Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
Fotokozani Fanizoli
1. M’fanizo lopezeka pa Luka 18:9-14, kodi Mfarisiyo anali munthu wotani?
(Chongani yankho kapena mayankho olondola m’mabokosiwa.)
□ Wodzichepetsa □ Wolapa □ Wodzikweza
2. Kodi wokhometsa msonkhoyo anali munthu wotani?
(Chongani yankho kapena mayankho olondola m’mabokosiwa.)
□ Wodzichepetsa □ Wolapa □ Wodzikweza
3. Kodi ndani pa awiriwa amene anali wolungama kwambiri?
․․․․․
KAMBIRANANI:
Kodi mufunika kupewa kunena kapena kuchita chiyani kuti musafanane ndi Mfarisi uja? Kodi mungatsanzire bwanji wokhometsa msonkho uja?
Kuchokera M’magazini Ino
Yankhani mafunsowa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.
MASAMBA 8 ndi 9 Kodi tsogolo la dzikoli lili m’manja mwa ndani? Yesaya 11: ․․․
TSAMBA 20 Kodi Mulungu amaona bwanji kulambira mafano? Eksodo 20: ․․․
TSAMBA 21 Kodi mtumwi Yohane anachenjeza kuti tifunika kupewa chiyani? 1 Yohane 5: ․․․
TSAMBA 27 Kodi nthawi zina ngakhale munthu wamakhalidwe abwino kwambiri angakhale ndi chiyani? 1 Yohane 2: ․․․
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?
Kuti mupeze yankho, onani pa zokuthandizani. Onaninso malembawo. Kenaka lembani mayina olondola pa mizereyi.
4. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Ndinkatha kunena miyambi zikwi zitatu, ndipo nyimbo zanga “zinali chikwi chimodzi mphambu zisanu.”
Werengani 1 Mafumu 4:30-32.
5. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Ndinali mfumu yomaliza ya ufumu wogwirizana wa Isiraeli.
Werengani 1 Mafumu 12:1-3, 16-20.
6. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Gulu langa la asilikali linagonjetsa gulu lalikulu la asilikali a Yerobiamu chifukwa ‘tinatama Yehova.’
Werengani 2 Mbiri 13:13-20.
▪ Mayankho ali pa tsamba 19
MAYANKHO A MAFUNSO A PA TSAMBA 31
1. Wodzikweza.
2. Wodzichepetsa ndi wolapa.
3. Wokhometsa msonkho.
4. Solomo.—Mateyo 1:6.
5. Rehabiamu.—Mateyo 1:7.
6. Abiya.—Mateyo 1:7.