Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndingatani Ndi Vuto la Kupanikizika Kusukulu?

Kodi Ndingatani Ndi Vuto la Kupanikizika Kusukulu?

Zimene Achinyamata Amadzifunsa

Kodi Ndingatani Ndi Vuto la Kupanikizika Kusukulu?

“Kusukulu kupanikizika sikutha ngakhale pamene ukukula. Zifukwa zake zimangosintha.”—James, New Zealand. *

“Ndinkapanikizika kwambiri kusukulu, moti nthawi zina ndinkafuna kulira kapena kuthawa.”—Sharon, United States.

KODI mumaona kuti makolo anu samvetsa kuti mumapanikizika kusukulu? N’zoona kuti angakuuzeni kuti palibe chifukwa chodandaulira popeza mulibe ngongole yoti mubweze, banja loti mudyetse, kapenanso bwana woti mum’sangalatse. Koma n’kutheka kuti mumaona kuti kusukulu ndinu wopanikizika ngati makolo anu, mwinanso kuwaposa.

Kupita ndi kubwera kusukulu kungakhale kopanikiza. Tara, yemwe amakhala ku United States, akuti: “Nthawi zambiri, ndewu inkabadwa m’basi ya sukulu. Zikatero, woyendetsa basiyo ankaima ndipo aliyense ankatsika. Tonse tinkachedwa ndi mphindi 30 kapena kuposa pamenepa.”

Kodi ukafika ku sukulu, kupanikizikako kumatha? Ayi. Mwina mwakumanapo ndi zimene zanenedwa m’munsimu.

Kupanikizika chifukwa cha aphunzitsi.

“Aphunzitsi amafuna kuti ndizichita bwino m’kalasi kuposa wina aliyense, ndipo ndimapanikizika pofuna kuwasangalatsa.”—Sandra, Fiji.

“Aphunzitsi amauza ana a sukulu kuti azilimbikira kuti adzakhoze bwino, makamaka ngati anawo ali ndi luso linalake. Aphunzitsiwo amatipanikiza kuti tikhale opambana.”—April, United States.

“Ngakhale utakhala ndi zolinga zabwino pamoyo wako, aphunzitsi ena amakuona ngati ndiwe wachabechabe ngati zolinga zako pamaphunziro n’zosiyana ndi zimene iwo akuganiza.”—Naomi, United States.

Kodi mumamva bwanji aphunzitsi akamakupanikizani?

․․․․․

▪ Kupanikizika chifukwa cha anzanu.

“Kusekondale, ana a sukulu amakhala ndi ufulu ndipo amakhala opulupudza kwambiri. Ngati suchita nawo zimene amachita, amakuona ngati wotsalira.”—Kevin, United States.

“Tsiku ndi tsiku, ndimalimbana ndi vuto lofuna kumwa nawo mowa kapena kuchita chiwerewere. Nthawi zina zimakhala zovuta kukana.”—Aaron, New Zealand.

“Panopa ndili ndi zaka 12, ndipo vuto lalikulu lomwe ndikukumana nalo ndi lakuti anzanga amandikakamiza kuyamba chibwenzi. Aliyense kusukulu amandifunsa kuti, ‘Kodi udzakhala wopanda chibwenzi mpaka liti?’”—Alexandria, United States.

“Anzanga ankandikakamiza kuyamba chibwenzi. Nditakana, anayamba kundinena kuti ndimangofuna kugonana ndi atsikana anzanga. Komatu panthawiyi n’kuti ndili ndi zaka 10 zokha.”—Christa, Australia.

Kodi mumamva bwanji anzanu akamakupanikizani?

․․․․․

Kupanikizika poganizira mmene anzanu akusukulu angaonere chipembedzo chanu.

“Zimavuta kwambiri kuuza anzako akusukulu za chipembedzo chako chifukwa sudziwa kuti azikuona bwanji. Umada nkhawa kuti iwo azikudabwa.”—Carol, Hawaii.

“Kupulayimale ndi kusekondale, ana amagwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo, amachita chiwerewere ndiponso kumwa mowa. Zimakhala zopanikiza kwambiri popeza sufuna kuti anzako azikuseka ukamachita zinthu mosiyana nawo chifukwa chotsatira mfundo za m’Baibulo.”—Susan, United States.

Kodi mumamva bwanji mukaganiza mmene ena angaonere chipembedzo chanu?

․․․․․

Zinthu zina zimene zingachititse kupanikizika. Chongani chimene chimakupanikizani kwambiri, kapena lembani chimene pansipa palibe.

□ Mayeso

□ Homuweki

□ Makolo akamafuna kuti muzichita bwino kwambiri

□ Mukamafuna kuti muzichita bwino kwambiri

□ Anthu andewu kapena ofuna kukuchotserani ulemu

□ Zina ․․․․․

Zinthu Zisanu Zochepetsera Kupanikizika

Kunena zoona, sizingatheke kumaliza sukulu popanda zopanikiza. Komabe, kupanikizika kwambiri kumasautsa. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Nsautso iyalutsa wanzeru.” (Mlaliki 7:7) Koma inu musalole kuyaluka chifukwa chopanikizika. Chinsinsi chake ndi kudziwa mochitira mukapanikizika.

Kulimbana ndi vuto la kupanikizika kuli ngati kunyamula zitsulo. Kuti munthu wonyamula zitsulo zimuyendere bwino, amafunika kukonzekera bwino. Amasamala ponyamula zitsulozo ndipo sayamba ndi kunyamula zolemera kwambiri nthawi imodzi. Choncho, amakhala wadzitho ndithu popanda kuvulala. Koma ngati satsatira zimenezi, amadzipweteka mwina mpaka kuthyoka kumene.

Mofanana ndi zimenezi, mungalimbane ndi vuto la kupanikizika n’kukwanitsa ntchito imene mukufuna kuchita popanda kudzipweteka. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Mwa kuchita zotsatirazi:

1. Dziwani zimene zimayambitsa kupanikizika. Mwambi wina umati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala.” (Miyambo 22:3) Koma n’zosatheka kubisala kuti mupewe vuto losautsa la kupanikizika musanadziwe choyambitsa vutolo. Choncho, onaninso zimene mwalemba zija. Kodi ndi chiyani chimene chimachititsa kuti mupanikizike kwambiri?

2. Fufuzani m’mabuku. Mwachitsanzo, ngati mukupanikizika kwambiri chifukwa cha homuweki, fufuzani zimene mungachite m’nkhani yakuti, “Achinyamata Akufunsa Kuti—Kodi Nthawi Yochita Homuweki Ndingaipeze Kuti?” mu Galamukani! ya February 8, 2004. Ngati mnzanu kusukulu akukukakamizani kuti mugone naye, mungapeze mfundo zothandiza m’nkhani yakuti, “Zimene Achinyamata Amadzifunsa—Bwanji Ngati Wina Atandipempha Kuti Tikagonane?” mu Galamukani! ya March 2007.

3. Dziwiranitu mmene mungayankhire. Ngati mukupanikizika poganizira mmene anzanu akusukulu angakuonereni atadziwa chipembedzo chanu, musadikire kuti mpaka wina achite kudzakufunsani, musanaganize zokanena kapena zokachita. (Miyambo 29:25) Kelsey, wazaka 18, akuti: “Chomwe chinandithandiza ndicho kudziwiratu zochita. Ndinadziwiratu mmene ndingakafotokozere zimene ndimakhulupirira.” Aaron, mnyamata wazaka 18 wa ku Belgium, anachita chimodzimodzi. Iye akuti: “Ndinaganiza za mafunso amene ndingafunsidwe, n’kukonzekera mayankho ake. Ndikanapanda kutero, sindikanatha kufotokoza zimene ndimakhulupirira.”

4. Musazengereze. Mavuto mukamawanyalanyaza satha. M’malo mwake, amangokulirakulira mpaka kukupanikizani kwambiri. Mwachitsanzo, ngati ndinu wa Mboni za Yehova, zingakutetezeni kuwauza ena zimenezo mofulumira. Marchet, yemwe panopa ali ndi zaka 20, akuti: “Chaka chilichonse tikangotsegulira sukulu, ndinkayambitsa nkhani imene ndinkadziwa kuti indipatsa mpata wofotokoza mfundo za m’Baibulo zimene ndimatsatira. Ndinaona kuti ndikachedwa kwambiri kunena kuti ndine wa Mboni, m’pamenenso zinkandivuta kwambiri. Kufotokoza mfundo zimene ndimatsatira kunkandithandiza kwambiri chaka chonse.”

5. Pemphani ena kuti akuthandizeni. Ngakhale munthu wonyamula zitsulo wamphamvu kwambiri amakhala ndi malire ake. Inunso muli ndi malire. Koma simufunika kunyamula nokha mtolowo. (Agalatiya 6:2) Lankhulani ndi makolo anu kapena Akhristu anzanu okhwima mwauzimu. Asonyezeni mayankho amene mwalemba m’nkhani ino. Kambiranani mmene angakuthandizireni kulimbana ndi ena mwa mavutowo. Liz, wa ku Ireland, anafotokozera bambo ake kuti ankaopa kusekedwa chifukwa cha chipembedzo chake. Iye akuti: “Tsiku lililonse, bambo ankapemphera nane asanakandisiye kusukulu. Chifukwa cha zimenezi, mtima wanga unkakhala m’malo.”

Kodi Kupanikizika Kwina N’kwabwino?

Mwina simungakhulupirire, koma zoona zake n’zakuti kupanikizika kwina n’kwabwino. N’chifukwa chiyani tikutero? Tikutero chifukwa chakuti kupanikizika kwanu kungakhale umboni wakuti ndinu wakhama ndipo chikumbumtima chanu chikugwira ntchito. Onani mmene Baibulo limafotokozera munthu wooneka kuti sapanikizika ngakhale pang’ono. Limati: “Udzagona mpaka liti, wolesi iwe? Udzauka ku tulo tako liti? Tulo tapang’ono, kuwodzera pang’ono, kungomanga manja pang’ono, ndi kugona; ndipo umphawi wako udzafika ngati mbala.”—Miyambo 6:9-11.

Heidi, wazaka 16, akufotokoza bwino mfundo imeneyi. Iye akuti: “Kusukulu kumaoneka ngati si malo abwino, koma mavuto amene mumakumana nawo kumeneko ndi omwewonso mudzakumane nawo mukadzayamba ntchito.” Kunena zoona, n’zovuta kulimbana ndi kupanikizika, koma ngati mudziwa mochitira sikungakusowetseni mtendere. Ndipotu kungakuthandizeni kukhala munthu wolimba.

Nkhani zina zakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa,“ mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.dan124.com.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Mayina ena m’nkhani ino asinthidwa.

ZOTI MUGANIZIRE

▪ Kodi ndi zinthu zotani zimene zingasonyeze kuti mwapanikizika?

▪ N’chifukwa chiyani kufuna kuchita zinthu mosalakwitsa ngakhale pang’ono, kungawonjezere kupanikizika kwanu?

▪ Kodi mungalankhule ndi ndani ngati mukuona kuti mwapanikizika kwambiri?

[Chithunzi patsamba 27]

Kulimbana ndi kupanikizika kuli ngati kunyamula zitsulo. Kungakuthandizeni kukhala wamphamvu ngati mudziwa mochitira