Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

M’kamwa

M’kamwa

M’kamwa

Munapangidwadi Mwaluso

▪ Mukangoponya m’kamwa chakudya chimene mumachikonda kwambiri, nthawi yomweyo mumayamba kumva kukoma kwake. Koma kodi chimachitika n’chiyani kuti munthu azimva kukoma akamadya chakudya?

Taganizirani izi: M’kamwa mwanu mumakhala maselo othandiza kumva kukoma kwa chakudya. Ena amakhala kukhosi koma ambiri ali pa lilime ndipo amatithandiza kuti tizitha kumva kuwawasa, kukoma mchere, kutsekemera kapena kuwawa kwa chakudya. * Pali maselo ena osiyana ndi amenewa omwe amatithandiza kudziwa kuti m’chakudya athiramo tsabola kapena adyo. Tingoti chakudya chamtundu uliwonse chikafika m’kamwa, maselo othandiza kumva kukoma kwa chakudyacho amatumiza uthenga ku ubongo ndipo timamva kukoma kwake.

Koma pali zinthu zinanso zimene zimathandiza kuti munthu amve kukoma kwa chakudya. Mphuno ili ndi minyewa 5 miliyoni yothandiza kumva fungo. Minyewa imeneyi imathandiza kuti tizimva fungo la zinthu pafupifupi 10,000 ndipo imathandizanso kuti tizitha kumva kakomedwe ka zinthu zosiyanasiyana. Ofufuza apeza kuti nthawi zambiri fungo la chakudya ndi limene limachititsa kuti chakudyacho tizichimva kukoma.

Asayansi ena apanga chipangizo chomwe chimagwiritsa ntchito gasi ponunkhiza fungo la zinthu zosiyanasiyana. Koma katswiri wina wa za minyewa, dzina lake John Kauer, ananena kuti: “Chipangizo chilichonse chochita kupanga sichingafanane ngakhale pang’ono ndi chinthu chochita kulengedwa.”—Research/Penn State.

Tonse timakonda chakudya chifukwa cha kukoma kwake. Koma asayansi sanatulukirebe chimene chimachititsa kuti anthu azikonda kwambiri chakudya china kuposa chinzake. Nyuzipepala ina inati: “Anthu asayansi amadziwa zinthu zosiyanasiyana zimene zimachitika m’thupi la munthu koma sanafikebe pomvetsa bwinobwino zimene zimachitika kuti tizitha kumva fungo ndi kakomedwe ka zinthu.”—Science Daily.

Ndiyeno kodi inuyo mukuganiza bwanji? Kodi simukutha kuona kuti m’kamwa mwathu mumatsimikizira kuti tinapangidwa mwaluso?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Posachedwapa asayansi atulukira kuti palinso mtundu wina wa mchere wotchedwa umami, womwe umapezeka m’mbewu zosiyanasiyana komanso m’nyama. Ndipo akuti umapezekanso m’zinthu zina zokometsera chakudya.

[Chithunzi patsamba 26]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Mkati mwa lilime

[Chithunzi]

Pamwamba pa lilime

[Mawu a Chithunzi]

© Dr. . John D. Cunningham/Visuals Unlimited