Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupewa Zamizimu?

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupewa Zamizimu?

Zimene Baibulo Limanena

N’chifukwa Chiyani Muyenera Kupewa Zamizimu?

M’DZIKO lina ku Asia, gulu la anthu linali kuchita mwambo wolemekeza mizimu. Mwambowu unafika pachimake azimayi awiri atasankhidwa n’kugwidwa mizimu. Iwo anatong’ola maso awo, ndipo anayamba kunjenjemera kwadzaoneni.

Ku Puerto Rico, munthu wina wa zamatsenga anachititsa mwambo kuti alankhule ndi Changó, yemwe amati ndi mulungu wa mabingu. Pamwambowo, wamatsengayo amafotokoza zinthu zimene akuona m’masomphenya, ndipo anthu onse amene ali pamenepo amayamba kunjenjemera chifukwa chogwidwa mizimu.

M’mayiko ambiri anthu amachita zamatsenga. Kukhulupirira mizimu kwayamba kutchuka kwambiri, ndipo anthu ambiri akukopeka nako. Kuposa kale lonse, panopa pali mabuku, masewera, mapulogalamu a pa TV, ndiponso mafilimu ambiri osonyeza zamizimu.

Komano Baibulo limaphunzitsa kuti kuchita chinthu chilichonse chokhudzana ndi zamatsenga n’kukhulupirira mizimu. Nkhani yokhulupirira mizimu musaitenge mopepuka, n’kumaganiza kuti kuchita zimenezi kumangothandiza munthu kudziwa zinthu zobisika. Kwenikweni mumakhala mukuchita zinthu ndi ziwanda, kapena kuti angelo oipa amene anapandukira Mulungu.—Chivumbulutso 12:9, 12.

Dziwani kuti kukhulupirira mizimu ndi nyambo imene ziwanda zimakopera anthu. Msodzi amagwiritsa ntchito nyambo zosiyanasiyana pofuna kugwira nsomba za mitundu yosiyanasiyana. Nazonso ziwanda zimagwiritsa ntchito mitundu yosiyanasiyana ya kukhulupirira mizimu kuti zikole anthu osiyanasiyana. Mtsogoleri wa ziwanda amatchedwa “mulungu wa dongosolo [loipa] lino la zinthu.” Iyeyu ndi katswiri pochititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira, moti anthuwa satha kuzindikira choonadi cha m’Baibulo ndiponso cholinga cha Mulungu.—2 Akorinto 4:4.

Kuopsa Kokhulupirira Mizimu

Mwachidule, cholinga cha mizimu yoipa n’chakuti itisokoneze kuti tisakhale paubwenzi ndi Mlengi wathu. Imachititsa kuti anthu asamvere malamulo olungama a Mulungu, kaya modziwa kapena mosadziwa. Motero, Mulungu amasiya kum’konda munthu amene amakhulupirira mizimu, moti amakhala wopanda chiyembekezo chilichonse ndipo mapeto ake adzawonongedwa.—Chivumbulutso 21:8.

Luis, yemwe ndi wa ku Puerto Rico, anati: “Kuyambira ndili wamng’ono, banja lathu linkakhulupirira mizimu. Tingati chipembedzo chathu chinali chimenechi ndipo ndi mmene moyo wathu unalili basi. Ineyo ndinkatha kulotera zam’tsogolo ndipo ndinkaganiza kuti luso limeneli ndinangobadwa nalo basi. Nthawi zambiri ndinkatha kuwinitsa anthu mipikisano polota manambala owinira. Luso limeneli kwenikweni inali nyambo yondikolera kuti ndilephere kudziwa Baibulo n’kukhala paubwenzi ndi Mulungu.”—Yohane 17:3.

Anthu ambiri amaona kuti palibe vuto ndi kukhulupirira mizimu, ndiponso kuti mwina n’kopindulitsa. Iwo amati pali mizimu ina yabwino ndipo ena amati kukhulupirira mizimu kumawathandiza kudziwa zinthu zinazake, kulemera, kapena kukhala osangalala. Komatu limeneli ndi bodza lamkunkhuniza. Luis anati: “N’zosatheka kuchita zimenezi popanda kulowa nazo m’mavuto.”

Mnyamata wina, dzina lake Chad, anayamba kuona zinthu zoopsa ndipo anavutika kwambiri chifukwa nthawi iliyonse akati agone ankadzidzimuka. Iye anati: “Ziwanda zinayamba kundivutitsa ndi kundizunza usiku uliwonse.” Kodi tingatani kuti titetezedwe ku zoterezi?

Kodi Tingatetezedwe Bwanji?

Kuti tikhale otetezeka tiyenera kupewa chilichonse chokhudzana ndi zamizimu. (Agalatiya 5:19-21) N’chifukwa chake Yehova Mulungu amachenjeza atumiki ake kuti: “Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”—Deuteronomo 18:10-12.

Potsatira mawu amenewa, anthu ambiri ataya mabuku kapena zinthu zina zokhudzana ndi kukhulupirira mizimu n’cholinga chodziteteza. Mmodzi wa iwo ndi Ken, ndipo anati: “Ndinasanthula katundu wanga yense n’kuchotsamo chilichonse chimene ndinali kuchikayikira.”—Onani Machitidwe 19:19, 20.

Njira yaikulu kwambiri yodzitetezera ku mizimu ndiyo kukhala paubwenzi wabwino ndi Yehova, Mulungu woona. Taonani mfundo imene yalembedwa pa Yakobe 4:7, 8: “Gonjerani Mulungu; koma tsutsani Mdyerekezi, ndipo adzakuthawani. Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani. Yeretsani manja anu ochimwa inu, ndipo yeretsani mitima yanu, okayikakayika inu.”

Yehova Mulungu amaphunzitsa ndi kuteteza anthu amene akuyandikira kwa iye. Iwo ‘amadziwa machenjera a Satana,’ ndipo sanyengeka ndi zinthu zabodza. (2 Akorinto 2:11; 11:14) Chinanso n’chakuti Yehova ndi Wamphamvuyonse. Tikapemphera kwa Yehova mwachikhulupiriro, iye amatithandiza kuti mizimu yoipa isamativutitse. Chad, amene tamutchula kale uja, anati: “Chifukwa choti ndinkadziwa kuti ziwanda n’zimene zikundivutitsa, ndinapemphera kuti Yehova Mulungu anditeteze. Nditatero zinasiya kundivutitsa.”—Salmo 91:1, 2.

N’zoonekeratu kuti anthu a mtima wolungama ayenera kusangalala kuti Mulungu akuwateteza panopo ndiponso kuzindikira kuti posachedwapa ziwanda ndiponso anthu onse amene amanyengeka nazo adzawonongedwa. Tangoganizirani chimwemwe ndiponso mtendere umene anthu adzakhale nawo padziko pano, mizimu yoipa ikadzachotsedwa.—Yesaya 11:9; Chivumbulutso 22:15.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi Akhristu ayenera kupewa kuchita zinthu zotani zokhudzana ndi mizimu?—Deuteronomo 18:10-12; Chivumbulutso 21:8.

▪ Kodi ndani amalimbikitsa kukhulupirira mizimu?—2 Akorinto 2:11; 11:14; Chivumbulutso 12:9, 12.

▪ Kodi tingadziteteze bwanji ku mizimu yoipa?—Yakobe 4:7, 8.

[Chithunzi patsamba 10]

Dziwani kuti kukhulupirira mizimu ndi nyambo imene ziwanda zimakopera anthu