Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Kuti Kulambira Mulungu Kuzindisangalatsa?

Kodi Ndingatani Kuti Kulambira Mulungu Kuzindisangalatsa?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Kuti Kulambira Mulungu Kuzindisangalatsa?

Mnyamata wina wa zaka 16, dzina lake Joshua, anali gone pabedi. Mayi ake anaima pakhomo n’kumuuza mokalipa kuti: “Joshua, tadzuka apa! Iwe sukudziwa kuti madzulo ano timapita ku misonkhano?” Kwawo kwa Joshua ndi a Mboni za Yehova ndipo amakonda kupita ku misonkhano kukalambira. Koma Joshua anayamba kuchita ulesi.

Monyinyirika, iye anati: “Amayi, sindingajombe lero lokha kodi?”

Mayiwo anati: “Tangosintha zovala apa, kuvuta bwanji iwe? Usandichedwetsenso lero, wamva!” Kenako mayiwo anatembenuka n’kumapita.

Mayiwo asanapite patali, Joshua anayankhula mosaganizira bwino amvekere: “Kodi ndinakuuzani kuti ndimafuna kupita ku tchalitchi kwanuko?” Mayiwo anaima ndipo Joshua anadziwa kuti amva mawu akewo. Komabe iwo anangopitiriza kuyenda, osamuyankha.

Kenako Joshua anayamba kudandaula mu mtima chifukwa cha zimene analankhulazo. Cholinga chake sichinali choti awakhumudwitse mayi ake. Komabe, sanafune kupepesa. M’malo mwake anaganiza njira ina imene anaona kuti ndi yabwino.

Iye anadzuka modzikakamiza n’kuyamba kuvala. Kenako analankhula yekha kuti: “Yembekezani, posachedwapa ndidzayamba kuchita zimene ndikufuna. Ine sindili ngati anthu ena amene amapita ku Nyumba ya Ufumu aja. Chifukwa ine zopempherazi si kwenikweni.”

KODI inuyo munayamba mwamvapo ngati Joshua? Kodi nthawi zina mumaona kuti anthu ena amasangalala ndi zochitika za kumpingo zimene inuyo zimakutopetsani? Mwachitsanzo:

▪ Kodi mukamawerenga Baibulo mumangoona ngati mukuwerenga za kusukulu?

▪ Kodi mumaopa kulalikira nawo khomo ndi khomo?

▪ Kodi nthawi zambiri mukakhala ku misonkhano mumangonyong’onyeka?

Musakhumudwe ngati mumachita zinthu ngati zimenezi. Pali zinthu zochepa zimene muyenera kuchita pofuna kuti kulambira Mulungu kuyambe kukusangalatsani. Tiyeni tione zinthu zimenezi.

Chinthu Choyamba: Kuwerenga Baibulo

Kuvuta kwake. Mwina simukonda kuwerenga ndipo simungathe kukhala nthawi yaitali mukuwerenga n’kumatsatira bwinobwino nkhaniyo. N’kuthekanso kuti muli ndi zowerenga zambiri za kusukulu.

Kufunika kwake. Baibulo ndi buku louziridwa ndi Mulungu komanso ndi lothandiza “pophunzitsa, podzudzula, pakukonza cholakwa ndi pakulangiza za chilungamo.” (2 Timoteyo 3:16, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Kuwerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha zimene mukuwerengazo kungakuthandizeni kumvetsa zinthu zimene kale simunkazimvetsa ngakhale pang’ono. Monga mukudziwira, palibe chabwino chimene chimapezeka popanda khama. Mwachitsanzo, ngati mukufuna kuti muzichita bwino pa masewera enaake, mumafunika kudziwa bwino malamulo ake onse n’kumachita masewerawo pafupipafupi. Ngati mukufuna kukhala ndi thanzi labwino, mumafunika kuchita masewera olimbitsa thupi. Motero, ngati mukufuna kum’dziwa bwino Mlengi wanu, m’pofunikanso kuti muziwerenga Mawu a Mulungu.

Zimene achinyamata anzanu anenapo. “Nditapita ku sekondale panali zinthu zingapo zofunika kuti ndiziganizire bwino. Ana asukulu anzanga ankachita zinthu zambiri zoipa, ndipo ineyo ndinkadzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi n’zimene inenso ndikufuna? Kodi zimene makolo anga akundiphunzitsa n’zoonadi?’ Ndinayenera kupeza ndekha mayankho a mafunso amene ndinkadzifunsawa.”—Anatero Tshedza.

“Sindinkakayika ngakhale pang’ono kuti makolo anga ankandiphunzitsa zoonadi, komabe ndinafunika kutsimikizira pandekha mumtima mwanga. Ndinafunika kuyamba kumva kuti ineyo pandekha ndiyenera kulambira Mulungu osati kungotsatira makolo anga ayi.”—Anatero Nelisa.

Zimene mungachite. Konzani ndandanda yanuyanu yowerengera. Sankhani nokha zimene mukufuna kuwerenga. Komano kodi mungayambire pati? Mungathe kuyamba ndi kusanthula bwinobwino Baibulo ndiponso zimene mumakhulupirira, pogwiritsira ntchito mabuku ofotokoza Baibulo, monga buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? *

Zoti muchite. Monga poyambira, pamunsipa chongani mitu iwiri kapena itatu ya nkhani za m’Baibulo zimene mukufuna kuzidziwa bwino, komanso ngati mukufuna, mungathe kulembapo mitu yanuyanu.

□ Kodi Mulungu alikodi?

□ Kodi ndingatsimikize bwanji kuti olemba Baibulo anauziridwa ndi Mulungu?

□ Kodi n’chifukwa chiyani ndiyenera kukhulupirira kuti Mulungu ndi amene analenga zinthu zonse osati kuti zinangokhalako zokha?

□ Kodi Ufumu wa Mulungu n’chiyani, ndipo ndingatsimikizire bwanji kuti ulipodi?

□ Kodi zimene ndimakhulupirira pankhani ya imfa ndingazifotokoze bwanji kwa ena?

□ N’chifukwa chiyani ndiyenera kukhulupirira kuti akufa adzaukadi?

□ Kodi chipembedzo choona ndingachidziwe bwanji?

□ ․․․․․

Chinthu Chachiwiri: Kulowa Muutumiki

Kuvuta kwake. Zimachititsa mantha kuuza ena za Baibulo kapena kukumana ndi mnzanu wakusukulu pamene mukulalikira.

Kufunika kwake. Yesu analangiza anthu om’tsatira kuti: “Mukapange ophunzira . . . , [ndi] kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyo 28:19, 20) Koma pali zifukwa zinanso zimene tiyenera kulakira ena. Ofufuza anapeza kuti m’madera ena achinyamata ambiri amakhulupirira Mulungu komanso Baibulo. Koma ngakhale kuti amatero, achinyamatawa alibe chiyembekezo chenicheni cha m’tsogolo. Chifukwa chophunzira Baibulo, inu mukudziwa zinthu zimene anzanu ambiri akuzilakalaka ndiponso akufunikira.

Zimene achinyamata anzanu anenapo. “Ine ndi mnzanga tinakonzekera mawu abwino oyambira ulaliki, ndipo tinaphunzira njira zabwino zoyankhira anthu amene akukana kumva uthenga wathu komanso tinaphunzira mmene tingachitire tikabwerera kwa anthu amene tinawalalikira kale. Nditayamba kulimbikira kwambiri utumiki, ndiyamba kuukondanso kwambiri.”—Anatero Nelisa.

“Mlongo wina anandithandiza kwambiri. Iyeyu ndi wamkulu kwa ine ndi zaka 6, ndipo timapitira limodzi muutumiki komanso nthawi zina timakadyera limodzi chakudya cham’mawa kwinakwake. Anandisonyeza malemba olimbikitsa amene anandithandiza kwambiri. Chifukwa cha chitsanzo chake chabwino, panopo ndimakonda kwambiri kuthandiza anthu ena. Sindikudziwa kuti ndingam’thokoze bwanji.”—Anatero Shontay.

Zimene mungachite. Ngati makolo anu angakuloleni, pezani munthu wina wachikulirepo mumpingo mwanu woti muzilowa naye muutumiki. (Machitidwe 16:1-3) Baibulo limati: “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.” (Miyambo 27:17) Kugwirizana ndi anthu achikulire kungakupindulitseni m’njira zambiri chifukwa iwowo aona zinthu zambiri pamoyo. Alexis, yemwe ali ndi zaka 19, anati: “Kwenikweni munthu umakhala womasuka kwambiri ukamayenda ndi achikulire.”

Zoti muchite. Lembani pansipa dzina la munthu winawake wachikulire mumpingo mwanu amene angakuthandizeni mu utumiki, kuwonjezera pa makolo anu.

․․․․․

Chinthu Chachitatu: Kupita ku Misonkhano

Kuvuta kwake. Mukabwera ku sukulu madzulo mumakhala wotopa moti simungafune kuti mukakhalenso pansi kwa ola limodzi kapena awiri n’kumamvetsera nkhani za Mawu a Mulungu.

Kufunika kwake. Baibulo limalimbikitsa Akhristu motere: “Tiyeni tiganizirane wina ndi mnzake, kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga chilili chizolowezi kwa ena, koma tilimbikitsane wina ndi mnzake. Tiwonjezeredi kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.”—Aheberi 10:24, 25.

Zimene achinyamata anzanu anenapo. “Kukonzekera misonkhano si nkhani ya makonda ayi. Nthawi zina umafunika kuchita kudzikakamiza. Munthu ukapita ku msonkhano utakonzekera umasangalala chifukwa umadziwa zimene zikunenedwazo, ndipo ungathenso kulankhulapo.”—Anatero Elda.

“Panthawi ina, ndinayamba kuona kuti misonkhano imene ndinkayankhapo inayamba kundisangalatsa kwambiri.”—Anatero Jessica.

Zimene mungachite. Pezani nthawi yokonzekera misonkhano, ndipo ngati mungathe muzikayankhapo. Mukamatero, mumayamba kuona kuti nanunso zikukukhudzani zimene zikuchitika pamsonkhanopo.

Mwachitsanzo: Kodi n’chiyani chimakusangalatsani kwambiri pakati pa kuonerera masewera enaake pa TV kapena kuchita nawo masewerawo? N’zosachita kufunsa kuti kuchita nawo zinthu kumasangalatsa kwambiri kuposa kumangoonerera. Chonchotu mungachite bwino kuyamba kuona misonkhano m’njira yomweyi.

Zoti muchite. Pansipa lembani nthawi imene mungamapeze mphindi 30 pa mlungu zokonzekera msonkhano winawake.

․․․․․

Achinyamata ambiri akuona kuti mawu a pa Salmo 34:8 ndi oona. Mawuwa amati: “Talawani, ndipo onani kuti Yehova ndiye wabwino.” Kodi mumamva kukoma kwa chakudya chinachake, munthu akamakulongosolerani za kukoma kwa chakudyacho kapena mumamva kukoma mukamadya chakudyacho? N’chimodzimodzi ndi kulambira Mulungu. Lawani nokha zinthu zauzimu kuti muone ubwino wake. Baibulo limati munthu amene amachitadi zinthu, osati kungozimva chabe, ‘amakhala wosangalala pozichita.’—Yakobe 1:25.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.dan124.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 19 Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ N’chiyani chingachititse kuti wachinyamata asamasangalale ndi zinthu zauzimu?

▪ Pazinthu zitatu zokhudza kulambira zimene zatchulidwa m’nkhani ino, kodi n’chiti chimene mukufuna kulimbikira kwambiri, ndipo muchikwanitsa bwanji?

[Chithunzi pamasamba 20, 21]

Ngati mukufuna kulimbitsa thupi, muyenera kuchita masewera olimbitsa thupi. Ngati mukufuna kulimba mwauzimu, muyenera kuphunzira Mawu a Mulungu