wambirimbiri ndi zinyumwa, ndipotu anthu ambiri ku Thailand amakonda kwambiri zakudya zimenezi.

Kaya mwabwera kudzacheza ku Thailand kapena mukungofuna kulawako zakudya za ku Thailand zopezeka kwanu komweko, musalephere kulawa zakudya zotchedwa tom yam goong. Ameneyu ndi supu watsabola komanso wowawasira pang’ono, yemwe amamuphika pogwiritsa ntchito nkhanu zam’nyanja. Anthu a ku Thailand amam’konda kwambiri supu ameneyu. Zakudya zinanso zimene mungazikonde ndi monga mapapaya othirako zokometsera, zakudya zina zochokera ku nyemba kapena kachewere zomwe amadyera nkhuku kapena bakha wowotcha, nyama ya nkhumba ya mnofu wokhawokha, kapenanso nsomba. Palinso zakudya zina zotchedwa Ma ho, kutanthauza kuti “mahatchi othamanga,” zomwe amaziphika pophatikiza nyama ya nkhumba, mtundu winawake wa nkhanu, ndiponso mtedza. Zonsezi amaziika pamwamba pa chinanazi chosaphika ndipo pofuna kukongoletsa chakudyachi, pamwamba pake amaikapo tsabola wofiira ndi timasamba tinatake. Anthu akamaliza chakudya chokomachi, amakonda kutsitsira ndi kampunga katseketseke kothira madzi a kokonati ndi mango.

Kodi zakudya za ku Thailand amadya bwanji kuti zizikoma? M’madera ena a dzikolo, anthu amadya mpunga ndi manja ndipo amapanga nthongo ngati nsima n’kumasunsa. Koma mwina mungakonde kugwiritsa ntchito timitengo podya zakudya zochokera ku nyemba kapena kachewere zija. Ngati kudya ndi timitengo kukukuvutani ingotengani foloko kapena supuni.

Kodi tsopano mwayamba kulakalaka mutalawako chakudya cha ku Thailand? Inde, kukoma kwa zakudya za ku dziko lokongola la ku Asia limeneli kungakupangitseni kuyamba kukonda zakudya za amwenye.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 23]

1 Supu yotchedwa Tom yam goong

2 Zakudya zopangidwa kuchokera ku nyemba kapena kachewere zophatikiza ndi nyama ya nkhumba komanso nkhanu

3 Mapapaya othiridwa zokometsera

4 Zakudya Zotchedwa Ma ho

5 Kampunga katseketseke kothira madzi a kokonati ndi mango