Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ “Madzi oundana ku nyanja ya Arctic asungunuka kwambiri m’chaka cha 2007 ndipo izi zatidabwitsa kwambiri. N’zosiyana kwambiri ndi malipoti a zaka zonse.”—MARK SERREZE, NATIONAL SNOW AND ICE DATA CENTER, U.S.A.
▪ Akatswiri pa nkhani ya zamalonda apeza kuti ngati munthu aliyense atamagwiritsa ntchito zinthu za padzikoli ngati mmene amachitira anthu a ku United States, pakanafunika mapulaneti oposa asanu aakulu ngati dzikoli kuti aziwachirikiza. Anthu a ku France ndi ku Britain angafune mapulaneti oposa atatu, a ku Spain angafune atatu, a ku Germany angafune awiri ndi theka ndipo a ku Japan angafune oposa awiri.”—REUTERS NEWS SERVICE, BRITAIN.
“Amangoyambitsa Mavuto Ena”?
“Magazi amene anasungidwa n’kuthiridwa m’thupi la munthu amangoyambitsa mavuto ena,” linatero lipoti la pa yunivesite ina ku Durham, m’boma la North Carolina m’dziko la United States. Ofufuza apeza kuti anthu akaikidwa magazi amene anasungidwa, amadwala matenda a mtima, kufa ziwalo kapenanso kumwalira kumene. N’chifukwa chiyani zimatero? Makemikolo a m’magazi amene amachititsa kuti mitsempha izikhala ndi mpata wabwino woti magazi azidutsa amawonongeka magaziwo akangotuluka m’thupi la munthu. Zikatero mpweya wabwino suyenda mokwanira m’magazi. Lipotilo linapitiriza kuti: “Odwala ambiri amalandira magazi oti sangathe kuyendetsa bwino mpweya wofunika m’thupi la munthu.”—Duke University Medical Center.
Anthu a ku Bhutan Sasiyana ndi TV
Lipoti lina la ku Bhutan linanena kuti kwa zaka zambiri anthu a ku Bhutan, womwe ndi ufumu waung’ono wa ku Himalaya, sankaloledwa kukhala ndi TV. Koma anthu ambiri atadandaula kuti sanathe kuonera mpikisano wa mpira wa miyendo wapadziko lonse mu 1998, boma linavomereza zoti anthu azikhala ndi TV m’chaka cha 1999. Panopa anthu amaonera masiteshoni 40 a TV ndipo amakonda kwambiri mafilimu opangidwa ku America komanso masewero a pa TV a ku India. Panopa mabanja amene kale ankakhala malo amodzi n’kumaimba ndiponso kucheza amangokhalira kuonera TV basi. Nyuzipepala ina inagwira mawu a mkazi wina amene anadandaula kuti sapeza nthawi yochita zinthu zina zilizonse ngakhale kupemphera. Iye anati: “Ngakhale pochita mwambo wanga wopemphera ndimangoganiza za TV basi.” Nyuziyo inapitiriza kuti: “Koma chodetsa nkhawa kwambiri ndi chakuti anthu ambiri akhoza kuyamba kugula zinthu zosafunika kwenikweni zochokera m’mayiko ena. Otsatsa malonda pa TV akhoza kuchititsa kuti munthu azifuna kugula zinthu zimene sangakwanitse.”—The Peninsula.
Anthu Akulephera Kuika Maganizo Pantchito
Nyuzipepala ina inati: “Nthawi zina anthu ogwira ntchito mu ofesi amangokhalira kuyankha mafoni ndiponso kusokonezedwa ndi anthu ena.” Ofufuza anapeza kuti anthu ena ogwira ntchito mu ofesi amalephera kugwira ntchito kwa mphindi zitatu popanda kusokonezedwa. Popeza kuti tsiku lililonse maola awiri angathe kuwonongeka chifukwa cha zinthu zosokoneza, anthu ena ogwira ntchito m’maofesi amagwiritsa ntchito pulogalamu ya pakompyuta kuti iziwathandiza kusiyanitsa zinthu zofunika ndi zosafunika mwamsanga. Koma mfundo zimene zingathandize aliyense ndi zakuti: “Tiziwauza anthu zoona, . . . kuti tilibiretu ngakhale mphindi imodzi yoti tilankhulane nawo. Apo ayi tifunika kulimba mtima kuti tisamayankhe ma Imelo ndi mauthenga ena ndiponso tizizimitsa mafoni mpaka pamene mwamaliza ntchitoyo.”—New Scientist.