Kodi Dzikoli Lidzakhalabe ndi Zinthu Zokwanira Anthu Onse?
Kodi Dzikoli Lidzakhalabe ndi Zinthu Zokwanira Anthu Onse?
YOLEMBEDWA KU CANADA
▪ Gulu lina la akatswiri ndiponso akuluakulu oona zachilengedwe linafalitsa zimene linapeza pa kafukufuku amene linachita kwa zaka zinayi, wofuna kuona mmene zachilengedwe zilili m’madera ofunikira kwambiri padziko lonse. Zina mwa zinthu zimene anaona ndi izi: Pazaka 50 zapitazi, zinthu zachilengedwe zachepa kwambiri pa dziko lonse chifukwa mosiyana ndi kale, pakhala anthu ambiri ofunika chakudya, madzi, mitengo, thonje, ndiponso nkhuni kapena mafuta. Zimenezi zachititsa kuti ziyambe kukayikitsa ngati m’tsogolomu dzikoli lidzakhalabe ndi zinthu zokwanira anthu onse. Mbewu sizikuberekanso mokwanira, mpweya sukuyeretsedwa mokwanira chifukwa cha kuchepa kwa mitengo yachilengedwe, komanso nyanja sizikukwanitsa kubwezeretsa chonde m’nthaka. Komanso mitundu yambiri ya zamoyo padzikoli yatsala pang’ono kutheratu yonse.
Nyuzipepala ina ku Canada inati: “Anthu akuwononga kwambiri dziko kuposa kale lonse moti n’zotheka kuti kayendedwe ka zinthu zosiyanasiyana m’chilengedwe kangathe kudzasokonezeka mwadzidzidzi. Zimenezi zingadzayambitse matenda, kuwononga mitengo yambiri ndipo mwinanso zingadzachititse kuti malo ena a m’nyanja asakhalenso ndi zamoyo.” Nyuziyo inapitiriza kunena kuti: “Anthu awononganso kwambiri malo a zithaphwi, nkhalango zosiyanasiyana, nkhumano za mitsinje ndi nyanja, madera a nsomba zambiri a m’mphepete mwa nyanja ndiponso madera ena amene amathandiza kuyeretsa mpweya, madzi ndi zakudya zosiyanasiyana.” (Globe and Mail) Ngakhale kuti akatswiri ofufuza aja anavomereza zoti anthu angathe kuchepetsa mavuto a zachilengedwewa, iwo anati “m’pofunika kuti anthuwo asinthe kwambiri zochita zawo zimene zimakhudza chilengedwe.”
Kodi n’zotheka kuteteza dziko lathuli kuti lisawonongekeretu? Yankho n’lakuti n’zotheka. Ifeyo tili ndi udindo wosamalira chilengedwe cha Mulungu, motero tiziyesetsa kuchisamalira. (Salmo 115:16) Komabe, ndi Mulungu yekha basi amene adzakonze zinthu m’chilengedwe kuti zonse ziziyenda bwino. “Mlengi” wathuyu analonjeza kuti adzasamalira dziko lapansi ndi ‘kulithirira,’ kapena kuti kulipatsa zinthu zonse zofunika. (Yobu 35:10; Salmo 65:9-13) Zina mwa zinthu zimenezi ndi nyanja ndi zinthu zonse zopezeka m’nyanjamo. Yehova Mulungu ali ndi mphamvu zolamulira nyanja poti iye ndi Mlengi. (Salmo 95:5; 104:24-31) Ndipo zimene analonjeza zidzakwaniritsidwa chifukwa Mulungu “sanganame.”—Tito 1:2.
N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti dzikoli lidzakhalabe ndi zinthu zokwanira anthu onse. Zimenezi zimachititsa anthu onse oopa Mulungu kumutamanda chifukwa cha nzeru, mphamvu, ndiponso ubwino wake. Amamutamandanso chifukwa cha mmene amakondera chilengedwe chake.—Salmo 150:1-6.
[Mawu a Chithunzi patsamba 12]
Globe: NASA photo